Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mulembereni Kalata Anton”

“Mulembereni Kalata Anton”

“Mulembereni Kalata Anton”

● M’mudzi wa Schelkan mumzinda wa Stavropol’ Kray ku Russia, munali mnyamata wina wa Mboni za Yehova, dzina lake Anton. Iye ali mwana anapezeka ndi matenda enaake osachiritsika amene amachititsa munthu kuti azingowonda (Duchenne muscular dystrophy). Anthu ambiri odwala matendawa amamwalira asanafike zaka 20. Pamene Anton ankakwanitsa zaka 9, n’kuti akulephereratu kuyenda.

Munthu wina dzina lake Yevgeny limodzi ndi mkazi wake Diana, anakumana ndi Anton atapita kukachezera mpingo winawake wa Mboni za Yehova. Diana anafotokoza kuti: “Anton ankaoneka wofooka kwambiri komabe anali wamphamvu mwauzimu. Chifukwa chakuti mkulu wake anamwalira ndi matenda omwewa ali ndi zaka 19, Anton ankadziwa kuti nayenso sakhala nthawi yaitali ali ndi moyo. Komabe iye anali munthu wosangalala ndipo sankada nkhawa kwambiri chifukwa cha matenda akewa.”

Diana ndi mwamuna wake analimbikitsa Anton kuti akhoza kukwanitsa kumalalikira anthu ambiri akumidzi yakutali powalembera makalata. M’chaka cha 2005, makalata amene Anton analemba n’kuwatumiza kumidziyo anakwana pafupifupi 500. Koma iye anakhumudwa chifukwa palibe aliyense amene anamuyankha. Ngakhale zinali choncho, iye sanafooke. Anapitirizabe kulemba makalata komanso kupemphera ndi mtima wonse kuti Mulungu amuthandize kuti utumiki wake uziyenda bwino.

Tsiku lina Anton akuwerenga nyuzipepala, anaona kalata imene mayi winawake analemba. Mayiyo ankadwala kwambiri ndipo ankafuna kulimbikitsidwa. Anton anamulembera mayiyo kalata, yomwenso inadzatuluka m’nyuzipepala yomweyo. Mawu ena a m’kalatayo anali akuti: “Ngakhale kuti ndikudwala matenda osachiritsika, kuwerenga Baibulo kumandithandiza kuti ndizikhala ndi chiyembekezo. Ndimasangalala kwambiri anthu akamayankha makalata anga.”

Mayiyo anakhudzidwa kwambiri ndi kalatayo ndipo anayankha kalata imene Anton anamulemberayo. Kalata yake inatulukanso m’nyuzipepala yomweyo ndipo mutu wa kalatayo unali wakuti, “Mulembereni Kalata Anton.” Mayiyo anayamikira kwambiri mfundo za m’Baibulo zimene Anton analemba ndipo kenako ananena kuti: “Tiyeni timuthandize Anton. Tizimuyankha makalata ake. Mnyamata ameneyu akufunikira kwambiri kuuzidwa mawu olimbikitsa.” Adiresi ya Anton inalembedwa m’nyuzipepalayo kuti aliyense amene akufuna amulembere kalata.

Pasanapite nthawi yaitali, positi ofesi ya m’mudzi mwawo inayamba kulandira makalata ambirimbiri. Pankafika makalata opita kwa Anton pafupifupi 30 tsiku lililonse. Makalatawo ankachokera ku Russia, komanso ku Germany, France ndi kumayiko a kufupi ndi nyanja ya Baltic. Iye analandira makalata ambirimbiri kuchokera kwa anthu amene ankakonda kuwerenga nyuzipepala ija. Diana ananena kuti: “Anton anali wosangalala kwambiri chifukwa anapeza anthu ambiri olemberana nawo makalata, amene ankawauza mfundo za m’Baibulo.”

Kwa nthawi yoposa chaka chimodzi, Anton ankalemberana makalata ndi anthu osiyanasiyana n’kumawauza mfundo za m’Baibulo. Koma kenako manja ake anafooka kwambiri chifukwa cha matenda ake, moti sankathanso kulemba. Choncho akafuna kulemba kalata ankapempha munthu wina kuti amulembere zimene iye akufuna. Koma n’zomvetsa chisoni kuti Anton anamwalira mu September 2008, ali ndi zaka 20. Ngakhale kuti matenda ake ankachititsa kuti azikhala wofooka, Anton anali ndi chikhulupiriro champhamvu. Iye ankakonda kulalikira, ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wa m’Baibulo.