Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 6

Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?

Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?

1-3. (a) Kodi anthu amakhala ndi mafunso otani okhudza imfa? (b) Nanga zipembedzo zosiyanasiyana zimapereka mayankho otani?

BAIBULO limanena kuti tsiku lina “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) M’Mutu 5, tinaphunzira kuti dipo la Yesu ndi limene linachititsa kuti tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Koma panopa anthu amamwalirabe. (Mlaliki 9:5) Zimenezi zimachititsa kuti tizikhala ndi funso ngati lakuti, Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

2 Kudziwa yankho la funso limeneli n’kofunika kwambiri makamaka pamene m’bale wathu kapena mnzathu wamwalira. Tingadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi wapita kuti? Kodi akutiona? Kodi angatithandize? Nanga kodi tidzamuonanso?’

3 Zipembedzo zimapereka mayankho osiyanasiyana pa mafunso amenewa. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti ngati munthu ankachita zabwino, akamwalira amapita kumwamba koma ngati ankachita zoipa, amapita kukawotchedwa kumoto. Zina zimaphunzitsa kuti munthu akamwalira amasanduka mzimu ndipo amakakhala ndi achibale ake amene anamwalira kale. Pamene zinanso zimaphunzitsa kuti munthu akamwalira amaweruzidwa ndipo kenako amabadwanso ngati munthu wina kapena nyama.

4. Kodi zipembedzo zambiri zimaphunzitsa mfundo yofanana iti pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira?

4 Zipembedzo zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Koma zipembedzo zonsezi zimaphunzitsa mfundo imodzi yofanana yakuti munthu akamwalira, pali chinthu chinachake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo. Kodi zimenezi ndi zoona?

 KODI MUNTHU AKAMWALIRA AMAPITA KUTI?

5, 6. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

5 Yehova amadziwa zimene zimachitika munthu akamwalira, ndipo iye amatiuza kuti munthu akamwalira ndiye kuti moyo wake wathera pompo. Imfa imatanthauza kusakhalanso ndi moyo. Choncho munthu akamwalira, palibe chilichonse chimene chimapitiriza kukhalabe ndi moyo kwinakwake. * Munthu womwalira sangaone, sangamve komanso sangaganize.

6 Solomo analemba kuti: “Akufa sadziwa chilichonse.” Munthu wakufa sangakonde kapena kudana ndi wina aliyense, komanso “kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda.” (Werengani Mlaliki 9:5, 6, 10.) Baibulo, pa Salimo 146:4, limafotokozanso kuti munthu akamwalira, “zimene anali kuganiza” zimathera pomwepo.

ZIMENE YESU ANANENA PA NKHANI YA IMFA

Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale

7. Kodi Yesu anayerekezera imfa ndi chiyani?

7 Lazaro atamwalira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo.” Komatu Yesu sankatanthauza kuti Lazaro anali atagona tulo teniteni, chifukwa kenako ananena kuti: “Lazaro wamwalira.” (Yohane 11:11-14) Choncho Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Iye sananene kuti Lazaro wapita kumwamba kapena wapita kumene kuli achibale ake amene anamwalira kale. Ndiponso sananene kuti Lazaro akuzunzika kumoto kapena wabadwanso ngati munthu kapena nyama. Lazaro atamwalira zinangokhala ngati wagona tulo tofa nato. Palinso malemba ena omwe amayerekezera imfa ndi tulo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Sitefano ataphedwa, “anagona tulo ta imfa.” (Machitidwe 7:60) Mtumwi Paulo ananenanso za Akhristu ena omwe “anagona mu imfa.”—1 Akorinto 15:6.

8. Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu sanalenge anthu kuti azifa?

 8 Kodi Mulungu analenga Adamu ndi Hava n’cholinga choti akhale ndi moyo kwa nthawi yochepa kenako adzafe? Ayi. Yehova anawalenga kuti azisangalala ndi moyo mpaka kalekale. Yehova analenga anthu m’njira yoti azifuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlaliki 3:11) Palibe makolo amene angasangalale kuona ana awo akukumana ndi mavuto komanso kufa, ndipo ndi mmenenso Yehova amamvera ndi anthufe. Komano ngati Mulungu anatilenga n’cholinga choti tizikhala ndi moyo mpaka kalekale, n’chifukwa chiyani timafa?

 N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAFA?

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti lamulo limene Yehova anapereka kwa Adamu ndi Hava linali losavuta kulitsatira?

9 Adamu ali m’munda wa Edeni, Yehova anamuuza kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:9, 16, 17) Lamulo limeneli linali losavuta kulitsatira, ndipotu Yehova ndi amene anali ndi ufulu wouza Adamu ndi Hava zimene zinali zabwino kapena zoipa. Kumvera Yehova kukanasonyeza kuti ankamulemekeza. Kukanasonyezanso kuti ankayamikira zinthu zonse zomwe anawapatsa.

10, 11. (a) Kodi Satana anatani kuti achititse Adamu ndi Hava kusamvera Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Adamu ndi Hava analibe chifukwa chomveka chowapangitsa kusamvera lamulo la Mulungu?

10 N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Yehova. Satana anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Hava anayankha kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”—Genesis 3:1-3.

11 Koma Satana anati: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4-6) Satana ankafuna kuti Hava aziganiza zoti angathe kumasankha yekha zabwino kapena zoipa. Komanso anamunamiza pomuuza kuti sangafe ngati atadya chipatso chimene Mulungu anawaletsa. Hava atamva zimenezi, anadya chipatso chimene Mulungu anawaletsa ndipo kenako anapatsanso mwamuna wake. Adamu ndi Hava ankadziwa kuti Yehova anawauza kuti asadzadye chipatsocho. Choncho kudya chipatsochi kunali kusamvera mwadala lamulo losavuta  kutsatira komanso lomveka bwino limene Mulungu anawapatsa. Zimene anachitazi zinasonyezanso kuti sankalemekeza Atate wawo wakumwamba. Iwo analibe chifukwa chomveka chochitira zimenezi.

12. N’chifukwa chiyani zinali zokhumudwitsa kwambiri pamene Adamu ndi Hava sanamvere Yehova?

12 N’zomvetsa chisoni kuti makolo athu oyambirira sanalemekeze Mlengi wawo. Mwachitsanzo, kodi mungamve bwanji ngati ana anu atakuukirani n’kuyamba kuchita zinthu zotsutsana nanu? N’zoonekeratu kuti zingakupwetekeni kwambiri.

Adamu analengedwa kuchokera kufumbi ndipo anabwereranso kufumbi

13. Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamene anauza Adamu kuti “kufumbiko udzabwerera”?

13 Pamene Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu, anataya mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. Yehova anauza Adamu kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” (Werengani Genesis 3:19.) Zimenezi zinkatanthauza kuti Adamu adzakhalanso fumbi ngati mmene zinalili asanalengedwe. (Genesis 2:7) Adamu atachimwa anafa ndipo anabwerera kufumbi.

14. N’chifukwa chiyani timafa?

14 Adamu ndi Hava akanamvera Mulungu, akanakhala alipobe mpaka pano. Koma kusamvera kwawo kunachititsa kuti achimwire Mulungu ndipo kenako anafa. Uchimo uli ngati matenda oopsa amene tinatengera kwa makolo athu oyambirira. Tonsefe timabadwa tili ochimwa ndipo n’chifukwa chake timafa. (Aroma 5:12) Koma zimenezi sizimene Mulungu  ankafuna pamene ankalenga anthu. Mulungu safuna kuti anthu azimwalira ndipo Baibulo limati imfa ndi “mdani.”—1 Akorinto 15:26.

TIMAKHALA OMASUKA CHIFUKWA CHODZIWA ZOONA

15. Kodi kudziwa zoona zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kumatithandiza bwanji?

15 Kudziwa zoona pa nkhani ya imfa kumatithandiza kuti tisasocheretsedwe ndi mabodza osiyanasiyana. Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akamwalira samva kupweteka kulikonse komanso sangathe kudana ndi wina aliyense. Sitingathe kulankhula naye ndipo iyenso sangalankhule nafe. Sitingamuthandize ndipo iyenso sangatithandize. Choncho sitiyenera kumuopa chifukwa sangativulaze. Komabe zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti munthu akafa amakhalabe ndi moyo kwinakwake ndipo tingamuthandize popereka ndalama kwa atsogoleri achipembedzo kapena anthu ena amene amaonedwa ngati oyera kuti amupempherere. Koma kudziwa zoona zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira, kumatithandiza kuti tisapusitsidwe ndi mfundo zabodza zimenezi.

16. Kodi zipembedzo zambiri zimaphunzitsa bodza lotani lokhudza akufa?

16 Satana amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga pofuna kupusitsa anthu kuti azikhulupirira zoti munthu akafa amakakhalabe ndi moyo kwinakwake. Mwachitsanzo, atsogoleri azipembedzo ena amaphunzitsa kuti munthu akafa, mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake. Kodi zimenezi ndi zomwe chipembedzo chanu chimaphunzitsa, kapena chimaphunzitsa zimene Baibulo limanena? Satana amagwiritsirabe ntchito bodza pofuna kuchititsa anthu kuti asamakhulupirire Yehova.

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo yoti Mulungu amazunza anthu kumoto imanyozetsa Yehova?

17 Zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa ndi zochititsa mantha kwambiri. Mwachitsanzo, zipembedzo zina  zimanena kuti anthu amene amachita zoipa adzawotchedwa kumoto mpaka kalekale. Limeneli bodza ndipo kunena zimenezi kungakhale kuchitira mwano Yehova. Iye sangalole kuti anthu azizunzika mwa njira imeneyi. (Werengani 1 Yohane 4:8.) Kodi mungamve bwanji mutaona munthu wina akulanga mwana wake pomuwotcha manja pamoto? N’zodziwikiratu kuti mukhoza kumuona kuti ndi munthu wankhanza ndipo simungafune n’komwe kuti akhale mnzanu. Mmenemutu ndi mmene Satana amafuna kuti tizionera Yehova.

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa akufa?

18 Zipembedzo zina zimanena kuti munthu akafa, amasanduka mzimu. Zimaphunzitsanso kuti tikuyenera kulemekeza komanso kuopa mizimu imeneyi chifukwa ikhoza kukhala anzathu kapenanso adani athu oopsa kwambiri. Anthu ambiri amakhulupirira bodza limeneli. Ndipo zimenezi zimawachititsa kuopa anthu akufa n’kuyamba kuwalambira m’malo molambira Yehova. Koma musaiwale kuti anthu akufa sangamve kapena kuchita chilichonse, choncho sitiyenera kuwaopa. Yehova ndi amene anatilenga. Iye ndi Mulungu weniweni ndipo tiyenera kulambira iye yekha basi.—Chivumbulutso 4:11.

19. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira n’kothandiza bwanji?

19 Tikadziwa zoona zenizeni zokhudza imfa, timakhala omasuka ku zinthu zabodza zimene zipembedzo zina zimanena. Kudziwa zoona pa nkhani imeneyi kumatithandiza kumvetsa bwino zinthu zosangalatsa kwambiri zimene Yehova wakonza zokhudza moyo wathu komanso tsogolo lathu.

20. Kodi tiphunzira chiyani m’mutu wotsatira?

20 Zaka zambiri zapitazo, mtumiki wina wa Mulungu dzina lake Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (Yobu 14:14) Kodi zingathekedi kuti munthu amene wamwalira akhalenso ndi moyo? Zimene Mulungu amatiuza m’Baibulo n’zosangalatsa kwambiri. Tiona zimenezi m’mutu wotsatira.

^ ndime 5 Anthu ena amakhulupirira kuti mzimu umapitiriza kukhalabe ndi moyo munthu akamwalira. Kuti mumve zambiri, onani Mawu Akumapeto 17 ndi 18.