Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 46

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka Ndiponso Kubatizidwa?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka Ndiponso Kubatizidwa?

Munthu amadzipereka kwa Yehova akamulonjeza m’pemphero kuti azilambira iye yekha basi ndiponso kuti aziika zofuna za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wake. (Salimo 40:8) Kenako amabatizidwa. Umenewu umakhala umboni wakuti anadzipereka kwa Yehova. Choncho, kudzipereka kwa Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri chimene munthu ayenera kuchita pa moyo wake. Ndiye popeza kudzipereka kwa Yehova n’kofunika kwambiri ndiponso kungasinthe moyo wanu, n’chiyani chimene chingakuchititseni kusankha zimenezi?

1. N’chiyani chimachititsa munthu kuti adzipereke kwa Yehova?

Timadzipereka kwa Yehova chifukwa chakuti timamukonda kwambiri. (1 Yohane 4:10, 19) Baibulo limatiuza kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Timasonyeza kuti timakonda Mulungu mwa zolankhula ndi zochita zathu. Zimenezi tingaziyerekezere ndi mwamuna ndi mkazi omwe amasankha kukwatirana chifukwa choti akondana. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene amakonda Yehova. Chikondicho chimamupangitsa kuti adzipereke kwa iye komanso kubatizidwa.

2. Kodi Yehova amawadalitsa bwanji atumiki ake omwe abatizidwa?

Mukabatizidwa mudzalowa m’banja labwino kwambiri la Yehova. Kenako mudzaona kuti Yehova amakukondani kwambiri m’njira zosiyanasiyana ndipo mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba kuposa panopa. (Werengani Malaki 3:16-18.) Mudzayamba kuona Yehova monga Atate wanu ndipo mudzakhala ndi abale ndi alongo padziko lonse lapansi omwe amakonda Yehova komanso omwe amakukondani kwambiri. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Komabe, pali zinthu zina zomwe muyenera kuchita musanabatizidwe. Mukufunika kuphunzira zokhudza Yehova, kumukonda komanso kukhulupirira Mwana wake. Kenako mudzipereke kwa Yehova, kutanthauza kuti mumuuze m’pemphero kuti mudzamutumikira moyo wanu wonse. Mukachita zinthu zimenezi n’kubatizidwa mudzakhala ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amanena kuti ubatizo umapulumutsa munthu.​—1 Petulo 3:21.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe kufunika kodzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa.

3. Tonsefe tifunika kusankha amene tikufuna kumutumikira

Kale ku Isiraeli, anthu ena ankaganiza kuti akhoza kumalambira Yehova kwinaku akulambira mulungu wonyenga Baala. Koma Yehova anatumiza mneneri wake Eliya kuti akathandize anthuwo kuzindikira kuti kuchita zimenezi si koyenera. Werengani 1 Mafumu 18:21, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Aisiraeli ankafunika kusankha kuchita chiyani?

Mofanana ndi Aisiraeli, ifenso tikufunikira kusankha yemwe tikufuna kumutumikira. Werengani Luka 16:13, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani n’zosatheka kulambira Yehova kwinaku tikulambiranso munthu kapena chinthu chinachake?

  • Kodi tingamusonyeze bwanji Yehova kuti tinasankha kutumikira iye yekha basi?

4. Muziganizira zimene Yehova amachita posonyeza kuti amakukondani

Yehova watipatsa mphatso zambiri zamtengo wapatali. Ndiye kodi ifeyo tingamupatse chiyani? Onerani VIDIYO.

Kodi Yehova wakusonyezani chikondi m’njira ziti? Werengani Salimo 104:14, 15 ndi 1 Yohane 4:9, 10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi ndi mphatso ziti zimene Yehova anakupatsani zimene mumaziyamikira kwambiri?

  • Kodi mphatso zimenezo zikukuchititsani kuti muzimuona bwanji Yehova?

Munthu akatipatsa mphatso inayake yomwe yatisangalatsa kwambiri timamuyamikira. Werengani Deuteronomo 16:17, kenako mukambirane funso ili:

  • Mukaganizira zonse zimene Yehova wakuchitirani, kodi mukuona kuti mungamupatse chiyani?

5. Timapeza madalitso ambiri tikadzipereka kwa Yehova

Anthu ambiri amaganiza kuti angamakhale osangalala ngati atakhala otchuka, ngati akugwira ntchito yabwino kapenanso ngati ali ndi ndalama zambiri. Koma kodi zimenezi n’zoona? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani Andrey anasankha kusiya kusewera mpira ngakhale kuti ankaukonda kwambiri?

  • Kodi mukuganiza kuti anachita bwino kusiya kusewera mpira n’kudzipereka kwa Yehova? N’chifukwa chiyani mukutero?

Mtumwi Paulo asanakhale Mkhristu ankagwira ntchito yapamwamba. Iye anali atachita maphunziro okhudza malamulo Achiyuda ndipo anaphunzitsidwa ndi mphunzitsi wotchuka kwambiri pa nthawiyo. Koma anasiya zonsezi n’kukhala Mkhristu. Kodi Paulo ananong’oneza bondo ndi zimene anasankhazi? Werengani Afilipi 3:8, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti zimene ankachita poyamba asanakhale Mkhristu zinali ngati “mulu wa zinyalala”?

  • Nanga anapeza madalitso otani chifukwa cha zimene anasankhazi?

  • Kodi mukuganiza kuti moyo wanu ungakhale wabwino kwambiri ngati mutasankha kutumikira Yehova? N’chifukwa chiyani mukutero?

Paulo atakhala Mkhristu anapeza zinthu zambiri kuposa zimene anasiya

ZIMENE ENA AMANENA: “Munthu sufunika kuchita kudzipereka kwambiri kwa Mulungu, bola ngati umapemphera basi.”

  • N’chifukwa chiyani mukuona kuti kudzipereka kwa Yehova n’kofunika kwambiri?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Timadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa chifukwa chomukonda.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kumukonda ndi kumulambira ndi mtima wathu wonse?

  • Kodi Yehova amawadalitsa bwanji atumiki ake omwe abatizidwa?

  • Kodi inuyo mungakonde kupereka moyo wanu kwa Yehova?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani chifukwa chake woimba wina komanso katswiri wamasewera a mpira anasankha kudzipereka kwa Yehova.

Zimene Achinyamata Amafunsa​—Kodi Ndidzachita Zotani Pamoyo Wanga?​—Zimene Anasankha 6:54

Onani zifukwa zinanso zimene zingapangitse munthu kuti adzipereke kwa Yehova.

“N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka kwa Yehova?” (Nsanja ya Olonda, January 15, 2010)

Onerani nyimboyi kuti muone mmene anthu omwe amadzipereka kwa Yehova amasangalalira.

Ndadzipereka Kwa Inu 4:30

Munkhani yakuti, “Kwa Zaka Zambiri Ndinkadzifunsa Kuti, ‘Kodi Mulungu Anatilengeranji Anthufe?’” onani zimene zinachititsa munthu wina kuganiziranso zinthu zimene ankaziona kuti ndi zofunika pa moyo wake.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2012)