Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru

Muzigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru

Muzigwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru

NDALAMA zikhoza kugwiritsidwa ntchito m’njira zitatu zotsatirazi: (1) kugulira chinachake, (2) kuzisunga, kapena (3) kupatsa ena. Tiyeni choyamba tikambirane mmene mungagwiritsire ntchito ndalama mwanzeru.

Vuto la kusayenda bwino kwa chuma padziko lonse lathandiza anthu kuona kuti kukhala ndi bajeti n’kofunika kwambiri. Kodi bajeti ndi chiyani? Mwachidule tingati bajeti ndi kuoneratu mmene mudzagwiritsire ntchito ndalama zanu. Bajeti ikhoza kukhala ya munthu payekha, banja, kampani kapena boma.

Muzichitira Limodzi Bajeti

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupanga bajeti? Buku lina lolembedwa ndi Denise Chambers, linanena kuti: “Popanga bajeti pa banja panu, aliyense azikhalapo chifukwa zimenezi zimathandiza kuti aliyense aziyesetsa kutsatira bajetiyo.” Nthawi ndi nthawi, onse pa banjapo ayenera kukumana n’kuona ngati akutsatira bajetiyo kapena ayi. Kupanga bajeti n’kothandiza chifukwa aliyense amayesetsa kuti asawononge ndalama zambiri kuposa zimene banjalo limapeza.

Popanga bajeti, ena amagwiritsa ntchito pulogalamu ya pa kompyuta. Ena amalemba bajetiyo papepala limene amaligawa mbali ziwiri. Mbali imodzi amalembapo ndalama zimene amapeza ndipo mbali inayo amalembapo ndalama zimene amawononga. Popanga bajeti zimathandizanso kwambiri kuganizira ndalama zimene zimafunika kamodzi pachaka monga ndalama zolipira msonkho kapena ndalama zopitira kutchuthi.

Njira imene anthu akhala akuigwiritsa ntchito kwa zaka zambiri ndi yokhala ndi maenvulopu angapo kapena mafaelo olembedwa kuti “Zakudya,” “Lendi,” “Thilansipoti,” “Magetsi,” “Zolipilira Kuchipatala,” ndi zina zotero. Kale anthu ankaika ndalama zogwiritsira ntchito pa zinthu zimenezi m’maenvulopuwo. Koma masiku ano anthu ambiri amaona kuti ndi bwino kukaika ndalama kubanki, n’kumazitengako akafuna kulipirira zinthuzo.

Jonathan ndi mkazi wake Anne, omwe amakhala ku South Africa, komanso ana awo awiri aakazi, amakhala ndi faelo imene amalembamo bajeti yawo yonse. Jonathan ananena kuti: “Ngakhale ngati malipiro anu mumalandirira kubanki, muyenera kuonetsetsa kuti ndalama iliyonse imene mukutenga ndi yogwiritsiradi ntchito pa zinthu zimene munalemba pabajeti paja. Mwachitsanzo, ngati ndalama zogulira nyama zatha, musamatenge ndalama zimene munasunga n’cholinga choti mukagulire nyama ina.”

Poyamba Jonathan ankachita bizinezi koma panopa iye ndi banja lake amagwira ntchito yongodzipereka yomanga malo olambirira. Chifukwa chakuti akufuna kupitiriza kugwirabe ntchito yawo yodziperekayi, amapewa kuwononga ndalama mwachisawawa. Banjali limakumana nthawi ndi nthawi n’cholinga choti lione ngati pangafunike kusintha bajetiyo pena ndi pena.

Kupatsa Kumabweretsa Chimwemwe

Ofufuza ambiri apeza kuti munthu amene ali ndi mtima wopatsa amakhala wosangalala kwambiri. Mungagwiritse ntchito nthawi yanu, mphamvu zanu komanso ndalama zanu pochitira ena zinthu zabwino. Pa njira zitatu zimene zatchulidwa kumayambiriro kwa nkhaniyi, kuthandiza ena kukhoza kukhala njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito ndalama zanu.

Chris Farrell analemba m’buku lake kuti: “Kusunga ndalama kumathandiza kuti tizitha kuthandiza anthu ena. Ndipotu chinthu chofunika kwambiri komanso chanzeru chimene mungachite ndi ndalama zanu ndi kuthandizira ena.” * Farrell ananenanso kuti: “Mutati muganize mozama, mupeza kuti kuthandiza ena, osati kukhala ndi ndalama kapena katundu wambiri, n’kumene kumachititsa kuti muzicheza bwino ndi anthu, muzimva bwino mumtima, komanso muziona kuti mukuchita zinthu zinazake zofunika kwambiri.”—The New Frugality.

Katswiri wina wa zachuma, dzina lake Michael Wagner, ananena kuti mfundo imeneyi ndi yabwino kuitsatira. Polimbikitsa achinyamata kuti aphunzire kusunga ndalama, iye analemba m’buku lake kuti: “Munthu ukachitira ena zabwino, anthu enanso amakuchitira zabwino zambirimbiri, komanso chosangalatsa n’chakuti umamva bwino kwambiri mumtima.”

Baibulo limanena kuti kupatsa kumabweretsa chimwemwe. Monga mmene tafotokozera kale, m’Baibulo muli mfundo zimene zingakuthandizeni kugwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. Tiyeni tione mfundo zina 7 zothandiza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Mungagwiritse ntchito ndalama zanu pogulira ena mphatso, kapena pocherezera alendo. Mwachitsanzo, mungagule zakudya zoti muphikire achibale anu komanso anzanu.