Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Oceania

Oceania
  • MAYIKO 29

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 39,508,267

  • OFALITSA 96,088

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 63,333

“Tsopano Ndimamvetsa Zomwe Zikunenedwa”

Freda, yemwe ndi wosamva, anasangalala kwambiri atamva kuti iyeyo ndi mlongo amene amamuphunzitsa Baibulo azisonkhana ndi mpingo woyamba wa chinenero chamanja ku Papua New Guinea. Mpingowu unakhazikitsidwa pa March 1, 2013 ndipo Freda akuona kuti tsopano amamvetsa bwino zimene zikunenedwa pa misonkhano kusiyana ndi mmene ankachitira poyamba. Zili choncho chifukwa  tsopano safunikanso kugwiritsa ntchito mabuku koma amangoyang’ana munthu amene akulankhula m’chinenero chamanja kupulatifomu. Zimenezi zinamuthandiza kuchotsa manyazi ndipo tsopano amayankha pa misonkhano komanso kuchita mbali zina. Freda anakhala wofalitsa wosabatizidwa mu April 2013 ndipo akulimbikitsa ena omwenso ndi osamva kuti azipezeka pa misonkhano. Nthawi zambiri Freda amalira akakhala pa misonkhano. Atamufunsa chifukwa chake amachita zimenezi, iye anayankha kuti: “Ndikusangalala kwambiri chifukwa tsopano ndimamvetsa zomwe zikunenedwa.”

Anakwera M’galimoto Yolakwika

Tsiku lina Barbara, yemwe amakhala ku Australia, ankapita mu utumiki pa galimoto yake. Kenako anaima pamalo ena kuti aone ngati watenga buku lina limene ankafuna kukapatsa munthu pa ulendo wobwereza. Koma mwadzidzidzi, anangoona mayi wina watsegula chitseko cha galimotoyo, n’kulowa.

Modabwa, Barbara anauza mayiyo kuti: “Mayi, ndikuona ngati mwakwera galimoto yolakwika.”

Mayiyo anati: “Pepani, ndimaganiza kuti ndi galimoto ya amayi enaake, yomwe ndimakwera.” Mayiyu ataona magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! omwe anali m’galimotomo anati: “Panali amayi enaake awiri amene ankandiphunzitsa Baibulo, ndipo ankandipatsa magazini ngati amenewa.” Barbara anapatsa mayiyo magazini ndipo kenako anayamba kuphunzira naye Baibulo.

“Makalata Ochokera kwa Mulungu”

New Zealand: Violet amauza anthu ambiri choonadi kudzera m’makalata

Violet, ndi mlongo wa zaka 82 yemwe amakhala mumzinda wa Christchurch ku New Zealand ndipo amadwaladwala. Mlongoyu amakonda kulemba makalata n’kumatumiza  m’zipatala ndi malo amene amasungirako okalamba ndipo amaikamo mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Manesi amene amapereka makalatawa kwa anthu okalamba, ananena kuti anthu achikulirewo amasangalala kwambiri ndi makalatawa ndipo amati ndi ochokera kwa Mulungu. Ena amati akawerenga kalata ndi buku limene alandira, amasinthana ndi anzawo ndipo enanso amawerenga mokweza n’cholinga choti anzawo amene satha kuona bwino azimva nawo. Manesiwa ananenanso kuti anthu amene amalandira makalata ndi mabukuwa, amakhala odekha, osangalala komanso amakhala bwino ndi anzawo kusiyana ndi amene salandira mabukuwa.  Violet anati: “Ndikuona kuti Yehova akundigwiritsabe ntchito kuthandiza ena. Kuuza ena choonadi pogwiritsa ntchito njira imeneyi, kumandilimbikitsa kwabasi.”

Anawerenga Nkhani Yonena za Maluwa

Loweruka lina m’mawa, mlongo wina wa pachilumba cha Saipan, dzina lake Bernie ankafuna kupatsa magazini atsopano a Nsanja ya Olonda mtsikana wa pakoleji ina, dzina lake Bernadette. Koma anadabwa kwambiri mtsikanayo atayankha kuti: “Ndawerenga kale magazini amenewo.” Ndiyeno Bernie anatenga magazini ena m’chikwama chake kuti am’patse, koma mtsikanayo anayankhanso kuti: “Amenewanso ndawawerenga kale.” Bernie anadabwa kwambiri ndi zimenezi ndipo anamufunsa kuti: “Mwawapeza kuti magazini amene mwawerengawo? Kapena ndinu mlongo ndipo mwangobwera kumene kudera lino?” Bernadette anayankha kuti si wa Mboni koma anali atawerenga magaziniwo pa Intaneti. Iye anati tsiku lina ankafufuza pa Intaneti zokhudza maluwa enaake ndipo analemba dzina la maluwawo. Anadabwa patabwera nkhani yakuti, “Maluwa Okongola Mokopa a ku Africa” imene ili mu Galamukani! ndipo ikupezekanso pa webusaiti yathu. Bernadette anauza Bernie kuti anasangalala kwambiri ndi nkhaniyo moti anaganiza zofufuza zinthu zinanso pa webusaitiyi. Poyamba ankangofufuza zokhudza zomera ndi nyama koma kenako anapeza mfundo zochititsa chidwi zokhudza Baibulo. Bernie ataona kuti Bernadette ali ndi chidwi, anamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo ndipo pa ulendo wotsatira anamupititsira buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Pa ulendo wachitatu, anayamba kuphunzira mutu woyamba wa m’bukuli. Bernadette anapita patsogolo mofulumira moti anabatizidwa mu November 2012 patangotha chaka chimodzi chokha. Chifukwa cha zimenezi, anzake ankamunena moseka kuti “anathamangira” m’choonadi. Apatu n’zoonekeratu kuti webusaiti yathu inamuthandiza kuti aphunzire choonadi.