Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Mfundo Zachidule Zokhudza Mayiko a Sierra Leone ndi Guinea

Mfundo Zachidule Zokhudza Mayiko a Sierra Leone ndi Guinea

Mmene Mayikowa Alili Mayiko onsewa ali ndi madambo a m’mphepete mwa nyanja, zigwa ndiponso mapiri. Ku Guinea n’kumene kunayambira mitsinje ikuluikulu ya ku West Africa yomwe ndi Gambia, Niger ndi Senegal.

Anthu Ku Sierra Leone kuli mitundu 18 ya anthu koma mitundu ikuluikulu ndi ya Amende ndi Atemne. Akiliyo, omwe ndi mbadwa za anthu amene anamasulidwa ku ukapolo, amakhala cha ku Freetown. Ku Guinea kuli mitundu 30 ya anthu ndipo mitundu ikuluikulu ndi ya Afulani, Amandingo ndi Asusu. *

Chipembedzo Pa anthu 100 alionse a ku Sierra Leone, 60 ndi asilamu ndipo ena otsalawo amati ndi Akhristu. Pa anthu 100 alionse ku Guinea, 90 ndi asilamu. M’mayiko onsewa, anthu ambiri amapembedzanso milungu ya makolo awo.

 Zilankhulo Mtundu uliwonse wa anthu uli ndi chilankhulo chake. Koma chilankhulo chachikulu ku Sierra Leone ndi Chikiliyo. M’chilankhulochi amaphatikiza mawu achingelezi, a zinenero za ku Ulaya komanso za ku Africa. Chilankhulo chachikulu cha ku Guinea ndi Chifulenchi. Koma anthu ambiri m’mayikowa sadziwa kuwerenga ndi kulemba.

Ntchito zawo Anthu ambiri m’mayikowa ndi alimi. Dziko la Sierra Leone limadaliranso miyala ya dayamondi imene limagulitsa m’mayiko akunja. Pa dziko lonse lapansi, ku Guinea n’kumene kuli mtapo wa aluminiyamu wambiri.

Chakudya Anthu a m’mayikowa amakonda kunena kuti, “Ngati sindinadye mpunga ndiye kuti ndagona ndi njala.” Amaphikanso chinangwa kenako n’kuchipota. Chakudya chimenechi amachitchula kuti Fufu ndipo kawirikawiri amadyera nyama, therere ndiponso msuzi wowawasa.

Nyengo M’mphepete mwa nyanja mumatentha kwambiri, koma kumapiri kumazizira. M’chilimwe kumabwera mphepo yochokera kuchipululu cha Sahara yotchedwa harmattan. Mphepoyi imaomba kwa masiku angapo ndipo imachititsa kuti kuzizire koma imabweretsa fumbi losaneneka.

^ ndime 4 Mitundu ina imadziwika ndi mayina angapo.

 

SIERRA LEONE

GUINEA

KUKULA KWAKE

27,699 (71,740 sq km)

94,926 (245,857 sq km)

KULI ANTHU

6,092,000

11,745,000

OFALITSA MU 2013

2,039

748

ALIYENSE AFUNIKA KUPHUNZITSA ANTHU

2,988

15,702

OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO MU 2013

8,297

3,609