Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Anamupatsa Dzina Loti “Baibulo” Brown

William R. Brown

Anamupatsa Dzina Loti “Baibulo” Brown
  • CHAKA CHOBADWA 1879

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1908

  • MBIRI YAKE Anali woyamba kutsogolera ntchito yolalikira ku West Africa.

MU 1907, William akugwira ntchito yokonza ngalande yaikulu yotchedwa Panama Canal, anatulukira pamalo ena pamene M’bale Isaiah Richards ankakamba nkhani m’mbali mwa msewu. Pokamba nkhaniyi ankagwiritsa ntchito tchati chosonyeza zimene Mulungu wakhala akuchita pokwaniritsa cholinga chake. Nthawi yomweyo, William anadziwa kuti wapeza chipembedzo choona ndipo anabwerera ku Jamaica kuti akaphunzitse mayi ake ndi mchemwali wake. Kenako nawonso anakhala Ophunzira Baibulo.

M’bale Brown anatumikira mumzinda wa Panama kwa kanthawi. Ali komweko anakumana ndi Evander J. Coward, amene anatumizidwa ndi Watch Tower Society kuti azikakamba nkhani ku Panama. M’bale Coward anali wodziwa kukamba nkhani mwaluso, ndipo anthu ambiri ankakhamukira ku nkhani zake. Ataona khama la M’bale Brown, anamuuza kuti apitire limodzi kukalalikira ku Trinidad.

 Kwa zaka 10 kapena kuposerapo, M’bale Brown ankayendayenda ku West Indies. Iye ankalimbikitsa timagulu ta Ophunzira Baibulo komanso kuchita upainiya. Mu 1920, m’baleyu anakwatira mlongo wina wokhulupirika dzina lake Antonia. Patangodutsa masiku awiri kuchokera pa tsiku la ukwati, iwo anauyamba ulendo wa kukachilumba ka Montserrat ku Leeward Islands. Iwo ankaonetsa Sewero la Pakanema la Chilengedwe. Analalikiranso kuzilumba za Barbados, Dominica ndi Grenada. Apatu tingati analiyamba bwino banja lawoli.

Patapita zaka ziwiri, m’baleyu analembera kalata Joseph F. Rutherford amene pa nthawiyo ankayang’anira ntchito ya anthu a Yehova. M’kalatayo anati: “Yehova wandithandiza kulalikira m’zilumba zambiri za kuno ndipo panopa kuli ophunzira ambiri. Kodi ndipitirize kuzungulira m’zilumbazi?” Pasanapite masiku ambiri, M’bale Rutherford anamuyankha kuti: “Upite kudziko la Sierra Leone ku West Africa ndipo utenge mkazi wako ndi mwana wako.”

Pa zaka 27 zimene M’bale Brown anatumikira ku West Africa limodzi ndi banja lake, iye sankakonda kukhala mu ofesi. Ankangofuna kulalikira basi. Popeza ankagwiritsa ntchito Baibulo nthawi zonse pophunzitsa, anthu anamupatsa dzina loti “Baibulo” Brown.

Mu 1950, M’baleyu ali ndi zaka 71, anabwerera ndi mkazi wake ku Jamaica n’kumakachita upainiya. Iye sanasiye upainiya mpaka pamene anamaliza utumiki wake padzikoli mu 1967. Kunena zoona, m’baleyu ankakonda upainiya. Ankaona kuti upainiya ndi mwayi waukulu kwambiri.