Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE AND GUINEA

Baji Yawo Inali Ngati Pasipoti

Baji Yawo Inali Ngati Pasipoti

“MU 1987 anthu oposa 1,000 anafika pa msonkhano wachigawo wa mutu wakuti, ‘Khulupirirani Yehova’ womwe unachitikira ku Guékédou, m’dziko la Guinea. Popeza kuti malo a msonkhano anali m’malire a dziko la Sierra Leone ndiponso Liberia, anthu ena ankangoyendera kuchokera m’mayiko awiriwa. Komano vuto linali mapasipoti. Choncho abale ena anakambirana ndi akuluakulu a boma a m’malirewa ndipo anagwirizana zoti anthuwo azingosonyeza baji yawo n’kudutsa. Apolisi a m’malirewo akangoona baji yaolenji ankangoti dutsani.”—Everett Berry, yemwe anali mmishonale.

Abale ankalandira chakudya pa msonkhanowu