Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 21

Ndi Ndani Amene Amalalikira Uthenga Wabwino?

Ndi Ndani Amene Amalalikira Uthenga Wabwino?

Posachedwapa, Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetsa mavuto onse amene tikukumana nawo. Uthenga umenewu ndi wosangalatsa kwambiri ndipo aliyense ayenera kuumva. Yesu ankafuna kuti otsatira ake azilalikira uthenga umenewu kwa wina aliyense. (Mateyu 28:​19, 20) Kodi a Mboni za Yehova amachita zotani pomvera lamulo la Yesu?

1. Kodi lemba la Mateyu 24:14 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

Yesu ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:14) A Mboni za Yehova amasangalala kugwira ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Timalalikira uthenga wabwino padziko lonse m’zinenero zoposa 1,000. Ntchitoyi ndi yaikulu kwambiri. Ndipo imafunika kuigwira mwakhama komanso mwadongosolo. Komabe sitingakwanitse kuigwira patokha popanda kuthandizidwa ndi Yehova.

2. Kodi timachita zotani kuti tilalikire anthu?

Timalalikira kwina kulikonse kumene tingapeze anthu. Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, timalalikira “kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 5:42) Njira imeneyi, imatithandiza kuti tizilalikira anthu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse. Popeza nthawi zina anthu ena sapezeka pakhomo, timalalikiranso m’malo opezeka anthu ambiri. Timayesetsa kugwiritsa ntchito mwayi ulionse kuti tiuze ena zokhudza Yehova ndiponso zimene amafuna.

3. Ndi ndani amene ali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino?

Mkhristu woona aliyense ali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino. Timaona kuti udindo umenewu ndi wofunika kwambiri. Timalalikira mulimonse mmene tingathere chifukwa timadziwa kuti miyoyo ya anthu ili pangozi. (Werengani 1 Timoteyo 4:16.) Sitilandira malipiro alionse tikamagwira ntchitoyi, chifukwa Baibulo limati: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:​7, 8) Ngakhale kuti anthu ena amakana uthenga wathu sitisiya kulalikira chifukwa kugwira ntchitoyi ndi mbali ya kulambira kwathu ndipo imasangalatsa Yehova.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene a Mboni za Yehova amachita kuti alalikire padziko lonse komanso mmene Yehova amawathandizira.

4. Timachita khama kuti tilalikire anthu a mitundu yonse

A Mboni za Yehova amachita khama kuti akalalikire anthu kulikonse komwe ali. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chiyani chimene chikukuchititsani chidwi mukaganizira khama limene a Mboni za Yehova amachita kuti alalikire anthu?

Werengani Mateyu 22:39 ndi Aroma 10:13-15, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi ntchito yathu yolalikira imasonyeza bwanji kuti timakonda anthu?

  • Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amalalikira uthenga wabwino?​—Onani Aroma 10:15.

5. Ndife antchito anzake a Mulungu

Zimene zimachitika tikamagwira ntchito yolalikira ndi umboni wakuti Yehova amatsogolera ntchito yathu. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira m’bale wina wa ku New Zealand, dzina lake Paul. Tsiku lina akulalikira kunyumba ndi nyumba chakumadzulo, anakumana ndi mayi wina. M’mawa wa tsikuli, mayiyu anali atapemphera kwa Mulungu pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova ndipo anamupempha kuti amutumizire munthu woti adzamulalikire. Ndiyeno M’bale Paul anati: “Patangopita maola atatu ndinafika pakhomo la mayiyu.”

Werengani 1 Akorinto 3:9, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi chitsanzo cha ku New Zealand chikusonyeza bwanji kuti Yehova ndi amene amatsogolera ntchito yolalikira?

Werengani Machitidwe 1:8, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani timafunikira thandizo la Yehova kuti tigwire bwino ntchito yathu yolalikira?

Kodi mukudziwa?

Mlungu uliwonse, pamsonkhano wamkati mwa mlungu, timaphunzira mmene tingagwirire ntchito yolalikira. Ngati munapangapo misonkhanoyi, kodi mukuona kuti maphunziro amenewa ndi othandizadi?

6. Timamvera lamulo la Mulungu lakuti tizilalikira

Mu nthawi ya atumwi, anthu otsutsa ankauza otsatira a Yesu kuti asiye kulalikira. Komabe, Akhristuwa anateteza ufulu wawo wolalikira mwa “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.” (Afilipi 1:7) Ndi zimenenso a Mboni za Yehova amachita masiku ano. a

Werengani Machitidwe 5:27-42, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani sitingasiye kugwira ntchito yolalikira?​—Onani vesi 2938 ndi 39.

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amalalikira kunyumba ndi nyumba?”

  • Kodi mungamuyankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yesu analamula otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse. Yehova amathandiza anthu ake akamagwira ntchito imeneyi.

Kubwereza

  • Ndi ndani amene amalalikira uthenga wabwino padziko lonse?

  • Kodi ntchito yathu yolalikira imasonyeza bwanji kuti timakonda anthu?

  • Kodi mukuona kuti ntchito yolalikira ingatithandize kukhala osangalala? N’chifukwa chiyani mukutero?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zimene a Mboni za Yehova amachita polalikira m’mizinda ikuluikulu.

Ntchito Yapadera Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri ku Paris 5:11

Kodi a Mboni za Yehova achitapo zotani pothandiza anthu othawa kwawo?

Kuthetsa Ludzu Lauzimu la Anthu Othawa Kwawo 5:59

Onani mmene kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse kunathandizira munthu wina kukhala wosangalala.

Ndimasangalala Kuti Ndinasankha Kutumikira Yehova 6:29

Dziwani zokhudza milandu yofunika kwambiri imene tawinapo yomwe yathandizira kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ipite patsogolo.

“Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti” (Ufumu wa Mulungu Ukulamulira!, mutu 13)

a A Mboni za Yehovafe sitifunikira kupempha chilolezo cha munthu kuti tigwire ntchito yolalikira chifukwa Mulungu ndi amene anatilamula kuti tizigwira ntchitoyi.