Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiziona Kuti Tsiku Lina Pamlungu Ndi Lopatulika?

Kodi Tiziona Kuti Tsiku Lina Pamlungu Ndi Lopatulika?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Tiziona Kuti Tsiku Lina Pamlungu Ndi Lopatulika?

PADZIKO lonse, anthu azipembedzo zosiyanasiyana monga Asilamu, Ayuda komanso Akhristu, ali ndi tsiku limodzi pamlungu limene amaliona kuti ndi lopatulika. N’chifukwa chiyani amakhala ndi tsiku lapadera lolambirira? Munthu wina wachisilamu, dzina lake Ibrahim, yemwe amapita kumzikiti Lachisanu lililonse kukapemphera komanso kukamva ulaliki, ananena kuti kuchita zimenezi kumamuthandiza kuti aziyandikana ndi Mulungu komanso azikhala ndi mtendere wa mumtima.

Koma kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu amafuna kuti tikhale ndi tsiku lopatulika pamlungu? Kodi kukhala ndi tsiku lapadera lolambirira kumatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu?

Zinali Zakanthawi

Zaka zoposa 3,500 zapitazo, Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo apadera kudzera mwa mneneri Mose. Malamulo amenewa anaphatikizapo lamulo lokhala ndi masiku opuma, kapena kuti masiku a Sabata. Pa masiku amenewa anthu sankagwira ntchito pofuna kuchita zinthu zauzimu. Nthawi zambiri, anthu anali ndi tsiku limodzi pamlungu limene ankapuma. Sabatali linkayamba Lachisanu, dzuwa likangolowa ndipo linkatha Loweruka, dzuwa likangolowa.—Ekisodo 20:8-10.

Kodi anthu a mitundu yonse ankafunika kusunga Sabata limeneli? Ayi. Malamulo amene Mulungu anapatsa Mose anali opita kwa Aisiraeli ndi anthu amene anatembenukira ku chipembedzo chawo basi. Mulungu anauza Mose kuti: “Ana a Isiraeli azisunga sabata . . . Chimenechi n’chizindikiro pakati pa ine ndi ana a Isiraeli mpaka kalekale.” *Ekisodo 31:16, 17.

Baibulo limanena kuti Chilamulo cha Mose chinali “mthunzi wa zimene zinali kubwera.” (Akolose 2:17) Choncho, lamulo losunga Sabata linali m’gulu la malamulo okhalapo kwakanthawi, omwe ankachitira chithunzi zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. (Aheberi 10:1) Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anathetsa Chilamulo cha Mose, kuphatikizapo lamulo losunga Sabata, nthawi imene Yesu anaphedwa. (Aroma 10:4) Kodi Chilamulochi chinalowedwa m’malo ndi chiyani?

Njira Yatsopano Yolambirira

Chilamulo cha Mose chitakwaniritsa cholinga chake, panabwera njira yatsopano yolambirira Mulungu ndipo Baibulo limafotokoza bwino njira imeneyi. Kodi njira yatsopanoyi imafunanso kuti anthu azipatula tsiku limodzi pamlungu loti azilambira?

Malemba amasonyeza kuti malamulo ena amene anaperekedwa kwa Aisiraeli amagwiranso ntchito kwa Akhristu masiku ano. Ena mwa malamulowa ndi okhudza kupewa mafano ndi dama komanso magazi. (Machitidwe 15:28, 29) Koma lamulo losunga Sabata silinaphatikizidwe pa malamulo amene Akhristu ayenera kutsatira.—Aroma 14:5.

Kodi Baibulo limatiuzanso zinthu zina zotani zokhudza kulambira kwa Akhristu oyambirira? Iwo ankakumana pafupipafupi n’kumapemphera, kuwerenga malemba, kumvetsera ena akukamba nkhani, ndi kuimba nyimbo zotamanda Mulungu. (Machitidwe 12:12; Akolose 3:16) Pamisonkhano imeneyi, Akhristu ankalandira malangizo, kulimbitsa chikhulupiriro chawo ndiponso kulimbikitsana.—Aheberi 10:24, 25.

Koma m’Baibulo mulibe vesi lililonse limene limanena kuti Akhristu ayenera kukhala ndi tsiku limodzi pamlungu, kaya Lamlungu kapena tsiku lina lililonse, n’kumalambira Mulungu. Ngati zili choncho, ndiyeno n’chifukwa chiyani anthu ambiri amene amati ndi Akhristu amaona kuti tsiku Lamlungu ndi lopatulika? Anthu anayamba kulambira pa tsiku Lamlungu pamene Baibulo linamalizidwa kulembedwa. Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kutsatira zikhulupiriro komanso miyambo yosiyanasiyana yosagwirizana ndi Baibulo.

Kodi patapita zaka Mulungu anakhazikitsanso tsiku lapadera loti anthu azimulambira? Ayi. Zinthu zonse zokhudza kulambira Mulungu movomerezeka zimafotokozedwa mwatsatanetsatane m’Baibulo. Ndipo palibe buku linanso louziridwa kuwonjezera pa Baibulo, lomwe limafotokoza zinthu zinanso za mmene tiyenera kulambirira Mulungu. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Komabe, ngati ifeyo kapena mngelo wochokera kumwamba angalengeze nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma nkhaniyo n’kukhala yosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembereredwa.”—Agalatiya 1:8.

Kulambira Kumene Kumasangalatsa Mulungu

Ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo a m’nthawi ya Yesu ankasunga Sabata, kulambira kwawo kunali kosavomerezeka pamaso pa Mulungu chifukwa mitima yawo inali yoipa. Iwo ankakonda kwambiri ndalama ndiponso ankanyoza anthu wamba. Komanso ankakonda malo olemekezeka, anali achinyengo, ndiponso ankalowerera ndale. (Mateyu 23:6, 7, 29-33; Luka 16:14; Yohane 11:46-48) Iwo ankanena kuti akuchita chifuniro cha Mulungu koma Sabata limene Mulungu analikhazikitsa kuti anthu azipuma analisandutsa mtolo wolemetsa, chifukwa anakhazikitsa malamulo ambirimbiri opanga okha.—Mateyu 12:9-14.

Choncho, n’zoonekeratu kuti kusunga Sabata pakokha sikungathandize kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Mulungu. Ndiyeno kodi n’chiyani chimene chikufunika kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka? Yesu akutiitana tonse kuti: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mateyu 11:28) Kulambira kogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa n’kotsitsimutsadi. N’kopanda chinyengo komanso miyambo yambirimbiri yotopetsa.

Padziko lonse, Mboni za Yehova zimayesetsa kulambira Mulungu mogwirizana ndi mmene otsatira a Yesu oyambirira ankachitira. A Mboni amakumana mlungu uliwonse n’cholinga chophunzira Baibulo. Alibe tsiku lenileni lapadera limene amasonkhana. Iwo amasankha tsiku lina lililonse logwirizana ndi nthawi imene anthu ambiri amaiona kuti ndi yabwino kudera kwawoko, ndipo satsatira mwambo uliwonse wosagwirizana ndi Malemba posankha tsiku limeneli. Ngati mungakwanitse, mungachite bwino kupita ku malo awo olambirira kwanuko ndipo mungatsimikize nokha kuti kulambira kwawo n’kotsitsimutsadi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Baibulo likamagwiritsa ntchito mawu akuti “mpaka kalekale,” silitanthauza kwamuyaya, kapena kuti nthawi yosatha. Mawuwa amangotanthauza nthawi yaitali kwambiri, kapena nthawi imene sikudziwika bwinobwino kuti idzathera pati.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi muyenera kukhala ndi tsiku linalake lapadera lolambirira?​—Aroma 10:4; 14:5.

● Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusonkhana pamodzi kuti tizilambira Mulungu?​—Aheberi 10:24, 25.

● Kodi kulambira kovomerezeka kumakhala kotani?​—Mateyu 11:28.

[Tchati/Chithunzi pamasamba 10, 11]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

LACHIWIRI

LACHITATU

1 LACHINAYI

2 LACHISANU

3 LOWERUKA

4 LAMLUNGU