Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Africa

Africa
  • MAYIKO 58

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 979,685,702

  • OFALITSA 1,363,384

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 3,265,314

“Ndakonzeka Kutuluka mu Babulo Wamkulu”

Mnyamata wina wa ku Uganda, dzina lake Thomson, anakhumudwa ndi zimene zinkachitika m’chipembedzo. Iye anasiya kupita kutchalitchi chifukwa chakuti atsogoleri awo ankangofuna ndalama basi. Koma sanasiye kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Ankachita chidwi kwambiri ndi buku la Chivumbulutso ndipo ankayesetsa kuti amvetse tanthauzo lake n’kulemba notsi m’kope. Ndiyeno  m’bale wina anamupeza Thomson akuwerenga Baibulo pamalo amene ankagwira ntchito yake yazomangamanga. Anakambirana zambiri ndipo iye analandira buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Usiku wa tsiku limenelo, Thomson anamaliza kuwerenga buku lonse. Ndiyeno kutacha, m’baleyo analandira meseji yonena kuti: “Ndikuthokoza kwambiri Ambuye chifukwa cha buku limene mwandipatsa. Panopa ndakonzeka kutuluka mu Babulo Wamkulu.” Thomson anapempha kuti amupatse mabuku onse amene analembedwa m’mawu a m’munsi ndiponso kumapeto kwa bukuli. Iye ankaphunzira Baibulo mwakhama kwambiri moti anabatizidwa mu 2012 pa msonkhano wachigawo wakuti ‘Tetezani Mtima Wanu.’ Mu March 2013, Thomson anayamba upainiya wokhazikika ndipo akuthandiza anthu ena kuti atulukenso mu Babulo Wamkulu.

Anaphunzitsidwa ndi Abale Okwana 8

Munthu wina dzina lake Jimmy anakulira mumzinda wa Port Louis, womwe ndi likulu la dziko la Mauritius. Anayamba kumwa mowa ali ndi zaka 16, ndipo kenako ankaledzera tsiku ndi tsiku. Akaledzera ankalephera kudziletsa ndipo ankachita zinthu zimene zinachititsa kuti akhale kabwerebwere wa kundende. Nthawi zina ankatha kumwa mikunda itatu ya kachasu ndiponso kusuta ndudu 60 pa tsiku. Ndalama za kachasu zikamuthera ankangomwa mankhwala otsukira mawindo. Zikavutitsitsa ankangomwa perefyumu wa mayi ake. Munthu wina atamuuza kuti akuoneka ngati mtembo, anaganiza zopita kumalo othandiza anthu kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa. Anakhala kumeneko chaka ndi hafu koma sizinamuthandize.

Rodrigues: Jimmy ankafunitsitsa kusintha makhalidwe ake

Kenako Jimmy anakumana ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Nthawi zina ankasiya kuphunzira kuti amwe kaye mowa. Pamene ankafika  pozindikira kuti ayenera kusintha, anali ataphunzira ndi abale osiyanasiyana okwana 8. Iye anati: “Ndinamva ngati lupanga lotchulidwa pa Aheberi 4:12 likulasa mtima wanga. Tsiku lina ndikuwerenga Baibulo ndinaona lemba la Miyambo 24:16, limene limanena kuti: ‘Wolungama akhoza kugwa nthawi 7 ndipo amadzukanso.’ Mawu amenewa ndi amene anandithandiza kwambiri kuti ndisinthe.” Ataphunzira ndi abale 7, “n’kugwa” Jimmy anayesetsa “kudzukanso” ndipo m’bale wa nambala 8 anamuthandiza. Jimmy ankachonderera Yehova kuti amupatse mphamvu zoti asinthe, ankapita ku misonkhano ndipo anasiya zoipa zimene ankachita. Anabatizidwa mu 2003 ndipo anayamba upainiya wokhazikika mu 2012. Panopo ndi mtumiki wothandiza mumpingo wina wa pachilumba cha Rodrigues.

“Yehova ndi Angelo Adzakhala Anzanga”

Mayi wina wa ku Kenya wazaka 70 , dzina lake Mary, anali membala wa chipembedzo chinachake kwa zaka zambiri. Iye ankathandiza kwambiri chipembedzocho kuti chizipeza ndalama ndipo anathandizanso kuti tchalitchi china chimangidwe. Pamene mwana wake wina anakhala Mboni, Mary sanasangalale. Mwanayo ankamuitana kuti apite naye ku misonkhano koma Mary ankakana. Iye ankanena kuti akufuna kumva uthenga wa m’Baibulo mu chinenero chake cha Chikikuyu osati Chiswahili. Koma kenako Mary anavomera kupita ku msonkhano wachigawo umene unachitika mu Chikikuyu. Pa msonkhanowu anakhala pamalo a okalamba. Iye anachita chidwi kwambiri ndi mmene anthu anachitira naye zinthu mwachikondi. Ananena kuti sanaonepo chikondi ngati chimenechi m’chipembedzo chake. Iye anamvetsera mwatcheru  nkhani zonse ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anamva. Munthu wina atamuuza kuti angaphunzire naye m’kabuku kakuti Mverani Mulungu, anavomera nthawi yomweyo.

Mary atangophunzira kwa miyezi yochepa, anasankha zoti akhale wa Mboni za Yehova ndipo anatsanzika ku chipembedzo chakecho. Atsogoleri a chipembedzocho anakwiya kwambiri. Iwo anaitana m’busa mumzinda wa Nairobi, womwe ndi likulu la dzikolo, kuti abwere kudzalankhula naye. Iye anayesetsa kulimbikitsa Mary kuti asasiye chipembedzocho, koma iye sanasinthe maganizo. M’busayu anamufunsa kuti: “Kodi ndani adzakhale anzanu mukasiya chipembedzochi? Paja muli ndi anzanu ambiri amene ali m’tchalitchichi.”

Mary anayankha kuti: “Yehova ndi angelo adzakhala anzanga. Nawonso a Mboni adzakhala anzanga.”

Poona kuti walephera kusintha maganizo a Mary, m’busayu anachoka. Ndiyeno Mary akupitiriza kuphunzira Baibulo ndipo amapita ku misonkhano ngakhale kuti amakhala kutali. Tsiku lina anayenda kwa maola awiri mvula ikugwa kuti afike ku misonkhano chifukwa chakuti sanathe kukwera basi tsikulo. Ngakhale kuti  anthu ena okhala nawo pafupi akumutsutsa, Mary akufunitsitsa kuti akwaniritse cholinga chake choti abatizidwe.

Liberia: Akukonza malo oti achitire Chikumbutso. Mu 2013, ofalitsa 6,148 analandira alendo okwana 81,762

Abusa Anamutchera Ndale

Ku Cameroon kuli mtsikana wina wazaka 14 dzina lake Ashton. Iye amakhala ndi abambo ake aakulu. Atangoyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, bambo akewo limodzi ndi akazi awo anayamba kumutsutsa koopsa. Ankamukakamiza kuti azipita nawo ku mapemphero a tchalitchi cha Pentekosite. Tsiku lina ku mapempherowo, m’busa ankaika dzanja pa mitu ya anthu kuti awapatse mzimu ndipo anthuwo ankagwa. Koma ataika dzanja pamutu wa Ashton, sanagwe. Ndiyeno m’busayo anapemphera mobwerezabwereza koma iye osagwabe. Kenako m’busayo anangomutchera ndale n’kumugwetsa. Atafika kunyumba, Ashton anauza bambo ndi mayi akewo kuti abusa anamutchera ndale koma iwo sanakhulupirire. Nthawi yomweyo, iye anaganiza zoti asadzabwererenso kutchalitchiko. Ashton amapitabe ku misonkhano ngakhale kuti abale ake komanso aneba ake amamutsutsa kwambiri.

Anaitanidwa ndi Kamwana

Ku Angola, kamwana kena ka chaka chimodzi ndi miyezi 5, dzina lake Anilpa, kanagwira nawo mwakhama ntchito yoitanira anthu ku msonkhano wachigawo wa chaka chatha. Ntchito ya Anilpa inali yogogoda pakhomo n’kupereka kapepala koitanira anthu ku msonkhano pomwe mayi ake ankafotokoza mwachidule zimene abwerera. Ntchitoyi inafika pomusangalatsa kwambiri moti nthawi zina, sankadikira kuti mayi ake amalize kukambirana ndi  munthu asanakagogode khomo lina. Anilpa anachititsa chidwi kwambiri anthu omwe ankawapatsa timapepalawo moti pa tsiku lomaliza la msonkhano, mayi wina anabwera n’kumuuza kuti: “Ndimakufunafunatu. Ndasangalala kukupeza chifukwa ndiwe unandiitana ku msonkhanowu.”

Anatopa ndi Kuponderezedwa

Mu August 2012, ofalitsa ena ochokera mumpingo wa Antaviranambo ku Madagascar anakumana ndi gulu lina la anthu amene ananena kuti akufuna kukhala Mboni za Yehova. Anthuwo ankaona kuti akuponderezedwa ndi atsogoleri a matchalitchi awo omwe ankaphunzitsa zinthu zina koma n’kumachita zina. Anthuwo ananena kuti m’matchalitchi awo sawaphunzitsa Baibulo ndiponso alibe mabuku ofotokoza zimene amakhulupirira. Anadandaulanso kuti ankayenera kupereka ndalama zambiri m’matchalitchi awo komanso anthu sakondana mmene Akhristu oona ayenera kuchitira. Iwo ananenanso kuti a Mboni za Yehova sakhala ndi mavuto amenewa.

Kenako anthuwo analemba kalata yopita ku ofesi ya nthambi. M’kalatayo anati: “Tikukulemberani pofuna  kukudziwitsani kuti tikufunitsitsa kutumikira Yehova. Koma timakhala kutali. Enafe timayenda mtunda wa maola 9 kapena 15 kuti tikafike ku misonkhano. Choncho tikukupemphani kuti mutitumizire munthu woti azitiphunzitsa Baibulo. Sitingakwanitse kutumikira Yehova ndi mtima wonse ngati simutithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. Tilipo anthu okwana 215 ochokera m’midzi itatu. Tinali m’zipembedzo zosiyanasiyana koma panopa tonsefe tikufunitsitsa kutumikira ndiponso kumvera Yehova ndi mtima wonse. Tikudziwa kuti mudzatithandiza.”

Abale ena anapita kukakumana ndi anthuwo ndipo anayenda kwa maola 9 kuti akafike kumudzi woyamba. Kumudziko, abalewo anachititsa msonkhano ndipo anthu 65 anafika. Pasanapite nthawi, anthu ambiri kumidzi ina anamva ndipo ananena kuti nawonso akufuna kuti aphunzitsidwe Baibulo. Ndiyeno abalewo anayendanso kwa maola 4 n’kufika kumudzi wina kumene anthu 80 anafika pamsonkhano. Kumeneko anakumananso ndi anthu ena amene anawapempha kuti apite kumudzi kwawo ndipo anafunika kuyenda maola awiri. Abalewo anavomera ndipo anakachititsanso msonkhano kumeneko. Anthu oposa 50 anabwera.

Anthu oposa 30 ochokera m’midziyi anapita ku msonkhano kutauni ya Mahanoro ndipo anayenera kuyenda tsiku limodzi ndi hafu kuti afike. Izi zinachitika pa misonkhano iwiri. Anthu 25 anafikanso pa nthawi imene woyang’anira dera ankachezera mpingo wa m’tauniyi. Anthu ena anafika ndi banja lawo lonse ndipo ena anali achikulire. Onsewo anagona m’nyumba imodzi ndipo ankakambirana komanso kufunsana mafunso mpaka usiku. Iwo ananena kuti anthu ambiri ochokera kumidziyo akufuna kukhala a Mboni chifukwa atopa ndi kuponderezedwa ndi atsogoleri a zipembedzo zawo.