Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

MULUNGU sanalenge anthu kuti azifa. (Aroma 8:20, 21) Ndipotu pamene Mulungu ankamuuza Adamu za imfa, sananene kuti anthu ayenera kumafa, koma anati ngati anthu atachimwa chilango chake chidzakhala imfa. (Genesis 2:17) Adamu anamvetsa tanthauzo la imfa chifukwa ankaona nyama zikufa.

Koma Adamu anachimwa ndipo anafadi, ali ndi zaka 930. (Genesis 5:5; Aroma 6:23) Choncho anachotsedwa m’banja la Mulungu chifukwa cha kusamvera kwake, ndipo sanalinso mwana wa Mulungu. (Deuteronomo 32:5) Ponena za zotsatirapo zoipa za uchimo, Baibulo limati: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse.”—Aroma 5:12.

Kodi Wakufa Amaganiza?

Baibulo limati: “Chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera n’chimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. Onse apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.” (Mlaliki 3:19, 20) Kodi mawu akuti kubwerera kufumbi akutanthauza chiyani?

Mawuwa akuchokera pa zimene Mulungu anauza munthu woyambirira uja, zakuti: “Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Zimenezi zikutanthauza kuti matupi a zinyama ndiponso a anthu n’ngofanana. Ndipotu munthu si mzimu umene anthu ena amati umakhala m’kati mwa thupi. Choncho munthu akamwalira saganiza china chilichonse. Baibulo limati munthu akamwalira zimachitika ndi izi: “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:4.

Ngati zili choncho, nangano n’chiyani chimene chimachitika kwa anthu akufa? Mawu a Mulungu amayankha momveka bwino kuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Imfa si mnzathu amene angatitenge n’kutipititsa ku moyo wabwino, m’malo mwake Baibulo limati imfa ndi “mdani womalizira,” chifukwa tikamwalira sitingathe kuchita china chilichonse. (1 Akorinto 15:26; Mlaliki 9:10) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe chiyembekezo chilichonse kwa anthu akufa?

Nkhani Yolimbikitsa

Kwa anthu ambiri, imfa ili ngati tulo. Nthawi inayake Yesu anauza ophunzira ake kuti mnzake amene anali atamwalira ali mtulo. Iye anati: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukam’dzutsa ku tulo take.” Ndiyeno ali panjira yopita kumanda, Yesuyo anakumana ndi anthu olira malirowo. Ndipo Yesu atafika kumandako, anauza anthuwo kuti atsegule mandawo, ndipo anaitana mofuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Lazaroyo anatuluka ngakhale kuti anali atatha masiku anayi ali m’manda. (Yohane 11:11-14, 39, 43, 44) Zimene Yesu anachita poukitsa Lazaro, zimasonyeza kuti Mulungu sangaiwale chinthu chilichonse chokhudza munthu amene wafa, kaya umunthu wake, maganizo ake, kapenanso maonekedwe ake. Motero, sangalephere kuukitsa munthu. Panthawi inayake, Yesu anatinso: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

Baibulo limatiuzanso nkhani ina yosangalatsa yakuti: “Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Panthawi imeneyo, anthu sadzakhalanso achisoni n’kumapita kumanda kukaika anthu. Baibulo limati: “Ndipo imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Inde, zimene Baibulo limanena pankhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira n’zolimbikitsa kwambiri.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi anthu akufa amadziwa kanthu?—Mlaliki 9:5.

▪ Kodi pali chiyembekezo kwa anthu akufa?—Yohane 5:28, 29.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:4