Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuba Mwachinyengo ndi Vuto Lapadziko Lonse

Kuba Mwachinyengo ndi Vuto Lapadziko Lonse

Kuba Mwachinyengo ndi Vuto Lapadziko Lonse

WAYNE anali wodziŵa kulankhula mokopa anthu ndiponso mwachifatse ndipo anali ndi makhalidwe onse amene Karen ankafuna kuti mwamuna amene adzakwatiwe naye adzakhale nawo. “Anali ndendende munthu amene ndinkapempherera ndi kufunafuna,” anatero Karen. “Aliyense akationa ankati tinali oyenererana kwabasi. Wayne ankachita zinthu zosonyeza kuti anali kundikonda mapeto.”

Koma panali vuto limodzi. Wayne anauza Karen kuti anali wachitatu kwa mkulu wa bungwe laboma lochita kafukufuku wachinsinsi lotchedwa Australian Secret Intelligence Organization. Amafuna kuisiya ntchitoyo, koma ankamukaniza chifukwa ankadziŵa zinsinsi zambiri. Anamuuza kuti akasiya ntchitoyo amupha! Choncho Wayne ndi Karen anagwirizana zochita. Anagwirizana zoti adzakwatirana, adzaphatikiza pamodzi katundu ndi chuma chawo chonse, kenaka n’kuchoka ku Australia kuthaŵira ku Canada. Karen anagulitsa nyumba yake ndi katundu wake yense n’kupereka ndalamazo kwa Wayne.

Ukwatiwo unachitika monga momwe anakonzera. Wayne anathaŵa m’dzikomo, koma anamusiya Karen m’mbuyo, atangotsala ndi ndalama zokwana madola sikisi okha basi kubanki. Karen anadzazindikira kuti ananamizidwa mabodza ambirimbiri amene cholinga chake chinali chofuna kumubera basi. Wayne ananamizira kukhala munthu wabwino n’cholinga chofuna kumukopa. Mbiri yake, zokonda zake, khalidwe lake, ndiponso zoti amamukonda Karen, zonsezo zinali mabodza amene cholinga chake chinali choti Karen ayambe kumukhulupirira, ndipo chikhulupiriro chimenecho chinamutayitsa ndalama zopitira madola 200,000. Wapolisi wina anati: “Anamuchitira zinthu zankhanza kwambiri. Ndalamazo zili apo, n’zovuta kumvetsa kuti munthu angachitire mnzake zinthu zoipa chonchi.”

Karen anati: “Maganizo anga asokonezekeratu. Ankanamizira kukhala munthu wabwino, pamene sanali wotero n’komwe.”

Karen ndi munthu mmodzi yekha mwa anthu ambirimbiri amene amaberedwa mwachinyengo padziko lonse lapansi. Sizikudziŵika kuti anthu amaberedwa ndalama zingati mwachinyengo, koma ena akuti mwina zimakwana madola mabiliyoni ambirimbiri ndipo zikuchulukirachulukira chaka chilichonse. Kuwonjezera pa kuberedwa ndalama, anthu ngati Karen amapwetekedwa kwambiri mu mtima pozindikira kuti munthu wina, amene anali kumukhulupirira kwambiri, anachita zinthu zowapezerera.

Ndi Bwino Kwambiri Kudziteteza

Kuba mwachinyengo akuti ndi “kunyenga dala munthu wina n’cholinga chopeza ndalama ponamizira kukhala munthu wina, kunena mabodza, kapena kulonjeza zinthu zabodza.” N’zomvetsa chisoni kuti anthu oba mwachinyengo kaŵirikaŵiri salangidwa chifukwa choti nthaŵi zambiri zimakhala zovuta kupereka umboni wosonyeza kuti munthuyo anachitadi chinyengo mwadala. Kuwonjezera apo, anthu ambiri oba mwachinyengo amadziŵa malamulo amene angatheke kuwazemba ndipo amapezerapo mpata pa malamulo ameneŵa, kutanthauza kuti amadziŵa mmene angabere anthu mwachinyengo m’njira yoti zikhale zovuta kapena zosatheka kumene kuwapeza ndi mlandu. Komanso, kuimba mlandu munthu woba mwachinyengo kumafuna nthaŵi yambiri ndiponso ndalama zambiri. Nthaŵi zambiri anthu amene amapezedwa olakwa ndi anthu amene aba ndalama mamiliyoni ambiri kapena amene achita zinthu zazikulu kwambiri zoti anthu ambiri azidziŵa. Ngakhale wakubayo akagwidwa n’kulangidwa, mwina amakhala atawononga kale kapena kubisa ndalamazo. Choncho anthu oberedwa nthaŵi zambiri salandira chipukuta misozi chilichonse.

Choncho ngati akuberani mwachinyengo, ndiye kuti mwina palibe chimene mungachitepo. Ndi bwino kupeŵa kuberedwa mwachinyengo kusiyana n’kuyesayesa kupeza njira yoti akubwezereni ndalama zimene akuberanizo. Munthu wina wanzeru analemba kalekale kuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene mungadzitetezere kwa anthu oba mwachinyengo.