Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

North ndi South America

North ndi South America
  • MAYIKO 57

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 970,234,987

  • OFALITSA 3,943,337

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 4,341,698

Anawaitana Kuti Akakhale Kunyumba Kwawo

Banja lina la mumzinda wa Las Vegas ku Nevada, linkafuna malo abata oti lizikakhala. Choncho linagulitsa nyumba yawo kuti lisamukire ku Dominican Republic. Koma anafunika kuchoka m’nyumbayo kutatsala masiku 10 kuti anyamuke. Ndiyeno a Mboni za Yehova amene ankakhala nawo pafupi anawaitana kuti akakhale kunyumba kwawo pa masikuwo. Ali kunyumbayo anapita nawo ku  Nyumba ya Ufumu ndipo anachita chidwi atamva za chaka cha 1914. Iwo ankadziwa kuti chaka chimenechi n’chosaiwalika. Atafika ku Dominican Republic, anapempha a Mboni za Yehova amene anadzawalalikira kuti aziphunzira nawo Baibulo. Patangopita chaka chimodzi ndi miyezi iwiri, banjali linadzipereka kwa Mulungu ndipo linabatizidwa.

Anapeza Zimene Ankafuna

Pa chionetsero cha mabuku chimene chinachitika ku Panama City, m’dziko la Panama, abale anaikanso tebulo la mabuku. Atsikana awiri atafika patebulolo, mmodzi anauza mlongo amene anali pamenepo kuti pali zinazake zimene zikumukhumudwitsa. Anafotokoza kuti bambo ake amakonda kwambiri mankhwala osokoneza bongo. Mlongoyo anamusonyeza buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri pa mutu 23 wakuti “Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?”Mtsikanayo anati: “Zimenezi zindithandiza kwambiri.” Atsikanawo anamukumbatira mlongoyo ndipo patadutsa ola limodzi anabwereranso kudzamuyamikira. Pa masiku 5 a chionetserochi, abalewa anagawira mabuku 1,046, magazini 1,116 ndi timabuku 449. Anthu 56 anapereka maadiresi kuti Mboni zidzakawachezere.

Ankalalikira Yekhayekha kwa Zaka 4

Fredy, yemwe amalankhula Chikabeka, amakhala kudera la mapiri m’dziko la Costa Rica.Pafupifupi zaka 4 zapitazo, pamene Fredy ankagwira ntchito mumzinda wa San José, womwe ndi likulu la dzikoli, analandira buku lakuti   Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndiponso kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Wa Mboni amene anamugawira mabukuwa anamuuza kuti apite kwawo kukalalikira anthu a kumeneko. Choncho abwerera kwawo ndipo anaphunzira payekha buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kenako anasintha makhalidwe ake ndipo analembetsa ukwati wake. Ndiyeno ankayesetsa kuphunzitsa Baibulo anthu olankhula Chikabeka.

Fredy anakonza zoti pakhale makalasi 6 ophunzitsa Baibulo. Ndipo anagawa ophunzirawo m’makalasi malinga ndi mmene anakhozera mayeso. Iye ankachititsa misonkhano komanso Chikumbutso. Anapanganso timapepala toitanira anthu ku Chikumbutsocho. Timapepalato tinali ndi mawu akuti: “A Mboni za Yehova akukuitanirani ku Chikumbutso cha imfa ya Khristu.” Iye anachita zimenezi kwa zaka 4 popanda kuonana ndi Mboni. Koma ankapempha Yehova kuti a Mboni ena abwere kudzamuthandiza.

Posachedwapa, pemphero la Fredy linayankhidwa. A Mboni ena anayenda ulendo wovuta wopita kwawo kwa Fredy ndipo anadabwa kwambiri kuona zimene anachitazo. Iwo anati: “Ngakhale kuti Fredy ndi wosabatizidwa, amachita zinthu ngati wa Mboni.” Patangotha miyezi itatu, anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Kuti akabatizidwe, anayenera kutsika mapiri n’kupita ku msonkhano wake wachigawo woyamba. Iye anabwera ndi anthu 19 amene ankaphunzira nawo Baibulo. Panopa wayambitsa timagulu titatu tina ta anthu olankhula Chikabeka m’madera akutali.

Costa Rica: Fredy, yemwe ndi mpainiya wokhazikika, amapita kutali kukaphunzitsa anthu Baibulo

Analimba Mtima Kufotokoza Zimene Amakhulupirira

Ku United States kuli mtsikana wina wakusekondale dzina lake Anna. Tsiku lina anzake anamukwiyira kwambiri atamva kuti iye sakhulupirira Utatu. Anna anati:  “Anzangawo anandilusira kwambiri koma ndinayesetsa kuchita zinthu modekha. Sindinafune kuti anthu aganize kuti a Mboni za Yehova ndi anthu ovuta.” Usiku wa tsiku limenelo, iye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima. Anafufuzanso zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Tsiku lotsatira, Anna anatenga Baibulo popita kusukulu. Gulu la anzakewo linabwera pafupi ndipo ena ankamuseka. Koma iye analimba mtima n’kukambirana nawo malemba angapo. Kenako onse amene ankamutsutsawo anasowa chonena. Mtsogoleri wa amene ankamutsutsawo, yemwenso anali ndi udindo m’kalasi, ananena kuti tsopano ayamba kulemekeza Mboni za Yehova. Iye anapitiriza kufunsa Anna mafunso ambiri okhudza zimene amakhulupirira.

Lamba wa Nsapato Anadukira Pamalo Abwino

Pamene mtsikana wina wa ku Barbados, ankapita kutchalitchi, lamba wa nsapato yake anaduka. Iye anakhotera panyumba ina kuti akabwereke phinifolo kuti akonze  nsapatoyo. Kunyumbayo kunkakhala mlongo wina ndi mwana wake. Pomwe mtsikanayo ankakonza nsapato yakeyo, mlongoyo anayamba kumusonyeza kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa masiku ano. Mwana wa mlongoyo anamuitana mtsikanayo kuti apite nawo ku misonkhano. Poona kuti wachedwa kutchalitchi kwake, mtsikanayo anavomera. Pa misonkhanoyo, iye ankatsatira nawo malemba onse m’Baibulo lake. Anasangalala kwambiri ndi misonkhanoyo. Iye ananena kuti anali atatopa ndi ng’oma komanso phokoso kutchalitchi kwake ndipo ankafunitsitsa kuphunzira Baibulo pamalo abata. Analandira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Iye amapita ku misonkhano yonse ndipo amakonda kwambiri kuyankha.

Pali Mmodzi Yekha Yemwe Angamuletse Kulalikira

M’bale wina wachinyamata ku Guyana anati: “Ndimakonda kulalikira kwa anzanga kusukulu. Koma kuli mnyamata wina amene sasangalala nazo. Tsiku lina anandikanikizira kukhoma n’kundiuza kuti, ‘Iwe, usiyiretu kulalikira.’ Ndinamuyankha kuti, ‘Yehova yekha ndi amene angandiletse kulalikira.’ Pamene ndinkapitiriza kulalikira, mnyamatayu anang’amba chikwama changa. Kenako anandimenya chibakera mpaka kundivulaza mlomo. Mphunzitsi wamkulu anatiuza tonsefe kuti tipite ku ofesi kwawo. Iwo anandifunsa chomwe ndinamulakwira mnyamatayo kuti andimenye. Ndinanena kuti anandimenya chifukwa chakuti ndinkalalikira uthenga wabwino. Kenako anandifunsa kuti, ‘Bwanji sunam’bwezere? Ukanachita bwino kum’bwezera.’ Ndinawauza kuti ndinaphunzira m’Baibulo pa lemba la Aroma 12:17 kuti Akhristu sayenera ‘kubwezera choipa pa choipa.’ Atamva zimenezi, ananena kuti ndingapite ndipo athana ndi mnyamatayo.”

Catamarca, Argentina