Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tetezani Ana M’Banja Lanu

Tetezani Ana M’Banja Lanu

Tetezani Ana M’Banja Lanu

“OPANDA chikondi chachibadwa.” Baibulo limanena zimenezi pofotokoza mmene anthu ambiri alili “m’masiku otsiriza” ano. (2 Timoteyo 3:1, 3, 4) Kufala kwa vuto la kuchita chipongwe ana panyumba kukutsimikizira kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa. Kwenikweni, mawu a Chigiriki akuti asʹ-tor-gos, omwe m’Chichewa amati “opanda chikondi chachibadwa,” amasonyeza kusowa chikondi chimene chimayenera kukhalapo pakati pa achibale, makamaka pakati pa makolo ndi ana awo. * Ndipotu nthawi zambiri achibale ndi amene amachita ana zachipongwe zotere.

Ofufuza ena amati anthu ambiri amene amakonda kuchita ana zachipongwe amakhala bambo a anawo kapena mwamuna amene ali ndi udindo wa bambo pabanjapo. Komanso amuna ambiri amene ali achibale ndi amene amatha kum’chita mwanayo zachipongwe. Ambiri mwa ana amene amachitidwa zachipongwe ndi atsikana, koma zimenezi zimachitikanso ngakhale kwa anyamata ambiri. Ndipotu pali akazi ambiri amene amachita zachipongwe zoterezi tianyamata. Palinso ana ambiri amene amachitidwa zachipongwe ndi ana anzawo pakhomopo koma n’kutheka kuti sanena ayi. Mwina amachitidwa zachipongwezi ndi mkulu wawo kapena m’bale wawo wina yemwe amawapezerera. Kaya iyeyo ndi wamkazi kapena wamwamuna, angakakamize mlongo wake wamng’onoyo kuchita naye zopusa. N’zoona kuti zimenezi zingakunyanseni kwambiri monga makolo.

Kodi mungatani kuti mavuto ngati amenewa asachitike m’banja mwanu? N’zoonekeratu kuti aliyense m’banjamo ayenera kudziwa bwino mfundo zosiyanasiyana zoteteza ana kuti asachitidwe zachipongwe. Komanso aliyense azidziwa kufunika kwa mfundo zimenezi. Mfundo zothandiza kwambiri pankhani imeneyi zimapezeka m’Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo.

Zimene Mawu a Mulungu Amanena pa Nkhani ya Kugonana

Kuti ana akhale otetezeka m’banja lanu, m’pofunika kuti anthu onse m’banjamo azitsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Baibulo limanena mosapita m’mbali za nkhani ya kugonana. Limanena nkhaniyi mwaulemu, koma mosapsatira mawu. Limafotokoza kuti Mulungu anakonza zoti mwamuna ndi mkazi omwe anakwatirana ndiwo ayenera kugonana ndipo limati amenewa ndi madalitso. (Miyambo 5:15-20) Koma limaletsa kugonana popanda kukwatirana. Mwachitsanzo, Baibulo limaletseratu kugonana pachibale. Mu Levitiko chaputala 18, analembamo zinthu zosiyanasiyana zomwe Baibulo limaletsa zokhudza kugonana ndi wachibale. Taonani mawu awa: “Asasendere mmodzi wa inu kwa m’bale wake kum’vula [kapena kuti kugona naye]; ine ndine Yehova.”—Levitiko 18:6.

Yehova anaika khalidwe la kugonana ndi wachibale m’gulu la ‘zinthu zonyansa’ zimene chilango chake chinali imfa. (Levitiko 18:26, 29) N’zoonekeratu kuti Mlengi wathu ali ndi mfundo zapamwamba kwambiri pankhani imeneyi. Maboma ambiri masiku ano, amaona nkhaniyi chimodzimodzi ndipo akhazikitsa malamulo oletsa khalidweli. Malamulo a mayiko ambiri amati mwana akagonedwa ndi munthu wamkulu ndiye kuti wagwiriridwa. N’chifukwa chiyani amanena choncho ngakhale pamene mwanayo sanachite kum’kakamiza?

Maboma ambiri ayamba kuzindikira kuti zimene Baibulo linanena kalekale zokhudza ana n’zoona. Baibulo limati ana nthawi zambiri satha kuganiza ngati akuluakulu. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 22:15, limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” Ndipo mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali . . . kuganiza ngati kamwana, kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.”—1 Akorinto 13:11.

Zinthu zokhudza kugonana n’zoti mwana sangazimvetse, ndipo sangadziwe mmene kugonana kungakhudzire tsogolo lake. Motero, anthu ambiri amavomereza kuti, poti nzeru za mwana n’zopewera, n’zosamveka kunena kuti mwana angavomerezedi mwakufuna kwake kugonana ndi munthu winawake wamkulu. Kapena tinene kuti, munthu wamkulu, kapena mwana wina wosinkhukirapo, akagonana ndi mwana wamng’ono, sanganamizire kuti anachita zimenezi chifukwa choti mwanayo sanakane kapena kuti anafuna yekha. Mfundo imakhala yakuti mwanayo wachita kum’gwiririra basi. Nthawi zambiri chilango cha mlandu woterewu n’kutsekeredwa kundende. Pamenepa ndiye kuti munthu wamkuluyo ndiye ali ndi mlandu wogwiririra mwana wosalakwayo.

Komano n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri okhala ndi milandu yotereyi salangidwa n’komwe masiku ano. Mwachitsanzo, ku Australia akuti mwina ndi anthu 10 okha pa anthu 100 aliwonse ogona ana amene amaimbidwa mlandu, ndipo ndi ochepa chabe amene amalangidwa. M’mayiko enanso n’chimodzimodzi. Mabanja achikhristu sangadalire boma lokha kuti ndilo liziteteza ana awo, motero amagwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo chifukwa ndizo zili zothandiza kwambiri.

Akhristu oona amazindikira kuti Mulungu yemwe anachititsa kuti mfundo zimenezi zilembedwe m’Mawu ake sanasinthe ayi. Iyeyu amaona chilichonse chimene timachita, ngakhale zinthu zimene anthu ambiri sangathe kuziona. Baibulo limati: “Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.”—Aheberi 4:13.

Tizidziwa kuti Mulungu amationa tikamaphwanya malamulo ake ndi kuchita zinthu zoipa kwa anzathu. Komanso, iye amatidalitsa tikamayesetsa kutsatira malamulo ake opindulitsa banja. Kodi ena mwa malamulo amenewa ndi ati?

Banja Lizikhala Logwirizana ndi Lachikondi

Baibulo limati chikondi ndi “chomangira umodzi changwiro.” (Akolose 3:14) Baibulo limafotokoza kuti chikondi si kudololedwa kokha ayi. Limati chikondi chimaonekera pa zinthu zimene munthu akuchita, kapena kuti khalidwe limene akusonyeza ndiponso zinthu zimene amadziletsa kuchita. (1 Akorinto 13:4-8) Kusonyezana chikondi m’banja kumatanthauza kulemekeza aliyense m’banjamo ndi kum’chitira zinthu mokoma mtima. Kumatanthauzanso kuti m’banjamo aliyense aziona mnzake mogwirizana ndi mmene Mulungu amamuonera. Mulungu anapatsa munthu aliyense m’banja udindo wofunikira.

Poti bambo ndiye mutu wa banja, iye ayenera kukhala patsogolo posonyeza chikondi. Iye amadziwa kuti kukhala bambo wachikhristu si chilolezo chochitira nkhanza mkazi kapena ana ake. M’malo mwake, iye amasonyeza umutu wake motsanzira Khristu. (Aefeso 5:23, 25) Motero iye amasamalira mkazi wake ndi kum’konda ndipo amaleza mtima ndi ana ake n’kumawakondanso kwambiri. Amawateteza nthawi zonse ndipo amayesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti anawo asaone zoopsa zilizonse, zomwe zingawasokoneze maganizo n’kuwachititsa kuti asamakhulupirire anthu ndiponso kuti azikhala mwamantha.

Mayi nayenso ali ndi udindo wosangalatsa ndiponso wolemekezeka. Pofotokoza mmene Yehova ndi Yesu amatetezera anthu, Baibulo limapereka chitsanzo cha mmene nyama zazikazi zimagwiritsira ntchito nzeru zachibadwa poteteza ana awo. (Mateyo 23:37) Choncho, nawonso amayi ayenera kuchita khama poteteza ana awo. Mwachikondi, mayi amaonetsetsa kuti ana ake akuwateteza kwambiri. Mayi kapena bambo sayenera kuchitirana nkhanza, kuzunzana, kuopsezana kapena kuchita zinthu zoterezi kwa ana awo. Komanso asamalole kuti ana awo azichita zimenezi kwa ana anzawo.

Munthu aliyense m’banjamo akamalemekeza anzake sizivuta kukambirana zinthu momasuka. Wolemba mabuku wina dzina lake William Prendergast anati: “Tsiku lililonse, makolo ayenera kukambirana zakukhosi ndi ana awo aang’ono kapenanso osinkhukirapo.” Iye anatinso: “Zikuoneka kuti imeneyi ndi njira yothandiza kwambiri pothetsa vuto la kugona ana.” Ndipotu izi n’zimene Baibulo limalimbikitsa. (Deuteronomo 6:6, 7) Mukamatsatira malangizo amenewa, aliyense panyumba panu amakhala womasuka kulankhula zakukhosi kwake, popanda kuopa chilichonse.

N’zoona kuti tikukhala m’dziko loipa ndipo n’zosatheka kuthandiza ana onse kuti asachitidwe zachipongwe. Komabe, kuika chitetezo chokwanira panyumba panu kungathandize kwambiri. Ndipo ngati winawake m’banjamo wachitidwa zachipongwe ndi anthu ena osakhala a m’banjamo, amadziwa kopita kuti akalimbikitsidwe. Pakhomo pakakhala potero, ana amakhala otetezekadi ngakhale kuti tikukhala m’dziko loipa. Yesetsani kuchita khama kuteteza ana pakhomo panu ndipo Mulungu adzakudalitsani.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mabuku ena amamasulira mawu a Chigiriki chakalewa motere: “Kuumira mtima achibale.” Motero, Baibulo lina linamasulira vesi imeneyi motere: “Adzakhala . . . osowa chikondi cha pa abale awo.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

NJIRA ZINA ZOTETEZERA ANA ANU PANYUMBA

Intaneti: Ngati ana anu amagwiritsa ntchito Intaneti, muyenera kuwaphunzitsa bwinobwino mmene angaigwiritsire ntchito mosamala. Pa Intaneti pali malo ambirimbiri okhala ndi zinthu zolaula, ndiponso malo amene anthu amatumiziranapo mauthenga. Zidyamakanda zimapezerapo mwayi pa malo oterewa n’kumatumiza mauthenga awo kuti zikope ndi kunyengerera tiana. Motero, n’chinthu chanzeru kuika kompyuta pamalo oonekera, kuti makolo azitha kuona bwinobwino zimene ana akuchita pa Intanetipo. Popanda kuyang’aniridwa ndi makolo, ana asamatumize zinthu monga adiresi yawo kapena nambala yawo ya foni kwa munthu aliyense amene amudziwira pa Intaneti.—Salmo 26:4.

Zakumwa Zoledzeretsa: Nthawi zambiri ana amene amachitidwa chipongwe ndi anthu ogona ana, amakhala kuti anamwetsedwa mowa. Odziwa bwino za nkhani ya kugona ana amati anthu amene amamwa kwambiri zakumwa zoledzeretsa nthawi zambiri satha kudziletsa; moti ena amachita zinthu zimene sangachite atakhala bwinobwino. Mulimonsemo, zimenezi zikuthandiza kuona ubwino wotsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizipewa kuledzera ndi kumwa mosadziletsa.—Miyambo 20:1; 23:20, 31-33; 1 Petulo 4:3.

Apatseni Ulemu: Mayi wina amakumbukira kuti: “Mayi anga atamwalira, ndi bambo anga okha amene chipinda chawo chinali ndi chitseko ndiponso makatani. Ena tonsefe tinalibe malo aliwonse okhala mobisika, ngakhale kubafa.” Bambo amene akunenedwayu ankawagona ana ake onse aakazi. Ngakhale achibale ayenera kudziwa kuti kupatsa ana ulemu n’kofunika kwambiri. Makolo amafuna kupatsidwa ulemu kuti azitha kuchita zinthu zina pa malo obisika. Ananso amafunanso kuti makolo aziwapatsa ulemu wotere akamakula. Makolo anzeru amachitira ena zinthu zimene amafuna kuti enawo aziwachitiranso iwowo.—Mateyo 7:12.