Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Buku lothandiza pophunzira Baibuloli, linakonzedwa kuti likuthandizeni kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani zosiyanasiyana, monga chifukwa chake timavutika, zimene zimachitika munthu akamwalira, mmene tingakhalire ndi banja losangalala ndi zina zambiri.

Kodi Mulungu Anali ndi Cholinga Chotani Polenga Anthu?

N’kutheka kuti mumadabwa kuti n’chifukwa chiyani panopa m’dzikoli muli mavuto ambiri. Baibulo limaphunzitsa kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa mavuto onse monga matenda komanso imfa.

MUTU 1

Kodi Mukudziwa Zotani Zokhudza Mulungu?

Kodi Mulungu amakuganiziranidi? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe makhalidwe ake ndiponso zimene mungachite kuti mukhale naye pa ubwenzi.

MUTU 2

Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu

Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kupirira mavuto anu? N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira maulosi ake?

MUTU 3

Kodi Mulungu Analenga Anthu Chifukwa Chiyani?

Kodi moyo udzakhala wotani m’tsogolo dzikoli likadzakhala paradaiso?

MUTU 4

Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Yesu ali Mesiya, kumene anachokera komanso chifukwa chimene alili mwana wapadera wa Yehova.

MUTU 5

Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa

Kodi dipo la Yesu n’chiyani? Kodi lingakuthandizeni bwanji?

MUTU 6

Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?

Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kumene munthu amapita akamwalira komanso kuti mudziwe kuti n’chifukwa chiyani timafa.

MUTU 7

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo

Kodi wachibale kapena mnzanu anamwalira? Kodi n’zotheka kudzaonana nayenso? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limaphunzitsa.

MUTU 8

Kodi Ufumu Wa Mulungu N’chiyani?

Anthu ambiri amadziwa Pemphero la Ambuye. Kodi mawu oti “Ufumu wanu ubwere” amatanthauza chiyani?

MUTU 9

Kodi Dzikoli Lithadi Posachedwa?

Zochita za anthu komanso maganizo awo, zikusonyezeratu kuti tikukhala m’nthawi imene Mulungu watsala pang’ono kuwononga dziko lapansili, monga mmene Baibulo linaneneratu.

MUTU 10

Zimene Tiyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Baibulo limafotokoza nkhani zokhudza angelo komanso ziwanda. Kodi kulidi angelo ndi ziwanda? Kodi angatithandize kapena kutivulaza?

MUTU 11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu ndi amene akuchititsa mavuto amene akuchitika pa dzikoli. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Onani chifukwa chimene Mulungu amatiuza kuti n’chimene chikuchititsa kuti anthu azivutika.

MUTU 12

Kodi Mungatani Kuti Mulungu Akhale Mnzanu?

N’zotheka kumachita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo. Ndipo mukhoza kukhala naye pa ubwenzi.

MUTU 13

Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali

Kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani yochotsa mimba, kuikidwa magazi, komanso moyo wa zinyama?

MUTU 14

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala

Yesu ankakonda kwambiri anthu ndipo zimenezi ndi chitsanzo chabwino kwa amuna okwatira, akazi okwatiwa, makolo komanso ana. Kodi tingamutsanzire bwanji?

MUTU 15

Njira Yoyenera Yolambirira Mulungu

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe kuti ndi chipembedzo chiti chomwe chimalambira Mulungu m’njira yoyenera.

MUTU 16

Khalani ndi Cholinga Choti Muzilambira Mulungu

Kodi ndi mavuto otani amene mungakumane nawo pamene mukuyesa kufotokozera ena zimene mumakhulupirira? Ndipo mungawafotokozere bwanji m’njira yoti musawakhumudwitse?

MUTU 17

Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu

Kodi Mulungu amamvetsera mapemphero anthu? Kuti mudziwe yankho la funso limeneli, muyenera kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya pemphero.

MUTU 18

Kodi Ndidzipereke kwa Yehova Ndiponso Kubatizidwa?

Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti ayenerere kubatizidwa? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe kuti kubatizidwa kumatanthauza chiyani komanso kuti kuyenera kuchitika bwanji.

MUTU 19

Musasiyane ndi Yehova

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu komanso timayamikira zonse zimene amatichitira?

Mawu Akumapeto

Matanthauzo a mawu amene agwiritsidwa ntchito m’buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa