Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

ANANENA IZI NDANI?

Lembani mzere kuchokera pa mawuwo kufika pa munthu amene anawanena.

Mose

Petulo

Yohane

Adamu

1. “Ana apamtima inu, pewani mafano.”

2. “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga.”

3. “Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula.”

4. “Kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.”

Kambiranani: Kodi mukudziwapo chinthu chinanso chiti chokhudza aliyense mwa anthu a m’Baibulo amenewa?

ZINACHITIKA LITI?

Tchulani anthu amene analemba mabuku a m’Baibulo amene ali m’munsiwa, ndipo lembani mzere wolumikiza buku ndi nthawi imene anamaliza kulilemba.

1450 B.C.E. 844 B.C.E. 536 B.C.E. 56 C.E. 61 C.E.

5. Danieli

6. Yona

7. Aheberi

NDINE NDANI?

8. Mawondo anga ananjenjemera chifukwa cha chozizwitsa chimene chinachitika.

NDINE NDANI?

9. Ndinathawa mbuye wanga koma ndinabwerera kwa iye nditakhala Mkhristu.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunso awa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

Tsamba 5 Kodi wachibwana amatani? (Miyambo 14:․․․)

Tsamba 11 Kodi ndi khalidwe liti limene lili chomangira umodzi changwiro? (Akolose 3:․․․)

Tsamba 19 Kodi tonsefe timatani nthawi zambiri? (Yakobe 3:․․․)

Tsamba 28 Kodi imfa inafalikira motani kwa anthu onse? (Aroma 5:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 14)

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Yohane.—1 Yohane 5:21.

2. Adamu.—Genesis 2:23.

3. Petulo.—1 Petulo 5:8.

4. Mose.—Salmo 90:2.

5. Danieli, 536 B.C.E.

6. Yona, 844 B.C.E.

7. Paulo, 61 C.E.

8. Belisazara.—Danieli 5:1, 5, 6.

9. Onesimo.—Filemoni 10-16.