Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Anali ndi Cholinga Chotani Polenga Anthu?

Kodi Mulungu Anali ndi Cholinga Chotani Polenga Anthu?

MUKAMAWERENGA nyuzipepala, kuonera TV kapena kumvetsera wailesi, nkhani zimene mumamva nthawi zambiri ndi zokhudza kuphwanya malamulo, nkhondo komanso uchigawenga. N’kuthekanso kuti inuyo mukuvutika chifukwa cha matenda kapena chifukwa choti mnzanu kapena wachibale wanu anamwalira.

Dzifunseni kuti:

  • Kodi Mulungu ankafuna kuti moyo wanga komanso wa achibale anga ukhale wotere?

  • Kodi ndingapeze kuti thandizo kuti ndithe kulimbana ndi mavuto anga?

  • Kodi nthawi ina zidzatheka kuti anthu azikhala mwamtendere padzikoli?

Baibulo lili ndi mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa.

 BAIBULO LIMAPHUNZITSA KUTI MULUNGU ADZACHITA ZINTHU ZOTSATIRAZI PADZIKO LAPANSI:

 ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ZIKHOZA KUKUTHANDIZANI

Mwina mukuganiza kuti zimene mwawerenga m’masamba apitawa ndi zinthu zosatheka. Koma Mulungu analonjeza kuti achita zimenezi posachedwapa ndipo Baibulo limafotokoza mmene zimenezi zidzachitikire.

Kuwonjezera pa zimenezi, Baibulo limafotokozanso zinthu zimene zingatithandize kuti tizikhala osangalala ngakhale panopa. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimakupangitsani kukhala ndi nkhawa? N’kutheka kuti muli ndi mavuto a zachuma, a m’banja, matenda ndiponso mwina wachibale wanu kapena mnzanu anamwalira. Baibulo lingakuthandizeni kupirira mavuto amenewa komanso lingakulimbikitseni chifukwa limayankha mafunso ngati awa:

  • N’chifukwa chiyani timavutika?

  • Kodi tingapirire bwanji mavuto amene tili nawo?

  • Kodi zingatheke kuti banja lathu lizisangalala?

  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

  • Kodi n’zotheka kudzaonananso ndi anzathu komanso achibale athu amene anamwalira?

  • Kodi n’chiyani chingatithandize kutsimikizira kuti zimene Mulungu analonjeza zidzachitikadi?

 Kuwerenga bukuli komwe mukuchitaku ndi umboni woti mukufuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Bukuli likuthandizani kwambiri. Ndime iliyonse ili ndi funso lake ndipo mafunsowo akuthandizani kulimvetsa bwino Baibulo. Anthu ambiri amasangalala akamaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo tikukhulupirira kuti nanunso musangalala. Mulungu adzakudalitsani mukamayesetsa kufufuza zimene Baibulo limaphunzitsa.