Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Msamariya Wachifundo Wamakono

Msamariya Wachifundo Wamakono

Msamariya Wachifundo Wamakono

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU MEXICO

Ambiri a ife tinamvapo nkhani ya m’Baibulo ya mwamuna wokonda mnansi wake amene nthaŵi zambiri amatchedwa Msamariya Wachifundo. (Luka 10:​29-37) Mu fanizo limeneli, Yesu Kristu anasonyeza zinthu zambiri zimene mwamuna wina wachisamariya anachita posonyeza chikondi kwa mnansi wake atavutika. Kodi Asamariya achifundo oterowo alipo masiku ano? Taonani nkhani yotsatirayi yochokera ku Mexico.

Betuel ndi banja lake anali kubwerera kunyumba kuchokera ku ulendo ndipo atatsala pang’ono kufika anaona ngozi yoopsa zedi itachitika pamsewu. Anaima kuti athandizepo. Dalaivala mmodzi amene anachita nawo ngoziyo, amene anali dokotala, anawapempha kuti atengere mkazi wake, amene anali woyembekezera, ndi ana awo aakazi aŵiri ku chipatala chapafupi. Iwo anachita zimenezi, ndipo kenaka Betuel anabwereranso pamene panachitika ngozi paja kuti aone ngati panalinso zina zoti angathandizepo.

Betuel akufotokoza kuti: “Apolisi anali atafika, ndipo anati amutenga dokotalayo kuti akamufunse mafunso chifukwa pangoziyo panafa munthu. Dokotalayo atandifunsa kuti n’chifukwa chiyani ndimamuthandiza, ndinafotokoza kuti ndife Mboni za Yehova ndipo tinaphunzira m’Baibulo kuti tiyenera kukonda anansi athu. Ndinamuuza kuti asadandaule za mkazi wake ndi ana ake, chifukwa tiasamalira. Atalengeza misozi m’maso mwake chifukwa choyamikira, anandipatsa katundu wake wofunika kuti ndimusungire.”

Betuel ndi banja lake anatengera banja la mwamunayo kunyumba kwawo ndipo analisamalira kwa masiku angapo. Betuel anagwiritsa ntchito mwayi umenewo kuyamba nawo phunziro la Baibulo. Dokotalayo atamasulidwa, ananena kuti anathokoza ndi kusirira kwambiri Mboni za Yehova. Analonjeza kuti adzapitiriza kuphunzira Baibulo akafika kwawo, ndiponso kuti ngati mkazi wake adzabereke mwana wamwamuna, adzamutcha dzina loti Betuel. Betuel akupitiriza kuti: “Tsopano, patatha zaka ziŵiri, tinali ndi mwayi wokawachezera. Ndinadabwa kupeza kuti akuphunzira Baibulo, ndipo kamwana kawo kakamuna dzina lake ndi Betuel!”

[Chithunzi patsamba 15]

Betuel