Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Matatu—Galimoto Zochititsa Chidwi za ku Kenya Zonyamula Apaulendo

Matatu—Galimoto Zochititsa Chidwi za ku Kenya Zonyamula Apaulendo

Matatu—Galimoto Zochititsa Chidwi za ku Kenya Zonyamula Apaulendo

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU KENYA

MUNTHU wokacheza ku Kenya salephera kusimba nkhani zambiri zosangalatsa akamafotokoza za ulendo wake. Munthuyo amakumbukirabe zinthu zina zimene anaona monga chimanthu cha njovu, chimkango champhamvu, ndiponso amakumbukira thambo lofiirira looneka dzuŵa likamaloŵa. Kunoku kuli zinthu zosiyanasiyana zokongola kwambiri. Komatu m’misewu yambiri m’derali mumapezeka zinthu zina zochititsa chidwi mwapadera. Zinthuzi ndi galimoto zimene anthu anazipatsa dzina loti matatu ndipo zimagwira ntchito zosiyanasiyana. Limeneli ndi dzina la gulu la galimoto zolipiritsa zimene anthu ambiri amakwera. Galimoto zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri ndipo n’chifukwa chake anthu ambiri amakonda kuyenda m’galimotozi ku Kenya.

Galimoto za matatu zinayamba mochititsa chidwi kwambiri ndipo zimayendanso mochititsa chidwi. Galimoto yoyamba ya mtunduwu inali chiphapha cha mtundu wa Ford chotchedwa Thames, cha asilikali a ku Britain chimene chinatsala pankhondo ya ku Ethiopia panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Kumayambiriro kwa m’ma 1960, munthu wina wa ku Nairobi ananyamula anzake pa chiphapha chimenechi kupita nawo m’kati mwa mzinda, n’kuwapempha kuti aliyense apereke makobidi ochepa okwana masenti 30 kuti agulire mafuta. * Kenaka posakhalitsa, anthu enanso anaona kuti galimoto zakale zimenezi zikhoza kuwabweretsera ndalama. Motero galimoto zambiri anazikonza kukhala zonyamula anthu 21 pozikhomera mabenchi oyang’anizana a matabwa kuti anthu azikhalira. Njira imeneyi n’njofanana ndi ya galimoto zakale za ku Nigeria zotchedwa bolekaja. Munthu aliyense ankalipira ma 10 senti atatu paulendo uliwonse. Mwina zimenezi n’zimene zinachititsa kuti galimotozi zipatsidwe dzina lakuti matatu, kuchokera ku mawu a Chiswahili akuti tatu, kutanthauza zinthu “zitatu.” Kuyambira nthaŵi imeneyo kudzafika lero, galimoto za matatu zinaloŵedwa m’malo ndi galimoto zatsopano zosiyana kwambiri ndi galimoto zaphokoso za poyamba zija. Inde, matatu zamasiku ano ndi galimoto zokhala ndi mitundu yowala kwambiri. Nyuzipepala ina ya ku Kenya inafotokoza kuti galimotozi zimaoneka “zosongoka kutsogolo ndipo n’zopakidwa mitundu yambiri ya penti.” Galimoto zimenezi sizinapangidwe ndi kakampani kosadziŵika bwino ka m’ma 1960!

Mukakwera galimoto ya matatu mumayenda mosangalala koma mtima uli m’mwamba, makamaka dalaivala wake akalimba mtima kudutsana ndi galimoto zambirimbiri zoyenda mumzindamo! Tatiyeni tiyendeko pang’ono chabe mumzinda wa Nairobi titakwera matatu ndiye tidzionere tokha kusangalatsa kwake.

Zochititsa Chidwi Kwambiri

Ulendo wathu uyambira pamalo pamene pamaimikidwa galimoto zambiri zamtunduwu poyembekeza kuti auyambe ulendo wopita kumadera osiyanasiyana. Tsopano nthaŵi ndi wani koloko masana ndipo anthu ali piringupiringu pofunafuna galimoto ya matatu yoyenera imene angakwere kuti akafike kumene akupita. Apaulendo ena akupita kutali ndi mzindawo, umene uli ulendo wotenga maola angapo kuti akafike. Ena akutuluka pang’ono mumzindawu, mwina kuti akangodya mwamsangamsanga. Galimoto ya matatu imathandiza kwambiri.

Kodi mwaona kuti galimoto zambiri zamtunduwu zili ndi mitundu yambiri yowala zedi? Si kuti zimenezi zikungowonjezera kuti galimotozi zizioneka bwino basi. Pali makasitomala ena amene amakonda kukwera m’galimoto za matatu zooneka bwino kwambiri. Mukayang’ana bwinobwino pa galimotozi muonanso kuti m’mbali mwake munalembedwa maina osiyanasiyana. Ena mwa mawu ameneŵa akufotokoza zinthu zikuluzikulu zochitika masiku ano, monga mwachitsanzo, “Elenino,” “Mileniyamu,” “Intaneti” ndi zina zotero. Mawu ena monga “Wofatsa” ndiponso “Mmishonale” amasonyeza zinthu zimene anthu amalakalaka kapena zimene amafuna atakhala. Galimoto imene imaoneka mofanana kwambiri ndi galimoto za matatu ndi inayake ya ku Philipines yotchedwa jeepney. N’zochititsa chidwi kuti nayonso jeepney inayamba kupangidwa nthaŵi yomweyo ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse.

Zimachititsa chidwi kwambiri kuona mmene anthu okwera galimotozi amadandaulirana. Ngakhale kuti kutsogolo kwa galimotozi kumakhala chikwangwani chosonyeza kumene akupita, makondakitala amaitanira anthu mokuwa kwambiri kwinaku madalaivala akuimba mahutala mothirira mang’ombe. Musadabwe kuona zikwangwani zina za matatu zolembedwa kuti akupita ku “Yerusalemu” kapena ku “Yeriko.” Ngati mutakwera galimoto yotero, si kuti mukafika kumeneko ayi, koma mukafika dera limene liri kunja kwa mzinda wa Nairobi limene lili ndi maina a m’Baibulo ameneŵa. N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri akuvutika kuti asankhe galimoto yoti akwere chifukwa chakuti makondakitala akulimbirana makasitomala kuti akwere m’galimoto zawo.

Loŵani, loŵani, loŵani, muno mu Mabulosi! Mwinatu mukakwera galimoto ya dzina limeneli mumangomva kukoma ngati kuti mukudyadi mabulosi. Zikuoneka kuti anthu ambiri akukonda kukwera matatu imeneyi chifukwa siinachedwe kudzaza. Kanyimbo kamene kakumveka chapansipansi kuchokera m’masipika aang’onoang’ono amene ali kudenga la galimotoyi kakuwasangalatsa anthu amene akwera. Komatu musaganize kuti galimoto zonse za matatu n’zotere. Pali zina zokhala ndi masipika aakulu pansi pamipando amene amalira mogonthetsa makutu. Komatu tsopano papita mphindi khumi chidzazireni mipando yonse. Koma matatu yathu siinayambebe ulendo wake. N’chifukwa chiyani ikuchedwa chonchi? Pakufunika kuti anthu ena aimirire m’mipata yomwe ili pakati pa mabenchiwo. Posakhalitsa galimotoyi yadzaziratu moti palibenso ndi mpata wina uliwonse woti munthu angathe kungotembenuka. Komansotu n’kutheka kuti matatu imeneyi iima kangapo m’njira kuti inyamulenso anthu ena.

Basi, tanyamuka tsopano. Anthu osadziŵana n’komwe akukambirana nkhani zosangalatsa kwambiri, makamaka zinthu zimene zachitika tsiku limeneli. Zikungokhala ngati ndi pamsika. Komatu musamale n’kuchita chidwi kwambiri ndi nkhanizo. Akuti anthu ena anapitirira nazo malo awo otsikira chifukwa chokomedwa kwambiri ndi nkhani zotere.

Tanena kale kuti galimoto ya matatu imagwira ntchito zingapo. Siidutsa njira imodzi yokha. Kuti ayende mwamsanga malingana ndi nthaŵi imene waganizira yekha, dalaivala amadutsa paliponse pamene pali kampata ngakhale m’tinjira todutsa anthu oyenda pansi, ndipo nthaŵi zina amatsala pang’ono chabe kugunda anthuwo. Komatu nayo ntchito ya kondakitala ndi yovuta. Iye akuyesetsa kuti alandire ndalama kwa anthu amene akwera omwe akuchita phokoso kwambiri, ndiponso ena akuvutavuta. Koma nthaŵi zambiri iye salekerera kuti winawake azingovuta zilizonse. Munthuyo amalipira kapena matatu imaima nthaŵi yomweyo n’kumuuza kuti atsike, ndipo nthaŵi zina amachita kum’tulutsa asakufuna! Kondakitalayo amam’dziŵitsa dalaivala za anthu amene akufuna kutsika, ndipo panthaŵi yomweyo amakhala tcheru kuyang’ana anthu ena amene akufuna kukwera. Iye amam’dziŵitsa dalaivala poimba likhwelu, kugogoda denga la galimotoyo kapena poliza belu limene analiika mwaluso pafupi ndi khomo. Ngakhale kuti pali malo ake enieni oimira galimoto zonse zonyamula anthu, matatu zimaima pena paliponse nthaŵi ina iliyonse, mwina pokweza kapena potsitsa anthu.

Popeza kuti tatuluka m’kati mwa mzinda, tafika tsopano ku kadera kena kamene kali kunja kwa mzinda ndipo n’kumene anthu ambiri akutsikira. Ndi nthaŵi yoti matatu ibwerere komwe yachokera. Inyamulanso anthu ambiri m’njira. Anthu ameneŵa nawo akumana ndi zimene takumana nazo ifeyo. N’zosakayikitsa kuti ngakhale ulendo wathu unali wa mabampu tayenda bwino kwambiri m’mabulosi.

Galimotozi Sizidzasiya Kugwira Ntchito Yawo

Ku Kenya kuli galimoto za matatu zoposa 30,000, ndipo bizinesi ya matatu imeneyi inayamba ndi galimoto yotsala pankhondo zaka makumi angapo zapitazo ndipo panopa yasanduka bizinesi yaikulu, ndiponso ya ndalama zambiri. Komabe zagwapo m’vuto chifukwa chochita zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, madalaivala ake akhala akuimbidwa milandu chifukwa chosasunga malamulo apamsewu okhudza zinthu zina zoyenda pamsewu, ndipo boma lakhazikitsa malamulo ena othandiza kuti bizinesiyo isakule monyanyira. Chifukwa cha malamulo otere nthaŵi zina anthu ochita bizinesiyi amasiya kuyendetsa galimoto zawo, ndipo potero anthu ambiri amene amadalira matatu tsiku lililonse amavutika mayendedwe. Ngakhale kuti si anthu onse amene amakonda kayendedwe ka matatu, galimotozi ndi zothandizadi kwa anthu ofuna ulendo wofulumira amene amapeza ndalama zochepa m’derali.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Shilling ndi ndalama ya ku Kenya yokwana masenti 100 a ku Kenyako. Dola imodzi ya ku United States imakwana pafupifupi ma shilling 78.

[Chithunzi patsamba 16, 17]

Galimoto ya mtundu wa Ford yotchedwa Thames

[Mawu a Chithunzi]

Noor Khamis/The People Daily