Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 2 2017 | Kodi Mulandira Mphatso Yaikulu Imene Mulungu Wapereka?

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi mphatso yaikulu kwambiri imene Mulungu anatipatsa ndi iti?

Baibulo limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.”Yohane 3:16.

Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu anatumizira Yesu padziko lapansi kuti adzatifere komanso zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira mphatsoyi.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Mphatso Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse

Baibulo limafotokoza za mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene ingathandize anthu amene ailandira kuti adzapeze moyo wosatha. Kodi pangakhale mphatso yaikulu kuposa imeneyi?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Mphatso Imene Mulungu Watipatsa Ndi Yamtengo Wapatali?

Kodi ndi zinthu ziti zimene zimachititsa kuti mphatso ikhale yamtengo wapatali? Kuganizira zimenezi kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri dipo.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumayamikira Mphatso Imeneyi?

Kodi chikondi cha Khristu chimatilimbikitsa kuchita chiyani?

Kodi Atumiki Achikhristu Safunika Kukwatira?

Zipembedzo zina zimaletsa kuti atsogoleri awo akwatire. Koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi?

Akapolo Anapeza Ufulu M’mbuyomu Komanso Masiku Ano

Kale, anthu a Mulungu anapulumutsidwa ku ukapolo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ambiri adakali akapolo.

Ubwino wa Mtima Wopatsa

Mtima wopatsa umathandiza inuyo komanso anthu ena. Umathandizanso kuti anthu azigwirizana. Kodi mungatani kuti muzisangalala chifukwa chopatsa?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Baibulo limanena kuti “masiku otsiriza” idzakhala “nthawi yovuta.” Kodi inuyo mukuona umboni woti tili m’masiku otsiriza?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Nsembe ya Yesu Imawombola Bwanji “Anthu Ambiri”?

Kodi dipo limawombola bwanji anthu ku uchimo?