Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutha Kupeza Thandizo

Mutha Kupeza Thandizo

Mutha Kupeza Thandizo

‘M’KAPU muli mapilitsi 49 ogonetsa. Kodi ndiwamwe kapena ndisawamwe?’ mwamuna wina wazaka 28 anadzifunsa choncho ku Switzerland. Mkazi ndi ana ake anali atam’thaŵa, ndipo maganizo anayamba kum’soŵetsa mtendere. Koma atamwa mapilitsiwo analankhula yekha kuti: ‘Sindikufuna kufa ayi!’ Mwamwayi wake, anapulumuka n’kudzafotokoza yekha nkhaniyo. Si kuti nthaŵi zonse maganizo ofuna kudzipha amaphetsa munthu.

Alex Crosby, yemwe ali m’bungwe la U.S. Centers for Disease Control and Prevention ananenapo pa nkhani ya kufuna kudzipha kwa achinyamata kuti: “Ngati mutawasokoneza ngakhale kwa maola ochepa chabe pamene akufuna kudzipha, sangadziphenso. Mungathe kulepheretsa anthu ambiri kudzipha mwakuwasokoneza. Zimenezo zingawapulumutse.”

Pogwira ntchito yake pa chipatala choona zogwa mwadzidzidzi chotchedwa Lifesaving and Emergency Center pa koleji ya zamankhwala ku Japan, pulofesa Hisashi Kurosawa anathandiza anthu ambiri ofuna kudzipha kuti ayambenso kuufuna moyo. Inde, powasokoneza maganizo awo ofuna kudzipha m’njira inayake, mutha kuwapulumutsa kuti asafe. Kodi mungawathandize motani?

Mufunika Kudziŵa Mavuto Amene Abweretsa Maganizowo

Monga taonera m’nkhani yangothayi, ofufuza akuti anthu 90 mwa anthu 100 alionse amene anadzipha anali ndi matenda a m’maganizo kapena kuti anali kumwa moŵa mopitirira muyeso kapenanso anali kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Choncho Eve K. Mościcki, wa ku bungwe la U.S. National Institute of Mental Health, ananena kuti: “Njira yodalirika kwambiri yoletsera anthu amisinkhu yonse kuti asadziphe ndiyo kupeŵa matenda a m’maganizo ndiponso obwera chifukwa chozoloŵera kuchita zinthu zinazake zoipa.”

N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amene amadwala matendaŵa safunafuna chithandizo. N’chifukwa chiyani samatero? “Chifukwa chakuti tsankhu lakula kwambiri pakati pa anthu,” anatero Yoshitomo Takahashi wa ku bungwe la Tokyo Metropolitan Institute of Psychiatry. Iye anawonjezera kuti mapeto ake amakhala akuti ngakhale anthu amene sakudziŵa kwenikweni kuti akudwala amachita mantha kuti apemphe mankhwala mwamsanga.

Komabe anthu ena salola kuti manyazi awalepheretse kupempha kuti athandizidwe. Hiroshi Ogawa, yemwe ndi muulutsi wodziŵika kwambiri pa TV ndiponso amene anali mkonzi wa pulogalamu yakeyake ku Japan kwa zaka 17, anavomereza poyera kuti amadwala matenda a m’maganizo ndiponso kuti wakhala akufuna kwambiri kudzipha. “Matenda a maganizo ali ngati chimfine,” anatero Ogawa. Iye anafotokoza kuti aliyense akhoza kudwala matendaŵa, koma atha kuchira.

Uzaniko Munthu Winawake

Béla Buda, yemwe ndi wamkulu ku bungwe loteteza anthu ofuna kudzipha la Hungary’s Association for the Prevention of Suicide amene tam’tchula kale, ananena kuti, “Munthu akakhala yekhayekha pa mavuto, nthaŵi zambiri amangoona ngati mavutowo n’ngaakulu kwambiri mwakuti sangawathetse.” Mawu ameneŵa akutsimikizira nzeru ya mwambi wakale umene uli m’Baibulo wakuti: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”—Miyambo 18:1.

Mverani mawu anzeru amenewo. Musalole kuti muvutike nawo nokha mavuto anu osautsawo. Funafunani munthu wina amene mungam’khulupirire komanso kumuuza zakukhosi. Mwina munganene kuti, ‘Koma palibe munthu wina aliyense amene ndingamuuze zakukhosi.’ Malingana n’kunena kwa Dr. Naoki Sato, amene amagwira ntchito yokhudza matenda a m’maganizo akuti anthu ambiri amaganiza choncho. Sato anati odwala ambiri angalephere kuuza anthu ena chifukwa chosafuna kuoneka kuti ali ndi vuto.

Kodi munthu angapite kwa ndani amene angam’mvere? M’madera ambiri, iye angapemphe kuti athandizidwe kuchokera kuchipatala choteteza anthu ofuna kudzipha kapena kupeza dokotala wabwino wa matenda a m’maganizo. Koma akatswiri ena amadziŵanso kuti njira ina yothandiza ndiyo chipembedzo. Kodi chipembedzo chingathandize bwanji?

Anathandizidwa Mmene Anali Kufunira

Munthu wina wa ku Bulgaria dzina lake Marin, yemwe ndi wolumala, ankalakalaka kwambiri kuti adziphe. Tsiku lina mosayembekezera anapeza magazini ya Mawu a Mulungu ya Nsanja Ya Olonda, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Anavomera pempho limene lili m’magaziniyo lakuti Mboni za Yehova zidzam’chezere. Marin anafotokoza zimene zinadzachitika kuti: “Anandiphunzitsa kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Atate wathu wakumwamba ndiponso kuti tilibe ufulu wodzipweteka tokha kapena wodzipha mwadala. Motero ndinasintha maganizo anga ofuna kudzipha ndipo moyo ndinayamba kuukondanso!” Marin anathandizidwanso mwachikondi ndi mpingo wachikristu. Ngakhale kuti ndi wolumalabe, iye ananena kuti: “Masiku ano ndimakhala wokondwa kwambiri ndiponso sindikhala ndi nkhaŵa kwambiri, komanso pali zinthu zambiri zosangalatsa zimene ndimachita ndipo ndimachita kusoŵa nthaŵi yozichitira! Zonsezi n’chifukwa cha Yehova ndi Mboni zake.”

Mwamuna wa ku Switzerland amene tam’tchula poyamba paja nayenso anathandizidwa ndi Mboni za Yehova. Panopo salephera kusimba za “kukoma mtima kwa banja lachikristu” limene linam’tenga n’kumakhala naye m’nyumba mwawo. Iye anawonjezera kuti: “Kenaka anthu a mumpingo [wa Mboni za Yehova] sankati andiitana liti kunyumba zawo kuti ndikadye nawo chakudya. Chimene chinathandiza si kundichereza kokhako ayi komanso kulankhula ndi anthuko.”

Iyeyu analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene anaphunzira m’Baibulo, makamaka pamene anaphunzira zakuti Mulungu woona Yehova amawakonda kwambiri anthu onse. (Yohane 3:16) Indedi, Yehova Mulungu amakumverani ‘mukatsanulira mitima yanu’ kwa iye. (Salmo 62:8) ‘Maso ake ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi,’ osati n’cholinga chopezera anthu zifukwa, koma n’cholinga cha “kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Yehova amatitsimikizira kuti: “Usaope, pakuti ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; ine, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”—Yesaya 41:10.

Potchula za lonjezo la Mulungu la dziko latsopano, mwamuna wa ku Switzerland ameneyu anati: “Zimenezi zandithandiza kuti ndisataye mtima kwambiri.” Chiyembekezo chimenechi chimene anati chili ngati “nangula wa moyo,” chikuphatikizaponso lonjezo la moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Ahebri 6:19; Salmo 37:10, 11, 29.

Moyo Wanu N’ngofunika kwa Ena

N’zoona kuti mungakumane ndi mavuto amene angakuchititseni kuona ngati kuti muli nokhanokha ndiponso amene angakuchititseni kuona ngati kuti mutafa palibe aliyense amene angadandaule nazo. Koma musaiwale kuti pali kusiyana kwambiri pakati pa kuona ngati muli nokhanokha ndi kukhaladi nokhanokha. M’nthaŵi za m’Baibulo mneneri Eliya anafika nthaŵi ina m’moyo wake imene anavutika maganizo kwambiri. Iye ananena kwa Yehova kuti: ‘Anapha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha.” Inde, Eliya anaonadi ngati kuti watsala yekhayekha, ndipotu panali chifukwa chomveka ndithu. Aneneri anzake ambiri anali ataphedwa. Anali ataopsezedwa kuti nayenso aphedwa, choncho ankathaŵa kuti adzipulumutse. Koma kodi analidi yekhayekha? Ayi. Yehova anam’dziŵitsa kuti kunali anthu okhulupirika 7,000 amene anali kuyesetsa mokhulupirika ngati iyeyo kutumikira Mulungu woona m’nthaŵi zoopsazo. (1 Mafumu 19:1-18) Nanga bwanji inuyo? N’kuthekatu kuti simulidi nokhanokha.

Pali anthu ena amene amakuganizirani. Pali anthu monga makolo anu, mkazi kapena mwamuna wanu, ana anu ndiponso anzanu. Koma palinso ena. Mumpingo wa Mboni za Yehova mukhoza kupeza Akristu okhwima maganizo amene amakuganizirani, amenenso angamvetsere mofatsa mukamawauza zakukhosi ndiponso amene angapemphere nanu komanso amene angakupempherereni. (Yakobo 5:14, 15) Ndipo ngakhale munthu wina aliyense wopanda ungwiro atakukhumudwitsani, alipo Munthu amene sadzakusiyani. Mfumu Davide yakale inanena kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Inde, Yehova ‘amasamalira inu.’ (1 Petro 5:7) Musaiwale kuti ndinu wofunika kwambiri kwa Yehova.

Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. N’zoonadi kuti nthaŵi zina moyo umaoneka ngati chinthu chotopetsa osati mphatso. Koma kodi mungamve bwanji ngati mutapatsa munthu wina mphatso yapamwamba kwambiri mwachifundo chabe kenaka iye n’kuitaya asanaigwiritse ntchito kwenikweni? Anthu opanda ungwirofe tangoyamba chabe kugwiritsa ntchito mphatso yamoyo imeneyi. Kwenikweni, Baibulo limasonyeza kuti moyo umene tili nawo panopa Mulungu sauona kuti ndi “moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:19) Inde, posachedwapa moyo wathu udzakhala wosasoŵa kanthu, wabwino kwambiri ndiponso wosangalatsa kwambiri. Zidzatheka bwanji?

Baibulo limati: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Taganizirani mmene moyo wanu udzakhalire mawu amenewo akadzakwaniritsidwa. Khalani kaye phee. Ndiye muyese kuganizira zinthu zabwino kwambiri zimene mumalakalaka kwambiri. Zimene mukuganizirazo zidzachitikadi. Mukamasinkhasinkha mmene Yehova anachitira ndi anthu ake akale, ndiye kuti chikhulupiriro chanu mwa iye chikula ndiponso zinthu zimene mumaganizira zija muyamba kuziona kuti ndi zenizeni ndipo zidzachitikadi.—Salmo 136:1-26.

Pangatenge kanthaŵi kuti mukhaliretu ndi maganizo ofuna kukhala ndi moyo. Pitirizani kupemphera kwa “Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4; Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Yehova angakupatseni mphamvu imene mukufunikira. Iye angakuphunzitseni kuti moyo ndi wokoma.—Yesaya 40:29.

[Bokosi patsamba 27]

Kodi Mungathandize Bwanji Munthu Amene Akuoneka Kuti Akufuna Kudzipha?

Kodi muyenera kutani ngati munthu wina atakuuzani kuti akufuna kudzipha? Bungwe la U.S. Centers for Disease Control and Prevention (CDC) linalangiza kuti, “Mvetserani mwachidwi akamakuuzani zakukhosi.” Mulekeni akuuzeni mmene akumvera. Koma nthaŵi zambiri munthu amene akufuna kudzipha amadzipatula ndipo sakonda kulankhula ndi ena. Dziŵani kuti akumvadi kupweteka kapena kuti wathedwadi nzeru. Ngati mutamuuza mwaulemu kuti akuoneka kuti wasintha pochita zinthu zina zake, mungam’pangitse kuti amasuke n’kukuuzani zakukhosi.

Muzimvetsera mosonyeza kuti zikukukhudzani. Bungwe la CDC linanena kuti, “N’kofunika kumuuza motsindika kuti moyo wake ndi wofunika kwa inu ndiponso kwa ena.” M’dziŵitseni mmene inuyo ndiponso anthu ena angadandaulire ngati iye atafa. M’thandizeni munthuyo kuona kuti Mlengi wake amam’ganizira.—1 Petro 5:7.

Akatswiri amatinso ndi bwino kuchotsa chinthu chilichonse chimene munthuyo angagwiritse ntchito kuti adziphe, makamaka mfuti. Ngati zikuoneka kuti zafika poopsa kwambiri, mwina mungam’limbikitse munthuyo kuti apite kuchipatala. Pamene zachita kunyanyira n’kutheka kuti simungachitire mwina koma kungoitanitsa achipatala othandiza pa zinthu za mwadzidzidzi.

[Bokosi patsamba 28]

Kodi Munthu Wina Amene Munali Kum’konda Anadzipha?

Munthu wina akadzipha, achibale ndiponso anzake apamtima amasokonezeka maganizo kwambiri. Ambiri amaona ngati iwowo ndiwo analakwa kuti munthuyo adziphe. Amanena zinthu monga zakuti: ‘Ndikanadziŵa sindikanam’siya yekha msanga tsiku limene lija,’ ‘Ndikanadziŵa sindikananena mawu aja ‘Ndikanadziŵa ndikanayesetsa ndithu kum’thandiza.’ Nkhani yaikulu imakhala yakuti, ‘Ndikanangochita zakuti kapena zakuti, bwenzi wokondedwa wanga alipobe.’ Koma kodi n’chilungamo kudziimba mlandu chifukwa cha kudzipha kwa munthu wina?

Musaiwale kuti n’kosavuta kutulukira zizindikiro za munthu amene anali kufuna kudzipha munthuyo atadzipha kale. Panopa n’kovuta ndithu kutulukira zizindikirozo munthuyo asanadziphe. Baibulo limati: “Mtima udziŵa zosautsa uwo, ndipo mlendo sangathe kugaŵana nawo chimwemwe chake.” (Miyambo 14:10, Malembo Oyera) Nthaŵi zina n’kosatheka n’komwe kudziŵa zimene munthu wina akuganiza. Anthu ambiri amene amafuna kudzipha sanena n’komwe kwa anthu ena, ngakhale kwa achibale awo enieni zimene akuganiza mumtima mwawo.

Buku lakuti Giving Sorrow Words limanena izi pankhani yokhudza zizindikiro za munthu wofuna kudzipha: “Kunena zoona nthaŵi zambiri n’kovuta kudziŵa zizindikiro zoterozo.” Buku lomwelo limawonjezera kunena kuti ngakhale kuti munaonadi zizindikiro zina mwa munthuyo, kungoona kokhako sindiye kuti mukanakhoza kum’letsa kuti asadziphe. M’malo momangodzivutitsa, mungalimbikitsidwe ndi mawu a Mfumu yanzeru Solomo akuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Wokondedwa wanuyo sakuzunzidwa m’moto wahelo. Ndipo zinthu zimene zinam’pweteka m’maganizo kuti mpaka adziphe zathera pomwepo. Iye sakuvutikanso; akungopumula.

Zingakhale bwino kwambiri tsopano kuganizira za anthu amene ali moyo komanso kudziganizira nokha. Solomo anapitiriza kuti: “Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako” udakali moyo. (Mlaliki 9:10) Khulupirirani kuti chiyembekezo cha anthu amene anadzipha cha kudzakhalanso ndi moyo chili m’manja mwa Yehova, “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.”—2 Akorinto 1:3. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 34 Mungapeze mfundo zokuthandizani kuona mosamala chiyembekezo cha m’tsogolo cha anthu amene anadzipha m’nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Kudzipha—Kodi Pali Chiukiriro?” mu Galamukani! ya September 8, 1990.

[Bokosi patsamba 29]

‘Kodi Mulungu Angandikhululukire Poganiza Zimenezi?’

Kusonkhana ndi Mboni za Yehova kwathandiza anthu ambiri kuthetsa maganizo ofuna kudzipha. Komabe masiku ano palibe munthu amene sakumana ndi zinthu zosautsa m’moyo kapena zovutitsa m’maganizo. Nthaŵi zambiri Akristu amene anaganizapo zofuna kudzipha chikumbumtima chimawapweteka akamaganizira zimenezo. Maganizo amenewo angathe kungowonjezera vuto lawolo. Nanga maganizo oterowo angathetsedwe bwanji?

Ndi bwino kudziŵa kuti amuna ndi akazi ena okhulupirika m’nthaŵi za m’Baibulo anadandaulapo kwambiri ndi moyo. Rebeka mkazi wa kholo lakale Isake, anasoŵa mtendere chifukwa cha mavuto a m’banja moti ananena kuti: ‘Ndalema nawo moyo wanga.’ (Genesis 27:46) Yobu amene anavutika chifukwa choferedwa ndi ana ake, kudwala kwambiri, kuwonongeka kwa chuma chake ndiponso kunyozeka m’maso mwa anthu, ananena kuti: “Mtima wanga ulema nawo moyo wanga.” (Yobu 10:1) Nthaŵi inayake Mose analirira Mulungu kuti: “Mundiphetu tsopano apa.” (Numeri 11:15) Eliya mneneri wa Mulungu, ananenapo panthaŵi ina kuti: “Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga.” (1 Mafumu 19:4) Ndipo mneneri Yona ananena kangapo konse kuti: “Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ayi.”—Yona 4:8.

Kodi Yehova anadana nawo anthu ameneŵa chifukwa choganiza zimenezi? Ayi sanatero. Iye m’malo mwake anasunga mawu awo m’Baibulo. Komabe n’kofunika kwambiri kudziŵa kuti palibe aliyense wa anthu okhulupirika ameneŵa amene analola maganizo ake kuti am’limbikitse zoti adziphe. Yehova anawakonda kwambiri; anafuna kuti akhale ndi moyo. Mulungutu amaganizira ngakhale moyo wa anthu oipa. Amawalimbikitsa kuti asinthe njira zawo kuti ‘akhale ndi moyo.’ (Ezekieli 33:11) Ngati amafuna oipa kuti akhale ndi moyo, nanga kuli bwanji anthu amene akuyesetsa kumusangalatsa!

Mulungu anapereka nsembe yadipo ya Mwana wake, anapereka mpingo wachikristu, Baibulo ndiponso mwayi wa kupemphera. Mungalankhulitsane ndi Mulungu m’njira imeneyi nthaŵi iliyonse imene mungafune. Mulungu angathe kumva ndipotu amamvetseradi anthu onse amene amam’lankhulitsa ndi mtima wodzichepetsa ndi woonadi. “Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.”—Ahebri 4:16.

[Chithunzi patsamba 25]

Moyo wanu n’ngofunika kwa ena

[Chithunzi patsamba 26]

Uzaniko munthu winawake