Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lemba la Chaka cha 2014

“Ufumu Wanu Ubwere.”Mateyu 6:10

Lemba la Chaka cha 2014

Zaka pafupifupi 100 zapitazo, Yehova anaika Yesu pampando wachifumu kumwamba. Kuyambira nthawi imeneyo, atumiki a Mulungu akhala akulengeza mwakhama madalitso amene Ufumu wa Khristu udzabweretse. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri Yesu akadzayamba kulamulira dzikoli mwachikondi. Dzikoli lidzakhala Paradaiso ndipo anthu onse adzakhala okondana. Sipadzakhala chiwawa, kumenyana, kudwala, kuvutika komanso imfa.

Posachedwapa, tidzaona zinthu zosangalatsazi zikuchitika. Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndipo ukadzabwera, zinthu zonse zimene Yehova analonjeza zidzachitika. Tizipemphera kuti Ufumuwu ubwere, tiziuza ena za Ufumuwu ndiponso tiziganizira zinthu zonse zimene udzachita.