Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 12

Kodi Mungatani Kuti Mulungu Akhale Mnzanu?

Kodi Mungatani Kuti Mulungu Akhale Mnzanu?

1, 2. Tchulani mayina a anthu ena amene Yehova ankawaona ngati anzake.

KODI ndi munthu wotani amene mungakonde atakhala mnzanu? N’zosakayikitsa kuti mungakonde munthu amene zochita zake zimakusangalatsani, amene mukhoza kumachita naye zinthu mosavuta komanso yemwe ali ndi makhalidwe abwino amene inuyo mumawasirira.

2 Yehova amasankha anthu ena kuti akhale anzake. Mwachitsanzo, Abulahamu anali mmodzi wa anthu amene anali anzake a Yehova. (Yesaya 41:8; Yakobo 2:23) Yehova ankakondanso Davide. Pa nthawi ina ananena kuti Davide anali ‘munthu wapamtima pake.’ (Machitidwe 13:22) Nayenso mneneri Danieli anali “munthu wokondedwa kwambiri” ndi Yehova.—Danieli 9:23.

3. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha Abulahamu, Davide ndi Danieli kuti akhale anzake?

3 Koma kodi n’chiyani chimene chinapangitsa kuti Abulahamu, Davide, komanso Danieli akhale anzake a Yehova? Yehova anauza Abulahamu kuti: “Wamvera mawu anga.” (Genesis 22:18) Yehova amagwirizana ndi anthu amene amamumvera modzichepetsa. N’zothekanso mtundu wonse wa anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Iye anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Muzimvera mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.” (Yeremiya 7:23) Choncho inunso muyenera kumvera Yehova ngati mukufunadi kuti iye akhale mnzanu.

YEHOVA AMATETEZA ANTHU AMENE ALI NAYE PA UBWENZI

4, 5. Kodi Yehova amateteza bwanji anthu omwe ndi anzake?

4 Baibulo limanena kuti Yehova amafufuza njira zoti “aonetse  mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Palemba la Salimo 32:8, Yehova analonjeza anthu amene ndi anzake kuti: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”

5 Pali mdani wathu yemwe ndi wamphamvu kwambiri amene akufuna kutilepheretsa kuti Mulungu akhale mnzathu. Koma Yehova akufunitsitsa kutiteteza. (Werengani Salimo 55:22.) Timatumikira Yehova ndi mtima wathu wonse chifukwa chakuti iye ndi mnzathu. Timakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto. Ndipo nafenso timanena motsimikiza mawu amene wolemba masalimo wina ananena. Ponena za Yehova, iye analemba kuti: “Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Salimo 16:8; 63:8) Koma kodi Satana amachita chiyani pofuna kuti Mulungu asakhale mnzathu?

ZIMENE SATANA ANANENA

6. Kodi Satana amanena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa chiyani?

6 M’Mutu 11 tinaphunzira kuti Satana anatsutsa ulamuliro wa Yehova ndipo ananenanso kuti Yehovayo ndi wabodza komanso wopanda chilungamo. Iye ananena kuti zikanakhala bwino kwambiri ngati Yehova akanapatsa Adamu ndi Hava mwayi woti azisankha okha zinthu zimene akuona kuti ndi zabwino kapena zoipa. Buku la Yobu limafotokoza kuti Satana amanena zoipa zokhudza anthu amene amayesetsa kuchita zinthu zoti Mulungu akhale mnzawo. Iye amanena kuti anthu amene amatumikira Mulungu amachita zimenezi chifukwa chofuna kupezapo kenakake osati chifukwa choti amakonda Mulunguyo. Satana ananenanso kuti akhoza kuchititsa munthu aliyense kuti asiye kumvera Mulungu. Tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire kwa Yobu komanso mmene Yehova anamutetezera.

7, 8. (a) Kodi Yehova ankamuona bwanji Yobu? (b) Kodi Satana ananena kuti Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha chiyani?

7 Kodi Yobu anali ndani? Iye anali munthu wabwino  kwambiri amene anakhala padzikoli zaka 3,600 zapitazo. Yehova ananena kuti pa nthawiyo panalibenso munthu wina wofanana naye padziko lapansili. Yobu ankalemekeza kwambiri Mulungu ndiponso ankadana ndi zinthu zoipa. (Yobu 1:8) Zimenezi zinachititsa kuti akhale mnzake weniweni wa Yehova.

8 Satana ananena kuti Yobu ankatumikira Yehova pa zifukwa zadyera. Iye anauza Yehova kuti: “Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo? Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. Mwadalitsa ntchito ya manja ake ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri padziko lapansi. Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”—Yobu 1:10, 11.

9. Kodi Yehova analoleza Satana kuchita chiyani?

9 Pamenepatu Satana ankatanthauza kuti Yobu ankatumikira Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene ankamupatsa. Satana ananenanso kuti akanatha kuchititsa Yobu kuti asiye kutumikira Yehova. Koma Yehova anatsutsa zimenezi, ndipo analola kuti Satana ayese Yobu n’cholinga choti zidziwike ngati Yobuyo ankatumikira Yehova chifukwa chomukonda kapena ayi.

MMENE SATANA ANAZUNZIRA YOBU

10. Kodi Satana anayesa bwanji Yobu, nanga Yobuyo anachita zotani?

10 Choyamba, Satana anachititsa kuti ziweto za Yobu zibedwe ndipo zimene zinatsala zinaphedwa. Kenako Satana anapha antchito ambiri a Yobu ndipo zotsatira zake zinali zakuti iye anakhala wopanda chilichonse. Pomaliza, Satana anapha ana a Yobu okwana 10 ndi mphepo yamkuntho. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto onsewa, Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Baibulo limanena kuti: “M’zonsezi Yobu sanachimwe, kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.”—Yobu 1:12-19, 22.

Yehova anadalitsa Yobu chifukwa anali wokhulupirika

11. (a) Kodi Satana anamuchitiranso chiyani Yobu? (b) Nanga kodi Yobu ananena kuti chiyani?

11 Satana sanasiyire pomwepo. Iye anauza Mulungu kuti:  ‘Khudzani mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!’ Choncho Satana anachititsa kuti Yobu adwale matenda opweteka kwambiri. (Yobu 2:5, 7) Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Iye anati: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.

12. Kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti Satana ndi wabodza?

12 Koma Yobu sankadziwa zimene Satana ananena zokhudza iyeyo komanso chimene chinachititsa kuti akumane ndi mavuto ambirimbiri. Iye anayamba kuganiza kuti Mulungu ndi amene ankachititsa kuti iye azikumana ndi mavuto. (Yobu 6:4; 16:11-14) Komabe, iye anapitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika. Apa zinaonekeratu kuti zimene Satana ananena zoti Yobu ankatumikira Mulungu pa zifukwa zadyera zinali zabodza. Zinasonyeza kuti Yobu ankatumikira Yehova chifukwa chomukonda.

13. Kodi Yehova anamuchitira chiyani Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake?

13 Ngakhale kuti Yobu sankadziwa zimene zinali kuchitika kumwambazi, iye anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ndipo zinadziwika kuti Satana ndi woipa kwambiri. Yehova anadalitsa Yobu chifukwa chokhalabe wokhulupirika.—Yobu 42:12-17.

ZIMENE SATANA AMAKUNENANI

14, 15. Kodi Satana ananena zotani zomwe zimakhudza anthu onse?

14 Mukhoza kuphunzira zinthu zambiri kuchokera pa zimene zinachitikira Yobu. Masiku ano, Satana amanena kuti timangotumikira Mulungu n’cholinga choti atipatse zinazake. Pa Yobu 2:4, Satana ananena kuti: “Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Satana amanena kuti anthu onse ndi adyera, osati Yobu yekha. Patapita zaka zambirimbiri Yobu atamwalira, Satana ankanyozabe Yehova komanso atumiki ake. Mwachitsanzo, pa Miyambo 27:11, timawerenga kuti: “Mwana wanga, khala wanzeru  ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza [kapena kuti, kundinyoza].”

15 Muli ndi ufulu wosankha kumvera Yehova zomwe zingathandize kuti mukhale mnzake komanso kusonyeza kuti Satana ndi wabodza. Ngakhale zitakhala kuti pali zinthu zambiri zimene mukufunika kusintha kuti Mulungu ayambe kukuonani ngati mnzake, kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri. Kusankha kukhala mnzake wa Mulungu si nkhani yaing’ono. Satana amanena kuti inuyo simungakhale wokhulupirika kwa Mulungu ngati mutakumana ndi mavuto. Iye amayesetsa kutipusitsa kuti tisamachite zimene Mulungu amafuna. Kodi amachita zimenezi motani?

16. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira ziti kuti alepheretse anthu kutumikira Yehova? (b) Kodi mukuganiza kuti Mdyerekezi angagwiritse ntchito njira ziti kuti akulepheretseni inuyo kutumikira Yehova?

16 Satana amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana n’cholinga choti atisokoneze kuti tisakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Iye amatha kutiukira “ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) Choncho musamadabwe ngati anzanu, abale anu, kapena anthu ena atayesetsa kuti musiye kuphunzira Baibulo ndiponso kuti musiye kuchita zinthu zoyenera. Zimenezi zingakupangitseni kuona kuti mukuzunzika. * (Yohane 15:19, 20) Nthawi zinanso Satana amadzisintha kuti azioneka ngati “mngelo wa kuwala.” Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, akhoza kutipusitsa kuti tisiye kumvera Yehova. (2 Akorinto 11:14) Njira inanso imene Satana amagwiritsa ntchito kuti tisiye kutumikira Yehova ndi kutipangitsa kuti tiziona kuti ndife achabechabe moti sitingakhale atumiki a Mulungu.—Miyambo 24:10.

MUZIMVERA MALAMULO A YEHOVA

17. Kodi timamvera Yehova chifukwa chiyani?

17 Tikamamvera Yehova timakhala tikusonyeza kuti Satana  ndi wabodza. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kukhala anthu omvera? Baibulo limanena kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.” (Deuteronomo 6:5) Timamvera Yehova chifukwa chakuti timamukonda. Chikondi chimenechi chikamakula, tidzafunitsitsa kuchita chilichonse chimene iye angafune. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3.

18, 19. (a) Kodi zina mwa zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zoipa ndi ziti? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova satiuza kuchita zinthu zoti sitingakwanitse?

18 Komano kodi zina mwa zinthu zimene Yehova amatiuza kuti n’zoipa ndi ziti? Zitsanzo zina zili m’bokosi lakuti, “ Muzidana ndi Zinthu Zimene Yehova Amadana Nazo.” Poyamba mukhoza kuona ngati kuti zinthu zinazo si zoipa kwenikweni. Koma mukawerenga mavesi a m’Baibulo n’kuwaganizira mofatsa, mungathe kuona kuti ndi nzeru kutsatira malamulo a Yehova. Mungathenso kuona kuti pali makhalidwe ena amene mukufunika kusintha. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kumakhala  kovuta nthawi zina, kusintha makhalidwe anu kungakuthandizeni kuti muzikhala wosangalala ndiponso kuti muzikhala ndi mtendere mumtima, zomwe zimatheka chifukwa choti muli pa ubwenzi ndi Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Kodi tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kusintha makhalidwe athu?

19 Yehova satipempha kuti tichite zinthu zomwe sitingathe. (Deuteronomo 30:11-14) Monga mnzathu weniweni, amatidziwa bwino kuposa mmene ifeyo timadzidziwira. Amadziwa zinthu zomwe tingakwanitse komanso zimene sitingakwanitse. (Salimo 103:14) Mtumwi Paulo ananena mfundo yolimbikitsa yakuti: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” (1 Akorinto 10:13) Tizikhulupirira kuti nthawi zonse Yehova adzatipatsa mphamvu zotithandiza kuchita zinthu zoyenera. Adzakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti ikuthandizeni kupirira mavuto. (2 Akorinto 4:7) Paulo atathandizidwa ndi Yehova pa mavuto osiyanasiyana, ananena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza  mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

MUZIKONDA ZIMENE MULUNGU AMAKONDA

20. Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene muyenera kutsanzira, ndipo n’chifukwa chiyani?

20 Ngati tikufuna kuti Yehova akhale mnzathu, tikuyenera kusiya kuchita zinthu zimene amatiuza kuti ndi zoipa. Koma palinso zina zimene tiyenera kuchita. (Aroma 12:9) Anthu amene ndi anzake a Mulungu amakonda zinthu zimene Mulunguyo amakonda. Anthu amenewa akufotokozedwa pa lemba la Salimo 15:1-5. (Werengani.) Anzake a Yehova amayesetsa kutsanzira makhalidwe ake ndipo amasonyeza “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”—Agalatiya 5:22, 23.

21. Kodi mungatani kuti muzisonyeza makhalidwe amene Mulungu amakonda?

21 Kodi mungatani kuti muzisonyeza makhalidwe abwino kwambiri amenewa pochita zinthu? Muyenera kumawerenga komanso kuphunzira Baibulo nthawi zonse n’cholinga choti mudziwe zinthu zimene Yehova amakonda. (Yesaya 30:20, 21) Mukamachita zimenezi, mudzayamba kukonda kwambiri Yehova komanso zidzakuchititsani kuti muzimumvera.

22. Kodi chingachitike n’chiyani mukamachita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo?

22 Kusintha kumene mungachite kuti mukhale ndi makhalidwe abwino tingakuyerekezere ndi kuvula zovala zakale n’kuvala zatsopano. Baibulo limanena kuti muyenera ‘kuvula umunthu wakale’ n’kuvala “umunthu watsopano.” (Akolose 3:9, 10) Ngakhale kuti kuchita zimenezi sikophweka, tikayesetsa kusintha makhalidwe athu n’kuyamba kumvera Yehova, iye amatilonjeza kutipatsa “mphoto yaikulu.” (Salimo 19:11) Mukamamvera ndi kutsatira zimene Yehova amanena, mudzasonyeza kuti zimene Satana ananena ndi zabodza. Muzitumikira Yehova chifukwa chakuti mumamukonda, osati chifukwa cha zinthu zimene walonjeza kuti adzachitira anthu m’tsogolo. Mukachita zimenezi, mudzakhala mnzake weniweni wa Mulungu.

^ ndime 16 Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu amene amafuna kuti musiye kuphunzira Baibulo ndiye kuti akulamuliridwa ndi Satana. Komano Satana ndi “mulungu wa nthawi ino” ndipo “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Choncho n’zosadabwitsa kuona anthu ena akuyesetsa kutilepheretsa kutumikira Yehova.—2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19.