Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Magulu Ochita Zamizimu

Magulu Ochita Zamizimu

MAGULU ochita zamizimu ndi ofala kwambiri ku West Africa ndipo m’maguluwa mumapezeka anthu ochokera m’mitundu, zikhalidwe komanso zilankhulo zosiyanasiyana. Magulu amenewa amatsogolera anthu awo pa zinthu zosiyanasiyana monga zokhudza chikhalidwe, maphunziro komanso ndale. Koma zinthu zambiri zimene amachita ndi zokhudza chipembedzo. Pa maguluwa pali magulu awiri akuluakulu, gulu lotchedwa Poro (lomwe ndi la amuna) ndi gulu lotchedwa Sande (lomwe ndi la akazi). * Buku lina linanena kuti gulu la Poro “limathandiza kuti mizimu isamavutitse anthu koma iziwathandiza.”—Initiation, 1986.

Anthu akalowa m’gulu la Poro amaphunzitsidwa matsenga, ufiti ndiponso amawatema mphini. Anthu atsopano amene alowa m’gulu la Sande amawaphunzitsanso zamatsenga ndiponso amachita mdulidwe wa akazi ngakhale kuti mwambowu unatha m’madera ena.

Magulu ena ochita zamizimu amalimbikitsa chiwerewere komanso amagwiritsa ntchito njira zamizimu poyesa kuchiza misala ndi matenda ena. Pa nthawi ya nkhondo yapachiweniweni ku Sierra Leone, gulu lina linkanena kuti anthu ake sangawomberedwe. Komatu limeneli linali bodza.

Mamembala a maguluwa amauzidwa kuti asamaulule zinsinsi kwa anthu ena. Munthu akapanda kumvera malamulo a gulu lawo amaphedwa.

^ ndime 3 M’madera ena, gulu lotchedwa Sande limadziwikanso kuti Bondo.