Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 16

Khalani ndi Cholinga Choti Muzilambira Mulungu

Khalani ndi Cholinga Choti Muzilambira Mulungu

1, 2. Kodi ndi funso liti limene muyenera kudzifunsa, ndipo n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika?

PA NTHAWI imene mwakhala mukuphunzira Baibulo, mwaona kuti anthu ambiri amene amati amalambira Mulungu, amaphunzitsa komanso kuchita zinthu zimene Mulunguyo amadana nazo. (2 Akorinto 6:17) N’chifukwa chake Yehova akutilamula kuti tiyenera kutuluka mu “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:2, 4) Kodi inuyo mumvera lamulo limeneli? Aliyense ayenera kusankha zochita pa nkhaniyi. Tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenera kumatumikira Mulungu m’njira imene iyeyo amaivomereza kapena ndizingomutumikira mulimonse mmene ineyo ndikufunira?’

2 Ngati munasiya kupita kuchipembedzo chonyenga kapena munalemba kalata yofotokoza kuti mwachoka m’chipembedzocho, munachita bwino kwambiri. Koma n’kutheka kuti pali miyambo inayake ya kuchipembedzo chonyenga imene imakusangalatsanibe. Tiyeni tikambirane ina mwa miyambo imeneyi kuti tione chifukwa chake tiyenera kumaiona ngati mmene Yehova amaionera.

KULAMBIRA MAFANO NDIPONSO MIZIMU YA MAKOLO

3. (a) N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kwa ena kuti asiye kugwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu? (b) Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

3 Anthu ena akhala akusunga mafano kapena zinthu zina m’nyumba zawo kwa zaka zambiri n’kumazigwiritsa ntchito polambira Mulungu. Ngati nanunso mwakhala mukuchita zimenezi, zikhoza kukhala zovuta komanso zachilendo kuyamba kulambira Mulungu popanda kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi. Koma kumbukirani kuti Yehova amatiphunzitsa njira  yoyenera yomulambirira. Ndiponso Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Yehova safuna kuti tizigwiritsa ntchito mafano pomulambira.—Werengani Ekisodo 20:4, 5; Salimo 115:4-8; Yesaya 42:8; 1 Yohane 5:21.

4. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kulambira mizimu ya makolo? (b) N’chifukwa chiyani Yehova analetsa anthu ake kuti asamayese kulankhula ndi anthu amene anamwalira?

4 Anthu ena amagwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zawo pochita zinthu zimene amaganiza kuti zingasangalatse mizimu ya makolo awo amene anamwalira. Anthu amenewa amathanso kulambira mizimu ya makolo awoyo. Koma taphunzira kuti anthu amene anamwalira sangatithandize kapena kutivulaza. Munthu akamwalira sakhalanso ndi moyo kwinakwake. Ndipotu kuyesa kulankhula ndi anthu amene anamwalira n’koopsa chifukwa uthenga uliwonse wooneka ngati wachokera kwa wachibale amene anamwalira umakhala ukuchokera kwa ziwanda. N’chifukwa chake Yehova analamula Aisiraeli kuti asamayese kulankhulana ndi anthu amene anamwalira kapena kuchita zilizonse zokhudzana ndi mizimu.—Deuteronomo 18:10-12; onani Mawu Akumapeto 26 ndi 31

5. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musiye kugwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu ndiponso kuti musiye kulambira mizimu ya makolo?

5 Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musiye kugwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu kapena kuti musiye kulambira mizimu ya makolo? Muyenera kumawerenga Baibulo ndiponso kuganizira mofatsa mmene Yehova amaonera zinthuzo. Iye amaona kuti zinthu zimenezi ndi ‘zonyansa.’ (Deuteronomo 27:15) Muzipemphera kwa Yehova tsiku lililonse kumupempha kuti akuthandizeni kumaona zinthu mmene iyeyo amazionera ndiponso kuti akuthandizeni kumamulambira m’njira imene amafuna. (Yesaya 55:9) Simuyenera kukayikira kuti Yehova adzakupatsani mphamvu kuti muthe kusiyiratu chilichonse chokhudzana ndi kulambira konyenga.

KODI TIYENERA KUMACHITA NAWO KHIRISIMASI?

6. Kodi n’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo anasankha zoti azikondwerera kubadwa kwa Yesu pa 25 December?

6 Khirisimasi ndi imodzi mwa maholide otchuka kwambiri  padziko lonse lapansi ndipo anthu ambiri amanena kuti patsikuli amakondwerera kubadwa kwa Yesu. Komatu Khirisimasi inachokera kuchipembedzo chonyenga. Buku lina limafotokoza kuti anthu a ku Roma ankakondwerera kubadwa kwa dzuwa pa 25 December. Atsogoleri amatchalitchi ankafuna kuti anthu ambiri achikunja ayambe Chikhristu, ndiye ngakhale kuti Yesu sanabadwe pa 25 December, iwo anasankha kuti azikondwerera kubadwa kwa Yesu patsiku limeneli. (Luka 2:8-12) Ophunzira a Yesu sankachita Khirisimasi. Buku lina limanena kuti kwa zaka 200 Yesu atabadwa, “palibe amene ankadziwa tsiku lenileni limene iye anabadwa, ndipo zoti Yesu anabadwa liti ambiri analibe nazo ntchito.” (Sacred Origins of Profound Things) Mwambo wa Khirisimasi unayamba patadutsa zaka mahandiredi ambiri Yesu atabwerera kumwamba.

7. N’chifukwa chiyani Akhristu oona sachita nawo Khirisimasi?

7 Anthu ambiri amadziwa zoti Khirisimasi ndiponso miyambo imene imachitika patsikuli zinachokera kuchipembedzo chonyenga. Miyambo imeneyi ndi monga kupatsana mphatso komanso kuchita phwando. Mwachitsanzo, kale ku England ndiponso mayiko ena a ku America, malamulo ankaletsa anthu kuchita Khirisimasi chifukwa chakuti ndi mwambo wochokera kuchipembedzo chonyenga. Aliyense amene ankachita Khirisimasi ankalandira chilango. Koma pang’ono ndi pang’ono anthu m’mayikowa anayamba kuchita nawo Khirisimasi. Koma Akhristu oona sachita nawo Khirisimasi chifukwa nthawi zonse amafuna kuchita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo.

KODI TIYENERA KUMAKONDWERERA TSIKU LIMENE TINABADWA?

8, 9. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu oyambirira sankakondwerera masiku amene anabadwa?

8 Anthu ambiri amakondanso kukondwerera tsiku limene anabadwa. Kodi Akhristu ayenera kumakondwerera tsiku limene anabadwa? Zikondwerero zokumbukira tsiku lobadwa  zimene zimatchulidwa m’Baibulo ndi za anthu omwe sankalambira Yehova. (Genesis 40:20; Maliko 6:21) Anthu ankakondwerera tsiku limene anabadwa pofuna kupereka ulemu kwa milungu yonyenga. N’chifukwa chake Akhristu oyambirira “ankaona kuti kukondwerera tsiku limene munthu anabadwa ndi mwambo wachikunja.”—The World Book Encyclopedia.

9 Aroma komanso Agiriki ankakhulupirira kuti pa nthawi imene munthu aliyense akubadwa pankabwera mzimu winawake ndipo mzimuwo unkamuyang’anira munthuyo moyo wake wonse. Buku lina linafotokoza kuti: “Mzimu umenewu unkakhala pachibale ndi mulungu amene anabadwanso pa tsiku ngati lomwelo.”—The Lore of Birthdays.

10. N’chifukwa chiyani Akhristu masiku ano sakondwerera tsiku limene munthu anabadwa?

10 Kodi inuyo mumaona kuti Yehova amasangalala ndi zikondwerero zokhudzana ndi kulambira konyenga? (Yesaya 65:11, 12) Ayi, sasangalala nazo. N’chifukwa chake sitikondwerera tsiku limene tinabadwa kapena holide iliyonse yogwirizana ndi kulambira konyenga.

KODI PALI VUTO NDI MMENE ZINAYAMBIRA?

11. Kodi anthu ena amachita nawo maholide chifukwa chiyani? Koma kodi chinthu chofunika kwambiri kwa inuyo chiyenera kukhala chiyani?

11 Anthu ena amakondwererabe Khirisimasi komanso maholide ena ngakhale kuti amadziwa zoti maholide amenewa anachokera kuchipembedzo chonyenga. Iwo amaona kuti maholidewa amawapatsa mpata wocheza ndi mabanja awo. Kodi nanunso mumaona choncho? Sikulakwa kufuna kukhala ndi nthawi yocheza ndi banja lanu. Yehova ndi amene anayambitsa banja ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi achibale athu. (Aefeso 3:14, 15) Komabe tiyenera kuona kuti chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova m’malo mosangalatsa achibale athu pochita zikondwerero zomwe n’zochokera kuchipembedzo chonyenga. N’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena kuti: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.”—Aefeso 5:10.

12. Kodi n’chiyani chingachititse kuti holide inayake ikhale yosakondweretsa Yehova?

 12 Anthu ambiri amaona kuti zilibe vuto kuti mwambo winawake unayamba bwanji, komatu Yehova saona choncho. Iye sasangalala ndi maholide amene anachokera kuchipembedzo chonyenga kapena omwe cholinga chake ndi kutamanda anthu kapena zizindikiro za mayiko. Mwachitsanzo, Aiguputo ankachita zikondwerero zosiyanasiyana polambira milungu yawo yonyenga. Aisiraeli atachoka ku Iguputo, anatengera mwambo wina wachikunja wa Aiguputowo ndipo anaupatsa dzina loti “chikondwerero cha Yehova.” Koma Yehova anawalanga chifukwa chochita zimenezi. (Ekisodo 32:2-10) Mogwirizana ndi malangizo amene Yesaya ananena, sitiyenera kukhudza “chinthu chilichonse chodetsedwa.”—Werengani Yesaya 52:11.

MUZICHITA ZINTHU MOSAMALA

13. Kodi anthu amene asiya kuchita nawo maholide ena amakhala ndi mafunso otani?

13 Ngati mwasiya kuchita nawo maholide amenewa, n’kutheka kuti mudakali ndi mafunso ambiri m’maganizo mwanu. Mwachitsanzo, mwina mumadzifunsa kuti: Kodi ndingatani ngati anzanga akuntchito atandifunsa chifukwa chimene sindikondwerera nawo Khirisimasi? Kodi ndingachite chiyani ngati wina atandipatsa mphatso ya Khirisimasi? Nanga ndingatani ngati mwamuna kapena mkazi wanga akufuna kuti ndichite nawo mwambo wa holide inayake? Kodi ndiyenera kuchita chiyani kuti ana anga asamaone ngati akumanidwa zinazake chifukwa choti sachita nawo maholide komanso kukondwerera tsiku limene anabadwa?

14, 15. Kodi mungatani ngati munthu wina atakufunirani mafuno abwino a holide inayake kapena kukupatsani mphatso?

14 Ngati tafunsidwa funso kapena ngati winawake atatipempha kuti tichite nawo zinazake tingaone mmene tingayankhire mogwirizana ndi mmene zinthu zilili. Mwachitsanzo, ngati anthu ena atakufunirani mafuno abwino a holide inayake, si bwino kungowanyalanyaza. Mukhoza kungowauza kuti, “Zikomo kwambiri.” Koma ngati munthu wina akufuna kudziwa zambiri, mungamufotokozere chifukwa chimene simukondwerera  nawo holideyo. Komabe, nthawi zonse muyenera kufotokoza mokoma mtima, mwaluso komanso mwaulemu. Baibulo limati: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akolose 4:6) Mwina mungawafotokozere kuti mumakonda kucheza ndi ena komanso kupereka mphatso kwa anthu koma kungoti mungakonde kuchita zimenezi pa nthawi ina osati nthawi ya maholide.

15 Koma kodi mungatani ngati wina atakupatsani mphatso? Baibulo lilibe mndandanda wa malamulo oti munthu azitsatira pa nkhani iliyonse, koma limatiuza kuti tiyenera kuchita zinthu zimene zingatithandize kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino. (1 Timoteyo 1:18, 19) N’kutheka kuti munthu amene akukupatsani mphatsoyo sakudziwa kuti simukondwerera nawo holideyo. Kapena akhoza kunena kuti, “Ndikudziwa kuti simukondwerera holideyi, koma ndangofuna kukupatsanibe mphatsoyi.” Pa zochitika ziwiri zonsezi, mungasankhe kulandira mphatsoyo kapena ayi. Komabe muyenera kuonetsetsa kuti mwasankha zinthu zimene sizingakupangitseni kuti muzidziimba mlandu. Sitikuyenera kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.

MUZICHITA ZINTHU MWAULEMU NDI ACHIBALE ANU

Anthu amene amatumikira Yehova amakhala osangalala

16. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati achibale anu akufuna kukondwerera holide inayake?

16 Kodi mungatani ngati achibale anu akufuna kuchita chikondwerero chinachake? Simukufunika kulimbana nawo. Kumbukirani kuti ali ndi ufulu wochita zimene akufuna. Muyenera kuwaganizira komanso kuwapatsa ulemu pa zimene asankha, monga mmene inunso mumafunira kuti azilemekeza zimene mwasankha. (Werengani Mateyu 7:12.) Koma nanga bwanji ngati achibale anuwo akufuna kuti nanunso mukakhale nawo pachikondwererocho? Musanasankhe chochita, muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru. Muyenera kuganizira komanso kufufuza mokwanira zimene zikachitike pachikondwererocho.  Muzikumbukira kuti nthawi zonse mumafunika kusankha zinthu zokondweretsa Yehova.

17. Kodi mungatani kuti ana anu asamasirire akaona ena akuchita zikondwerero zosiyanasiyana?

17 Kodi mungatani kuti ana anu asamasirire akaona ena akuchita zikondwerero zosiyanasiyana? Muyenera kumawakonzera nthawi yosangalala pafupipafupi. Muyeneranso kumawagulira mphatso zosiyanasiyana ngakhale pa nthawi imene sakuyembekezera. Ndipo ngati mutamapatula nthawi yocheza nawo komanso kuwasonyeza chikondi ingakhale mphatso yabwino kwambiri kuposa mphatso iliyonse.

MUZILAMBIRA MULUNGU M’NJIRA YOYENERA

18. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumapezeka pamisonkhano yachikhristu?

18 Kuti tisangalatse Yehova, tiyenera kutuluka m’chipembedzo chonyenga komanso kusiya miyambo yonse ya kuchipembedzocho. Tiyeneranso kumachita zinthu zimene anthu amene ali m’chipembedzo choona amayenera kuchita. Kodi zinthu zake ndi ziti? Chinthu chimodzi ndi kupezeka pamisonkhano yachikhristu nthawi zonse. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Misonkhano ndi yofunika kwambiri kwa anthu amene ali m’chipembedzo choona. (Salimo 22:22; 122:1) Tikasonkhana timatha kulimbikitsana.—Aroma 1:12.

19. Kodi n’chifukwa chiyani muyenera kuuza anthu ena zinthu zimene mwaphunzira m’Baibulo?

19 Chinthu china chofunika ndi kuuza ena zinthu zimene mwaphunzira m’Baibulo. Anthu ambiri amakhala osasangalala chifukwa cha zinthu zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli. N’kutheka kuti inuyo mukudziwapo anthu ena amene zoterezi zikuwachitikira. Muyenera kuwauza zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezera kutsogoloku. Mukamayesetsa kupezeka pamisonkhano yachikhristu ndiponso kuuza anthu ena uthenga wa m’Baibulo, mudzasiya kulakalaka kuchita nawo miyambo komanso zinthu zina za kuchipembedzo chonyenga. Dziwani kuti mukamachita zimenezi mudzasangalala kwambiri komanso Yehova adzakudalitsani chifukwa chosankha kumulambira m’njira yoyenera.—Malaki 3:10.