Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 5

Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa

Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa

1, 2. (a) Kodi inuyo mumaona kuti mphatso ndi yamtengo wapatali ikakhala yotani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti dipo la Yesu ndi mphatso yamtengo wapatali kuposa zonse?

PA MPHATSO zimene munalandirapo, kodi ndi mphatso iti imene mumaona kuti ndi yamtengo wapatali? Kuti mphatso ikhale yamtengo wapatali sizichita kufunika kuti ikhale ya ndalama zambiri. Ngati mphatsoyo yakusangalatsani kapena ngati mukuona kuti ikuthandizani, mumayamikira kwambiri.

2 Mulungu anatipatsa mphatso zambirimbiri koma pali mphatso imodzi yomwe ndi yofunika kuposa zonse. Monga mmene tionere m’mutuwu, Yehova anatumiza Mwana wake Yesu Khristu padziko lapansi kudzapereka moyo wake monga dipo. (Werengani Mateyu 20:28.) Iye anachita zimenezi kuti tidzapeze moyo wosatha. Zimene Yehova anachitazi ndi umboni woti amatikonda kwambiri.

KODI DIPO N’CHIYANI?

3. N’chifukwa chiyani anthufe timafa?

3 Dipo la Yesu ndi njira imene Yehova anagwiritsa ntchito kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Kuti timvetse chifukwa chake panafunika dipo, tiyenera kudziwa zimene zinachitika kalekale m’munda wa Edeni. Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anachimwa ndipo izi zinachititsa kuti patapita nthawi afe. Nafenso timafa chifukwa tinatengera uchimo wawowo.—Onani Mawu Akumapeto 9.

4. Kodi Adamu anali ndani, nanga anali wotani?

4 Adamu anali munthu woyambirira kulengedwa. Iye  anali wangwiro ndipo izi zikutanthauza kuti sakanadwala, kukalamba ndiponso kufa. Yehova anali ngati bambo ake chifukwa ndi amene anamulenga ndipo ankalankhula naye pafupipafupi. (Luka 3:38) Mulungu anafotokozera Adamu zinthu zoyenera kuchita ndipo anam’patsanso ntchito yosangalatsa yoti azigwira.—Genesis 1:28-30; 2:16, 17.

5. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Adamu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu”?

5 Adamu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova analenga Adamu ndi makhalidwe ofanana ndi ake monga chikondi, nzeru, chilungamo ndi mphamvu. Anamupatsanso ufulu wosankha zimene akufuna kuchita. Adamu sanalengedwe ngati mashini omwe saganiza. Iye anali ndi ufulu wosankha zomwe akufuna kuchita, kaya zabwino kapena zoipa. Ngati akanasankha kumvera Mulungu, akanakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso.

6. Kodi Adamu anataya chiyani chifukwa chosamvera Mulungu, nanga kuchimwa kwake kunatikhudza bwanji ifeyo?

6 Pamene Adamu anasankha kusamvera Mulungu, anataya mwayi waukulu chifukwa anaweruzidwa kuti ayenera kufa. Kusamvera kwake kunachititsa kuti asakhalenso pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti asakhale ndi moyo wangwiro. Kunachititsanso kuti athamangitsidwe m’Paradaiso mmene ankakhala. (Genesis 3:17-19) Adamu ndi Hava analibe mwayi woti Mulungu awamvere chisoni chifukwa anasankha dala kusamumvera. Kusamvera kwa Adamu kunachititsa kuti ‘uchimo ulowe m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Pamene Adamu anachimwa tingati ‘anadzigulitsa’ limodzi ndi ana ake omwe ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Aroma 7:14) Koma kodi ifeyo tikhoza kupulumutsidwa ku ukapolo umenewu? Inde, n’zotheka.

7, 8. Kodi mawu akuti dipo amatanthauza chiyani?

 7 Kodi mawu akuti dipo amatanthauza chiyani? Dipo lingatanthauze zinthu ziwiri. Choyamba, ndi ndalama kapena katundu amene amaperekedwa pofuna kuti munthu amene wagwidwa kapena zinthu zimene zatengedwa zibwezedwe. Chachiwiri, dipo ndi ndalama kapena katundu amene amaperekedwa polipira zinthu zimene zawonongedwa. Ndalama kapena katunduyo amayenera kukhala wofanana ndendende ndi mtengo wa zimene zawonongedwazo.

8 Palibe munthu amene akanatha kulipira zinthu zimene zinawonongeka pamene Adamu anachimwa. Koma Yehova anakonza njira yotipulumutsira ku uchimo ndi imfa. Tiyeni tikambirane mmene Yehova anaperekera dipo komanso mmene lingatithandizire.

MMENE YEHOVA ANAPEREKERA DIPO

9. Kodi chinkafunika n’chiyani kuti dipo liperekedwe?

9 Koma kodi n’chifukwa chiyani panalibe munthu amene akanapereka moyo wake polipira moyo umene Adamu anataya? N’chifukwa chakuti tonsefe ndife ochimwa. (Salimo 49:7, 8) Popeza Adamu anataya moyo wangwiro, pankafunikanso moyo wina wangwiro kuti ukhale “dipo lokwanira ndendende.”—1 Timoteyo 2:6.

10. Kodi Yehova anachita chiyani kuti dipo liperekedwe?

10 Ndiye kodi Yehova anapereka bwanji dipo? Yehova anatumiza padziko lapansi Yesu, yemwe ndi Mwana wake wapadera. Mwana ameneyu ndi amene anayambirira kumulenga asanalenge zinthu zina zonse. (1 Yohane 4:9, 10) Yesu analolera kusiyana ndi Atate wake n’kubwera padziko lapansi pano. (Afilipi 2:7) Yehova anangosamutsa moyo wa Yesu kumwamba choncho Yesuyo anabadwa padzikoli ali wangwiro.—Luka 1:35.

Yehova anapereka Mwana wake kuti akhale dipo

11. Kodi zinatheka bwanji kuti munthu mmodzi apereke dipo la anthu onse?

11 Paja Adamu atachimwa, anapangitsa kuti anthu onse asakhale angwiro. Ndiye kodi zikanatheka kuti munthu  mmodzi apulumutse anthu onse ku uchimo ndi imfa? Inde. (Werengani Aroma 5:19.) Yesu yemwe anali wosachimwa anapereka moyo wake kuti ukhale dipo. (1 Akorinto 15:45) Moyo wake wangwiro ndi womwe ukanathandiza kuti ana onse a Adamu amasuke ku uchimo ndi imfa.—1 Akorinto 15:21, 22.

12. N’chifukwa chiyani kunali koyenera kuti Yesu azunzidwe?

12 Baibulo limafotokoza mavuto amene Yesu anakumana nawo asanaphedwe. Anakwapulidwa mwankhanza, kukhomeredwa pamtengo wozunzirapo anthu ndipo kenako anamusiya kuti azingozunzika mpaka kufa. (Yohane 19:1, 16-18, 30) N’chifukwa chiyani kunali koyenera kuti Yesu azunzike chonchi? Chifukwa Satana ananena kuti munthu sangakhale wokhulupirika kwa Mulungu ngati atakumana ndi mavuto aakulu. Koma Yesu anasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kukhalabe wokhulupirika ngakhale atakumana ndi mavuto. Mosakayikira, Yehova anasangalala kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi.—Miyambo 27:11; onani Mawu Akumapeto 15.

13. Kodi chinafunikanso n’chiyani kuti dipo liperekedwe?

13 Kodi chinafunikanso n’chiyani kuti dipo liperekedwe? M’chaka cha 33 C.E., pa tsiku la 14 la mwezi womwe Ayuda ankautchula kuti Nisani, Yehova analola kuti Yesu aphedwe ndi adani ake. (Aheberi 10:10) Patatha masiku atatu, Yehova anamuukitsa ndipo anakhalanso mzimu ngati mmene analili asanabwere padziko lapansi. Koma kuti amalizitse zonse zofunika kuti dipo liperekedwe, Yesu anafunikanso kubwerera kumwamba. Atafika kumwambako anaonekera pamaso pa Mulungu ndipo Mulungu anavomereza zonse zimene iye anachita ali padziko lapansi popereka moyo wake monga dipo. (Aheberi 9:24) Apa ndiye kuti Yesu analipira moyo wangwiro umene Adamu anataya. Chifukwa cha zimene Yesu anachitazi, tili ndi mwayi womasulidwa ku uchimo ndi imfa.—Werengani Aroma 3:23, 24.

 MMENE DIPO LA YESU LINGAKUTHANDIZIRENI

14, 15. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atikhululukire machimo athu?

14 Mphatso yamtengo wapatali imeneyi inayamba kale kutithandiza. Tiyeni tione mmene imatithandizira panopa komanso madalitso amene tidzapeze m’tsogolo chifukwa cha mphatsoyi.

15 Mulungu amatikhululukira machimo athu. Nthawi zambiri zimativuta kuti tichite zinthu zoyenera. Nthawi zina timalankhula kapena kuchita zinthu zolakwika. (Akolose 1:13, 14) Kodi tingatani kuti Mulungu azitikhululukira? Tiyenera kuzindikira kuti talakwa n’kupempha Yehova kuti atikhululukire. Tikachita zimenezi, Mulungu amatikhululukira machimo athu.—1 Yohane 1:8, 9.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikudziimba mlandu chifukwa cha zomwe talakwitsa?

16 Tikachimwa sitimangodziimbabe mlandu. Tikachita zinthu zoipa, timadziimba mlandu ndipo izi zimachititsa kuti tisamasangalale komanso kuti tizidziona kuti ndife osafunika. Koma sitiyenera kutaya mtima zimenezi zikachitika. Ngati titapemphera kwa Yehova, akhoza kumva pemphero lathulo n’kutikhululukira chifukwa cha nsembe ya dipo imene Yesu anapereka. (Aheberi 9:13, 14) Yehova amafuna kuti tizimuuza mavuto athu komanso zimene timalakwitsa. (Aheberi 4:14-16) Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba.

17. Kodi tidzapeza madalitso ati chifukwa choti Yesu anatifera?

17 Tidzakhala ndi moyo wosatha. Baibulo limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Chifukwa chakuti Yesu anatifera, n’zotheka kudzakhala ndi moyo wosatha komanso wopanda mavuto. (Chivumbulutso 21:3, 4) Tiyeni tione zimene tingachite kuti tidzalandire madalitso amenewa komanso mmene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso ya dipo.

 MMENE MUNGASONYEZERE KUTI MUMAYAMIKIRA MPHATSOYI

18. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amatikonda kwambiri?

18 N’zodziwikiratu kuti munthu wina akakupatsani mphatso yabwino mumasangalala kwambiri. Dipo la Yesu ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa ndipo tiyenera kumuthokoza kwambiri. Baibulo limanena kuti “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha” kuti adzatifere. (Yohane 3:16) Tikudziwanso kuti Yesu amatikonda chifukwa anadzipereka ndi mtima wonse kubwera padzikoli. (Yohane 15:13) Choncho mphatso ya dipo iyenera kukuthandizani kuzindikira kuti Yehova komanso Yesu amakukondani kwambiri.—Agalatiya 2:20.

Tikamaphunzira zokhudza Yehova, timayamba kumukonda komanso kumuona kuti ndi mnzathu wapamtima

19, 20. (a) Kodi mungatani kuti muziona kuti Yehova ndi mnzanu wapamtima? (b) Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhulupiriradi dipo la Yesu?

19 Popeza mwadziwa kuti Yehova amakukondani kwambiri, kodi mungatani kuti iye akhale mnzanu? Zimakhalatu zovuta kwambiri kuti tiyambe kukonda munthu amene sitikumudziwa. Lemba la Yohane 17:3 limanena kuti n’zotheka kumudziwa Yehova. Mukadziwa zambiri zokhudza Yehova, mungayambe kumukonda kwambiri, kuchita zimene iye amasangalala nazo komanso kumuona kuti ndi mnzanu wapamtima. Choncho pitirizani kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zambiri zokhudza Yehova.—1 Yohane 5:3.

20 Muzisonyeza kuti mumakhulupirira nsembe ya dipo la Yesu. Baibulo limanena kuti “wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Kodi kukhala ndi chikhulupiriro kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kuchita zimene Yesu anaphunzitsa. (Yohane 13:15) Kungonena kuti timakhulupirira Yesu sikokwanira. Tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti timakhulupiriradi dipo la  Yesu. Lemba la Yakobo 2:26 limati: “Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.”

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu chaka chilichonse? (b) Kodi tidzaphunzira chiyani m’Mutu 6 ndi 7?

21 Muzipezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Yesu anauza otsatira ake kuti azichita mwambo wokumbukira imfa yake. Timachita mwambowu chaka chilichonse, ndipo umatchedwa kuti Chikumbutso kapena “Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.” (1 Akorinto 11:20; Mateyu 26:26-28) Yesu amafuna kuti tizikumbukira kuti anapereka moyo wake wangwiro monga dipo chifukwa cha ife. Iye ananena kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Werengani Luka 22:19.) Mukamapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu, mumasonyeza kuti mumayamikira chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Yesu anasonyeza popereka dipo.—Onani Mawu Akumapeto 16.

22 Monga taonera, dipo la Yesu ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri kuposa zonse. (2 Akorinto 9:14, 15) Anthu ambirimbiri amene anamwalira adzapindulanso ndi mphatso imeneyi. M’Mutu 6 ndi 7 tidzaphunzira kuti zimenezi zidzatheka bwanji.