Pitani ku nkhani yake

Kodi Nsembe ya Yesu Imawombola Bwanji “Anthu Ambiri”?

Kodi Nsembe ya Yesu Imawombola Bwanji “Anthu Ambiri”?

Yankho la m’Baibulo

 Nsembe ya Yesu ndi njira imene Mulungu amagwiritsa ntchito populumutsa anthu ku uchimo ndi imfa. Baibulo limanena kuti magazi amene Yesu anakhetsa anali dipo lomasula anthu. (Aefeso 1:7; 1 Petulo 1:18, 19) N’chifukwa chake Yesu ananena kuti anabwera “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”​—Mateyu 20:28.

N’chifukwa chiyani “anthu ambiri” anafunika kuwomboledwa?

 Poyamba Adamu, yemwe anali munthu woyamba kulengedwa, anali wangwiro kapena kuti wopanda uchimo. Iye akanatha kukhala ndi moyo wosatha koma anataya mwayiwu chifukwa chosamvera Mulungu. (Genesis 3:17-19) Ndiyeno ana amene anabereka anawapatsiranso uchimo wakewu. (Aroma 5:12) M’pake kuti Baibulo limasonyeza kuti Adamu ‘anadzigulitsa’ ndiponso anagulitsa ana ake kuti akhale akapolo a uchimo ndi imfa. (Aroma 7:14) Popeza ana ake onse ndi ochimwa, sangathe kuwombola moyo wawo ku ukapolowu.​—Salimo 49:7, 8.

 Mulungu anamvera chisoni ana a Adamu chifukwa analibe tsogolo lililonse. (Yohane 3:16) Koma popeza iye ndi wachilungamo sakanatha kungonyalanyaza machimo awo kapena kuwakhululukira popanda chifukwa chomveka. (Salimo 89:14; Aroma 3:23-26) Choncho chifukwa chakuti Mulungu amakonda anthu, anakonza njira yoti machimo awo azikhululukidwa ndiponso azifafanizidwa. (Aroma 5:6-8) Ndipo njira imeneyo ndi dipo.

Kodi dipo n’chiyani?

 M’Baibulo mawu akuti “dipo” amatanthauza zinthu zitatu izi:

  1.   Malipiro a chinthu chinachake.​—Numeri 3:46, 47.

  2.   Ndalama kapena zinthu zimene zaperekedwa n’cholinga choti munthu amasulidwe.​—Ekisodo 21:30.

  3.   Mtengo wofanana ndendende ndi chinthu chimene chikuwomboledwa. a

 Tiyeni tione kugwirizana kwa zinthu zitatuzi ndi nsembe ya dipo ya Yesu Khristu.

  1.   Malipiro. Baibulo limanena kuti Akhristu ‘anagulidwa pa mtengo wokwera.’ (1 Akorinto 6:20; 7:23) Mtengowo ndi magazi a Yesu omwe Mulungu anagwiritsa ntchito ‘pogula anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.’—Chivumbulutso 5:8, 9.

  2.   Kumasula. Nsembe ya Yesu ndi ‘dipo lotimasula’ ku uchimo.​—1 Akorinto 1:30; Akolose 1:14; Aheberi 9:15.

  3.   Kufanana ndendende. Nsembe ya Yesu imafanana ndendende ndi moyo wangwiro umene Adamu anataya. (1 Akorinto 15:21, 22, 45, 46) Baibulo limati: “Monga mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo [Adamu], ambiri anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu [Yesu Khristu], ambiri adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) Lembali likusonyeza mmene imfa ya munthu mmodzi ingalipirire uchimo wa anthu ambiri. Nsembe ya Yesu ndi “dipo lokwanira ndendende m’malo mwa onse” amene amayesetsa kuchita zoyenera.—1 Timoteyo 2:5, 6.

a M’Baibulo, mawu amene anamasuliridwa kuti “dipo” amanena za malipiro kapena chinthu chimene chimaperekedwa pogula zinthu. Mawu achiheberi akuti, ka·pharʹ amatanthauza “kuphimba.” Nthawi zambiri mawuwa amanena za kuphimba machimo. (Salimo 65:3, mawu a m’munsi) Mawu ena ofanana nawo akuti koʹpher amatanthauza malipiro amene amaperekedwa kuti awombole chinachake. (Ekisodo 21:30) Mawu achigiriki akuti lyʹtron omwe nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “dipo” angatanthauzenso “malipiro owombolera” chinthu. (Mateyu 20:28; Baibulo lakuti, The New Testament in Modern Speech, lolembedwa ndi R.  F.  Weymouth) Anthu olemba mabuku m’Chigiriki ankagwiritsa ntchito mawu akuti lyʹtron ponena za malipiro amene ankaperekedwa kuti munthu wogwidwa pa nkhondo kapena kapolo amasulidwe.