Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 09

Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu

Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu

Kodi nthawi zina mumaona kuti mumafunikira malangizo okuthandizani pa moyo wanu? Kodi muli ndi mafunso amene mukufunitsitsa mutadziwa mayankho ake? Kodi mukufuna kutonthozedwa kapena kulimbikitsidwa? Kodi mukufuna kuti Yehova akhale mnzanu wapamtima? Pemphero lingakuthandizeni pa zinthu zonsezi. Koma kodi tiyenera kupemphera motani? Kodi Mulungu amamvetsera mapemphero onse? Kodi mungachite chiyani kuti Mulungu azimvetsera mapemphero anu? Tiyeni tione.

1. Kodi tiyenera kupemphera kwa ndani, nanga tingapempherere zinthu ziti?

Yesu anatiphunzitsa kuti tizipemphera kwa Atate wathu wakumwamba yekha. Yesu nayenso ankapemphera kwa Yehova. Iye anati: “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba . . . ’” (Mateyu 6:9) Tikamapemphera kwa Yehova, Iye amakhala mnzathu wapamtima.

Tikhoza kupempherera nkhani ina iliyonse. Koma kuti Mulungu ayankhe mapemphero athu, mapempherowo ayenera kukhala ogwirizana ndi cholinga chake. Baibulo limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Yesu anatipatsa chitsanzo cha zinthu zoyenera kupempherera. (Werengani Mateyu 6:9-13.) Kuwonjezera pa kupempherera nkhawa zathu, tisamaiwale kuthokoza Mulungu chifukwa cha zimene amatichitira komanso kumupempha kuti athandize anthu ena.

2. Kodi tiyenera kupemphera motani?

Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizimukhuthulira Mulungu za mumtima mwathu.’ (Salimo 62:8) Choncho mapemphero athu ayenera kukhala ochokera pansi pa mtima. Tikhoza kupemphera mokweza kapena mosatulutsa mawu. Tikhoza kupemphera titakhala pansi, titaimirira, kapena titakhala mwanjira ina iliyonse, bola tichite zinthu mwaulemu. Tingapemphere pamalo alionse komanso nthawi iliyonse.

3. Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero athu?

Yehova amayankha mapemphero m’njira zosiyanasiyana. Iye anatipatsa Mawu ake Baibulo, lomwe limatithandiza kupeza mayankho a mafunso athu. Kuwerenga Mawu a Mulungu kumapatsa “nzeru munthu wosadziwa zinthu.” (Salimo 19:7; werengani Yakobo 1:5.) Yehova amatipatsa mtendere wa mumtima tikakumana ndi mavuto. Iye amagwiritsanso ntchito atumiki ake kuti atithandize pamene tavutika kwambiri.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti mapemphero anu azikhala ochokera pansi pa mtima ndiponso osangalatsa Mulungu. Onaninso mmene pemphero lingakuthandizireni.

4. Kodi mungatani kuti Mulungu aziyankha mapemphero anu?

Kodi ndi zinthu ziti zimene zimapangitsa kuti Mulungu azimva mapemphero athu kapena asamamve? Onerani VIDIYO.

Yehova amafuna kuti tizipemphera kwa iye. Werengani Salimo 65:2, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi mukuganiza kuti “Wakumva pemphero” amafuna kuti inuyo muzipemphera kwa iye? N’chifukwa chiyani mukuganiza choncho?

Kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene iye amafuna. Werengani Mika 3:4 ndi 1 Petulo 3:​12, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi tiyenera kuchita zotani kuti Yehova azimva mapemphero athu?

Pa nthawi ya nkhondo, asilikali a mbali zonse angapemphere kuti awine. Kodi n’zomveka kuyembekezera kuti Mulungu ayankha mapemphero oterewa?

5. Mapemphero athu azikhala ochokera pansi pa mtima

Anthu ena anaphunzitsidwa kuti azingobwereza mawu omweomwewo popemphera. Koma kodi Mulungu amafuna kuti tizipemphera mwanjira imeneyi? Werengani Mateyu 6:​7, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mungatani kuti popemphera musamanene “zinthu mobwerezabwereza?”

Tsiku lililonse, mukhoza kuganizira chinthu chimodzi chimene Yehova wakuchitirani pa moyo wanu n’kumuthokoza chifukwa cha chinthu chimenecho. Mukhoza kuchita zinthu zimenezi tsiku lililonse kwa mlungu umodzi, ndipo mudzaona kuti mwapempherera zinthu zosiyanasiyana zokwana 7 popanda kubwerezabwereza mapemphero anu.

Bambo wabwino amafuna kuti mwana wake azilankhula naye kuchokera pansi pa mtima. Yehova amafunanso kuti tizipemphera kwa iye kuchokera mumtima

6. Pemphero ndi mphatso yochokera kwa Mulungu

Kodi pemphero lingatipatse bwanji mphamvu pamene zinthu zikuyenda bwino komanso pamene sizikuyenda bwino pa moyo wathu? Onerani VIDIYO.

Baibulo limanena kuti pemphero lingatithandize kupeza mtendere wa mumtima. Werengani Afilipi 4:6, 7, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Ngakhale kuti nthawi zina mavuto athu amakhalapobe tikapemphera, kodi pemphero limatithandiza bwanji?

  • Tchulani zinthu zina zimene mungakonde kupempherera.

Kodi mukudziwa?

Mawu akuti “ame” amatanthauza “zikhale momwemo” kapena “ndithudi.” Ngakhale anthu akale otchulidwa m’Baibulo ankanena kuti “ame” akamaliza kupemphera.​—1 Mbiri 16:36.

7. Muzipeza nthawi yopemphera

Nthawi zina timatanganidwa kwambiri mpaka kuiwala kupemphera. Kodi Yesu ankaona kuti kupemphera n’kofunika bwanji? Werengani Mateyu 14:23 ndi Maliko 1:35, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yesu ankatani kuti azipeza nthawi yopemphera?

  • Kodi inuyo mukhoza kumapemphera nthawi yanji?

ZIMENE ENA AMANENA: “Pemphero silothandiza kwenikweni. Limangochititsa kuti maganizo a munthu akhale m’malo.”

  • Nanga inuyo mukuganiza bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Mapemphero ochokera pansi pa mtima amathandiza kuti Mulungu akhale mnzathu, amatipatsa mtendere wa mumtima, ndiponso amatipatsa mphamvu kuti tithe kuchita zinthu zosangalatsa Yehova.

Kubwereza

  • Kodi tiyenera kupemphera kwa ndani?

  • Kodi tiyenera kupemphera motani?

  • Kodi pemphero limatithandiza bwanji?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Pezani mayankho a mafunso amene anthu ambiri amakhala nawo okhudza pemphero.

“Mfundo 7 Zimene Muyenera Kudziwa pa Nkhani ya Pemphero” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2010)

Dziwani chifukwa chake muyenera kupemphera komanso zimene mungachite kuti mapemphero anu azikhala abwino.

“N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupemphera?” (Nkhani yapawebusaiti)

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti tizipemphera kwa ndani?

“Kodi Ndizipemphera kwa Anthu Oyera Mtima?” (Nkhani yapawebusaiti)

Munyimboyi onani ngati malo kapena nthawi zingachititse kuti Mulungu amve mapemphero athu.

Uzipemphera Nthawi Iliyonse (1:22)