Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 18

Kodi Ndidzipereke kwa Yehova Ndiponso Kubatizidwa?

Kodi Ndidzipereke kwa Yehova Ndiponso Kubatizidwa?

1. Kodi mungadzifunse funso liti pambuyo poti mwakhala mukuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito bukuli?

KUPHUNZIRA Baibulo pogwiritsa ntchito bukuli kwakuthandizani kudziwa zinthu zosiyanasiyana monga lonjezo la Mulungu la moyo wosatha, mmene akufa alili komanso zoti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. (Mlaliki 9:5; Luka 23:43; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) N’kutheka kuti munayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo munaona kuti iwo amalambira Mulungu m’njira yolondola. (Yohane 13:35) Mwinanso mwayamba kale kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndipo mukufuna  kuyamba kumutumikira. Komabe mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizitumikira Mulungu?’

2. Kodi n’chifukwa chiyani munthu wina wa ku Itiyopiya anapempha kuti abatizidwe?

2 Funso lofanana ndi limeneli ndi lomwe munthu wina wa ku Itiyopiya anali nalo. Munthu ameneyu analalikidwa ndi wophunzira wina wa Yesu dzina lake Filipo patapita zaka zingapo Yesu ataukitsidwa. Filipo anathandiza munthuyo kudziwa kuti Yesu anali Mesiya. Munthu wa ku Itiyopiyayo anasangalala kwambiri ndi zimene anaphunzira moti nthawi yomweyo ananena kuti: “Taonani! Si awa madzi ambiri. Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?”—Machitidwe 8:26-36.

3. (a) Kodi Yesu analamula otsatira ake kuti azichita chiyani? (b) Kodi munthu ayenera kubatizidwa motani?

3 Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti ngati mukufuna kuti muzitumikira Yehova, muyenera kubatizidwa. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. [Ndipo] muziwabatiza.” (Mateyu 28:19) Yesu anapereka chitsanzo pa nkhaniyi chifukwa nayenso anabatizidwa. Pamene ankabatizidwa, anaviikidwa thupi lonse, osati kungomuwaza madzi pamutu. (Mateyu 3:16) Masiku anonso Mkhristu akamabatizidwa amayenera kuviikidwa thupi lonse m’madzi.

4. Kodi ubatizo umasonyeza chiyani?

4 Mukabatizidwa mumasonyeza anthu ena kuti mukufunitsitsa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndiponso kumutumikira. (Salimo 40:7, 8) Komabe mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenera kuchita chiyani kuti ndibatizidwe?’

MUYENERA KUDZIWA ZOLONDOLA KOMANSO KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO

5. (a) Kodi ndi chinthu choyamba chiti chimene mufunika kuchita kuti muyenerere kubatizidwa? (b) Kodi misonkhano yachikhristu ndi yofunika bwanji?

5 Musanabatizidwe, muyenera kudziwa Yehova komanso  Yesu. Munayamba kale kuchita zimenezi pamene munayamba kuphunzira Baibulo. (Werengani Yohane 17:3.) Koma kungodziwa Yehova ndi Yesu sikokwanira. Baibulo limanena kuti muyenera ‘kudziwa molondola’ chifuniro cha Yehova. (Akolose 1:9) Kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova kungakuthandizeni kuti mumudziwe bwino Yehova. N’chifukwa chake muyenera kumapezeka pamisonkhano imeneyi nthawi zonse.—Aheberi 10:24, 25.

Muyenera kuphunzira kaye Baibulo, musanabatizidwe

6. Kodi muyenera kudziwa mfundo za m’Baibulo zochuluka bwanji kuti muyenerere kubatizidwa?

6 Komabe, sikuti Yehova amayembekezera kuti musanabatizidwe mukhale mutadziwa zonse zimene zili m’Baibulo. Iye sanayembekezere kuti munthu wa ku Itiyopiya uja adziwe zonse asanabatizidwe. (Machitidwe 8:30, 31) Ndipotu tidzapitirizabe kuphunzira za Mulungu mpaka kalekale. (Mlaliki 3:11) Komabe, kuti mubatizidwe muyenera kudziwa ndiponso kuyamba kukhulupirira mfundo zoyambirira za m’Baibulo.—Aheberi 5:12.

7. Kodi kuphunzira Baibulo kwakuthandizani bwanji?

7 Baibulo limanena kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Muyenera kukhala ndi chikhulupiriro musanabatizidwe. Baibulo limatiuza kuti anthu ena a mumzinda wa Korinto anamva zimene ophunzira a Yesu ankaphunzitsa ndipo “anayamba kukhulupirira ndi kubatizidwa.” (Machitidwe 18:8) Mofanana ndi anthu amenewa, kuphunzira Baibulo kumene mwakhala mukuchita kwakuthandizani kuti muzikhulupirira zimene Mulungu analonjeza ndiponso kuti muzikhulupirira nsembe ya Yesu imene ingatipulumutse ku uchimo ndi imfa.—Yoswa 23:14; Machitidwe 4:12; 2 Timoteyo 3:16, 17.

MUZIUZA ENA ZIMENE BAIBULO LIMANENA

8. Kodi n’chiyani chingakuchititseni kuti muziuza ena zimene mumaphunzira?

8 Mukapitiriza kuphunzira Baibulo ndiponso kuona  mmene likukuthandizirani pa moyo wanu, chikhulupiriro chanu chidzayamba kukula. Mudzayamba kufuna kuuza ena zimene mukuphunzira. (Yeremiya 20:9; 2 Akorinto 4:13) Koma kodi mungayambe ndi kuuza ndani zimene mukuphunzirazo?

Kukhulupirira Mulungu kuyenera kukuchititsani kuti muziuza ena zimene mumakhulupirira

9, 10. (a) Kodi mungayambe ndi kuuza ndani zimene mumaphunzira m’Baibulo? (b) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kuyamba kumalalikira limodzi ndi mpingo?

9 Mungamauze achibale anu, anzanu, anthu oyandikana nawo nyumba kapena anthu amene mumagwira nawo ntchito. Kuchita zimenezi n’kwabwino, koma muyenera kuzichita mwachikondi komanso mwaulemu. M’kupita kwa nthawi, mukhoza kukhala wokonzeka kuyamba kulalikira limodzi ndi mpingo. Mukadzaona kuti mukhoza kuyamba kulalikira ndi mpingo, mudzauze wa Mboni amene amaphunzira nanu Baibulo kuti mukufuna kuyamba kumalalikira limodzi ndi mpingo. Ngati naye ataona kuti ndinu wokonzekadi ndipo mumatsatira mfundo za m’Baibulo, padzakonzedwa zoti nonse muonane ndi akulu awiri amumpingo wanu.

10 Kodi cholinga choonana ndi akuluwo n’chiyani? Iwo adzakambirana nanu kuti aone ngati mukumvetsa komanso kukhulupirira mfundo zoyambirira za m’Baibulo, ngati mumatsatira zimene Baibulo limanena, ndiponso ngati mukufunadi kukhala wa Mboni za Yehova. Kumbukirani kuti akulu amasamalira anthu onse mumpingo, kuphatikizapo inuyo, ndiye simukuyenera kuchita mantha kukambirana nawo. (Machitidwe 20:28; 1 Petulo 5:2, 3) Pambuyo pa kukambiranaku, akuluwo adzakuuzani ngati mungayambe kulalikira limodzi ndi mpingo.

11. N’chifukwa chiyani munthu ayenera kusintha makhalidwe ena asanayambe kulalikira limodzi ndi mpingo?

11 Akulu akhoza kukuuzani kuti pali zinthu zina zimene mukufunika kusintha musanayambe kulalikira limodzi ndi  mpingo. Kodi kusintha zinthu zimene atchulazo n’kofunika bwanji? N’kofunika chifukwa tikamalalikira timakhala tikuimira Yehova, choncho khalidwe lathu liyenera kukhala labwino limene lingapangitse anthu kulemekeza Yehovayo.—1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21.

MUYENERA KULAPA NDIPONSO KUTEMBENUKA

12. N’chifukwa chiyani munthu aliyense afunika kulapa?

12 Palinso chinthu china chimene muyenera kuchita musanabatizidwe. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe.” (Machitidwe 3:19) Kodi kulapa n’kutani? Kulapa kumatanthauza kumva chisoni chifukwa cha zoipa zonse zimene tinachita. Mwachitsanzo, ngati poyamba munali ndi khalidwe lachiwerewere, muyenera kulapa. Ndipo ngakhale zitakhala kuti nthawi zonse mumayesetsa kuchita zinthu zabwino, muyenerabe kulapa chifukwa tonsefe ndi ochimwa ndipo timafuna kuti Mulungu atikhululukire.—Aroma 3:23; 5:12.

13. Kodi “kutembenuka” kumatanthauza chiyani?

13 Kodi kungomva chisoni ndi zomwe tinachita n’kokwanira? Ayi. Petulo ananena kuti tiyeneranso “kutembenuka.” Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kupewa makhalidwe onse oipa amene munkachita poyamba n’kuyamba kuchita zinthu zabwino. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyerekeze kuti mukupita dera linalake lomwe simunayambe mwapitako. Mutayenda kwa nthawi yaitali, mwazindikira kuti mukulowera kolakwika. Kodi mungatani? Sitikukayikira kuti mungaime, kutembenuka, n’kuyamba kulowera kolondola. Mofanana ndi zimenezi, n’kutheka kuti zimene mwakhala mukuphunzira m’Baibulo zakuthandizani kudziwa kuti pali makhalidwe komanso zinthu zina zimene muyenera kusiya. Mufunika kukhala wokonzeka “kutembenuka,” kapena kuti kusintha, n’kuyamba kuchita zinthu zabwino.

 MUYENERA KUDZIPEREKA KWA MULUNGU

Kodi munamulonjeza Yehova kuti mudzamutumikira?

14. Kodi mungadzipereke bwanji kwa Mulungu?

14 Chinthu chinanso chofunika kuchita musanabatizidwe ndi kudzipereka kwa Yehova. Mungadzipereke kwa Yehova, pomulonjeza m’pemphero kuti muzilambira iye yekha komanso muziona kuchita chifuniro chake kukhala kofunika kwambiri m’moyo wanu.—Deuteronomo 6:15.

15, 16. Kodi n’chiyani chingachititse munthu kuti adzipereke kwa Mulungu?

15 Kulonjeza kuti muzitumikira Yehova yekha kuli ngati kulonjeza kuti mudzakhala ndi munthu amene mumamukonda kwa moyo wanu wonse. Tayerekezani kuti mwamuna ndi mkazi ali pa chibwenzi. Mwamunayo akayamba kumudziwa bwino mkaziyo, amayamba kumukonda kwambiri ndipo kenako amafuna kumukwatira. Ngakhale kuti kukwatira kumapangitsa munthu kukhala ndi udindo waukulu, mwamunayo angamukwatirebe mkaziyo chifukwa choti amamukonda.

16 Inunso mukamaphunzira za Yehova mumayamba kumukonda kwambiri ndipo mumachita zonse zimene mungathe kuti muzimutumikira. Kuchita zimenezi kungakulimbikitseni kuti mupereke pemphero kwa Mulungu lomulonjeza kuti mudzamutumikira. Baibulo limanena kuti aliyense amene akufuna kutsatira Yesu, “adzikane yekha.” (Maliko 8:34) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti muziona kumvera Yehova kukhala chinthu chofunika kwambiri. Muziona kuti zimene Yehova amafuna kuti muzichita n’zofunika kwambiri kuposa zofuna kapena zolinga zanu.—Werengani 1 Petulo 4:2.

MUKHOZA KUKWANITSA

17. N’chifukwa chiyani anthu ena safuna kudzipereka kwa Yehova?

17 Anthu ena safuna kudzipereka kwa Yehova chifukwa amaganiza kuti sangathe kukwaniritsa zimene angalonjeze  zoti azimutumikira. Iwo safuna kukhumudwitsa Yehova, kapena amakhala ndi maganizo oti ngati sangadzipereke ndiye kuti Yehova sangawaimbe mlandu pa zimene akuchita.

18. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musamachite mantha kuti mwina mungadzakhumudwitse Yehova?

18 Ngati mumakonda Yehova simungakhale ndi mantha akuti mudzachita zinthu zomukhumudwitsa. Chikondi chanu chidzakupangitsani kuti muyesetse kuchita zinthu zimene munamulonjeza. (Mlaliki 5:4; Akolose 1:10) Simungaone kuti kuchita zimene Yehova amafuna n’kovuta. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3.

19. N’chifukwa chiyani simuyenera kuopa kudzipereka kwa Yehova?

19 Sikuti munthu amene amadzipereka kwa Yehova ndiye kuti amachita zinthu zolondola zokhazokha. Yehova safuna kuti tizichita zinthu zomwe sitingakwanitse. (Salimo 103:14) Iye adzakuthandizani kuti muzichita zinthu zoyenera. (Yesaya 41:10) Muzikhulupirira Yehova ndi mtima wanu wonse, ndipo ‘iye adzawongola njira zanu.’—Miyambo 3:5, 6.

KULENGEZA KWA ANTHU KUTI MUNADZIPEREKA KWA MULUNGU

20. Kodi mukadzipereka kwa Mulungu, chinthu chotsatira n’chiyani?

20 Kodi mukuona kuti ndinu wokonzeka kudzipereka kwa Yehova? Mukadzadzipereka kwa Yehova, padzatsala chinthu chimodzi choti muchite. Mudzayenera kubatizidwa.

21, 22. Kodi inuyo mungalengeze bwanji poyera za chikhulupiriro chanu?

21 Muyenera kumudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu wa mumpingo wanu kuti munadzipereka kwa Yehova ndipo mukufuna kubatizidwa. Kenako iye adzakonza  zoti akulu ena akambirane nanu mfundo zina zoyambirira za m’Baibulo. Ngati atatsimikiza kuti ndinudi woyenerera, adzakudziwitsani kuti mukhoza kubatizidwa pamsonkhano waukulu wotsatira wa Mboni za Yehova. Pamsonkhanowo, padzakambidwa nkhani imene idzafotokoze bwino tanthauzo la ubatizo. Kenako wokamba nkhaniyo adzafunsa anthu amene akuyembekezera kubatizidwa kuti ayankhe mafunso awiri osavuta. Pamene  mukuyankha mafunsowo, mumakhala ‘mukulengeza poyera’ za chikhulupiriro chanu.—Aroma 10:10.

22 Pambuyo pa nkhaniyo adzakubatizani. Mudzaviikidwa thupi lonse m’madzi. Ubatizowo udzasonyeza anthu  onse kuti munadzipereka kwa Yehova ndipo tsopano ndinu wa Mboni za Yehova.

ZIMENE UBATIZO UMATANTHAUZA

23. Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera” kumatanthauza chiyani?

23 Yesu ananena kuti ophunzira ake azidzabatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” (Werengani Mateyu 28:19.) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti mukuzindikira ulamuliro umene Yehova ali nawo ndiponso udindo umene Yesu ali nawo pokwaniritsa zimene Mulungu amafuna. Zimatanthauzanso kuti mumadziwa kuti Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu woyera pokwaniritsa cholinga chake.—Salimo 83:18; Mateyu 28:18; Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 1:21.

Mukabatizidwa, mumasonyeza kuti mukufuna muzichita zimene Mulungu amafuna

24, 25. (a) Kodi ubatizo umaimira chiyani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu womaliza?

24 Ubatizo umaimira chinthu chinachake chofunika kwambiri. Mukaviikidwa m’madzi, zimasonyeza kuti mwamwalira, kapena kuti mwasiya moyo wanu wakale. Mukamavuulidwa, mumayamba moyo wina watsopano wochita zimene Mulungu amafuna. Zimasonyeza kuti kuyambira pa nthawi imeneyi muzitumikira Yehova. Muyenera kukumbukira kuti simunadzipereke kwa munthu, bungwe, kapena ntchito inayake. Koma munadzipereka kwa Yehova.

25 Kudzipereka kudzakuthandizani kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ukule. (Salimo 25:14) Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti munthu angapulumuke chifukwa chongoti anabatizidwa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.” (Afilipi 2:12) Ubatizo umangokhala poyambira chabe. Koma kodi mungatani kuti mupitirize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova? Mutu womaliza wa m’bukuli udzayankha funso limeneli.