Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinalengedwa Kuti Tiziphunzira Mpaka Kalekale

Tinalengedwa Kuti Tiziphunzira Mpaka Kalekale

Tinalengedwa Kuti Tiziphunzira Mpaka Kalekale

“M’mutu wa munthu aliyense muli chiwalo chaching’ono koma champhamvu zedi ndipo chimagwira ntchito bwino kwambiri. Timati tikaphunzira zambiri zokhudza chiwalo chimenechi timapeza kuti mphamvu yake ilibe malire.”—ANATERO TONY BUZAN NDI TERENCE DIXON, ALEMBI ASAYANSI.

KODI ubongo wa munthu ungaphunzire zinthu zochuluka bwanji? Funso limeneli likupitirizabe kuchititsa chidwi ndi kuzunguza mitu anthu ochita kafukufuku. M’buku lotchedwa The Brain Book, Peter Russell analemba kuti: “Tikaphunzira zambiri za ubongo wa munthu m’pamene timapeza kuti uli ndi mphamvu kwambiri ndipo ungathe kuchita zinthu zambiri kuposa mmene tinkaganizira m’mbuyo monsemu.”

Mwachitsanzo, ubongo uli ndi mphamvu yaikulu kwambiri yokumbukira zinthu. Russel anati: “Mphamvu yokumbukira zinthu sili ngati chidebe chimene chimadzaza pakapita nthaŵi, koma ili ngati mtengo umene susiya kuphukira nthambi pamene mumakolowekapo zimene mukukumbukirazo. Chilichonse chimene mumakumbukira chili ngati nthambi zina zoti mungakolowekepo zinthu zina zatsopano zofunika kuzikumbukira. Choncho mphamvu yokumbukira zinthu imangokulirakulirabe. Ngati mukudziŵa zinthu zambiri, m’pamenenso mungathe kudziŵa zinthu zina zatsopano zambiri.” Zimenezi zikutifikitsa pa funso tinafunsa kale lija, loti N’chifukwa chiyani ubongo wa munthu uli ndi mphamvu zazikulu choncho zomwe sizigwiritsidwa ntchito?

Chiphunzitso chakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina sichitipatsa yankho lililonse logwira mtima. Chifukwa chiphunzitsochi chimadalira kwambiri mfundo yoti zamoyo zamphamvu n’zokhazo zimapulumuka, anthu oganiza bwino amazunguzika mitu chifukwa samvetsa chimene chinachititsa ubongo wa munthu kukhala ndi mphamvu zambiri choncho. Mwachitsanzo, kodi munthu angapangirenji lole yaikulu pamene akufuna kunyamula mchenga wodzaza fosholo imodzi yokha?

Koma Baibulo limatipatsa yankho lophweka komanso lomveka bwino kwambiri. Choyamba, limatiuza kuti makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo anapangidwa kuti azitha kusonyeza makhalidwe ochititsa chidwi a Mulungu. Chachiŵiri, limatiuza kuti anthuwo analengedwa kuti akhale ndi moyo kosatha, kutanthauza kuti analengedwa kuti aziphunzira mpaka kalekale. (Genesis 1:27; 2:16, 17) Ubongo wa munthu umasonyeza cholinga cha Mulungu chimenecho, ngakhale kuti panopa umachita zimenezo mopanda ungwiro chifukwa cha kubwera kwa uchimo m’banja la anthu.—Aroma 5:12.

Ngakhale zili choncho, cholinga cha Mulungu choyambirira choti dziko lapansi lidzazidwe ndi anthu angwiro oopa Mulungu okhala m’Paradaiso chidzakwaniritsidwa. Indedi, Yehova anatipatsa Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu, monga nsembe ya dipo kuti tikhale ndi moyo wosatha.—Mateyu 20:28; Yohane 3:16.

Chakudya Chabwino Kwambiri cha Maganizo Athu

Yehova anatipatsanso Mawu ake ouziridwa, Baibulo Lopatulika. (2 Timoteo 3:16; 2 Petro 1:21) Chifukwa chakuti buku lamtengo wapatali limeneli linalembedwa mwa mphamvu ya mzimu woyera, si kukokomeza kunena kuti lili ndi chakudya chabwino kwambiri cha anthu cha maganizo ndi chauzimu. (Salmo 19:7-10) Indedi, Yesu mwiniwakeyo ananena kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”—Mateyu 4:4.

Choncho, kaya ndinu wachinyamata kapena wachikulire, bwanji osapatulako nthaŵi yochepa tsiku lililonse kuŵerenga ‘mawu’ a Mulungu amtengo wapatali? Anthu amene amachita zimenezi ndipo amagwiritsa ntchito zimene amaphunzirazo amapindula panopa ndiponso adzapindula m’tsogolo. Zoonadi, angakhale ndi mwayi wokhala ndi moyo kosatha ndi kuphunzira mpaka kalekale, monga mmene Mulungu anafunira pachiyambi. Umenewo ndi mwayidi wapadera kwambiri!—Mlaliki 3:11; Yohane 17:3.

[Chithunzi patsamba 27]

Posonyeza cholinga cha Mulungu, ubongo wa munthu unalengedwa kuti uziphunzira mpaka kalekale

[Zithunzi patsamba 28]

Baibulo lili ndi chakudya chabwino kwambiri cha maganizo anu