Esitere 2:1-23

2  Pambuyo pake, mkwiyo wa Mfumu Ahasiwero+ utachepa, iye anakumbukira Vasiti+ ndi zimene anachita,+ komanso chilango chimene anasankha kum’patsa.+  Ndiyeno atumiki a mfumu, amene anali nduna zake,+ anati: “Pakhale anthu oti afufuzire+ mfumu atsikana, anamwali+ okongola.  Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu m’zigawo zonse+ za ufumu wanu. Anthuwo asonkhanitse pamodzi atsikana onse, anamwali okongola, kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ m’nyumba ya akazi imene Hegai+ akuyang’anira. Iye ndi munthu wofulidwa wa mfumu+ woyang’anira akazi, amenenso ndi mkulu woyang’anira nyumba ya akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa.  Mtsikana amene mtima wanu mfumu udzakondwere naye adzakhala mfumukazi m’malo mwa Vasiti.”+ Mawu amenewa anasangalatsa mfumu, ndipo inachitadi zomwezo.  Tsopano mwamuna wina, Myuda, anali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Mwamunayu dzina lake anali Moredekai+ mwana wa Yairi, mwana wa Simeyi amene anali mwana wa Kisi M’benjamini.+  Moredekai anali atatengedwa ku Yerusalemu pamodzi ndi anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+ Anthuwa ndi amene anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya+ mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anam’tenga kupita naye ku ukapolo.  Moredekai ndi amene analera+ Hadasa, amene ndi Esitere, mwana wa m’bale wa bambo ake,+ chifukwa analibe bambo kapena mayi. Mtsikanayu anali wooneka bwino ndi wokongola kwambiri.+ Bambo ndi mayi a mtsikanayu atamwalira, Moredekai anam’tenga ngati mwana wake.  Ndiyeno mawu a mfumu ndi malamulo ake atamveka, komanso atsikana ambiri atawasonkhanitsa pamodzi kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani+ kuti Hegai+ aziwayang’anira, Esitere nayenso anam’tengera kunyumba ya mfumu komweko kuti Hegai woyang’anira akazi azimuyang’anira.  Tsopano Hegai anasangalala naye mtsikanayu moti anam’sonyeza kukoma mtima kosatha.+ Mwamsanga anam’paka mafuta okongoletsa,+ anam’patsa chakudya chapadera ndiponso anam’patsa atsikana 7 osankhidwa kuchokera kunyumba ya mfumu. Kenako anam’samutsa pamodzi ndi atsikanawo n’kuwapatsa malo abwino kwambiri m’nyumba ya akaziyo. 10  Esitere sananene za mtundu wa anthu ake+ kapena za abale ake, pakuti Moredekai anali atamulamula kuti asanene kalikonse.+ 11  Ndipo tsiku lililonse Moredekai anali kuyenda m’bwalo la nyumba ya akazi kuti adziwe mmene Esitere anali kukhalira ndi zimene zinali kum’chitikira. 12  Mtsikana aliyense anali kukaonekera kwa Mfumu Ahasiwero pambuyo poti am’chitira zonse zimene amayenera kum’chitira pa miyezi 12 malinga ndi lamulo lokhudza akazi. Atsikanawo anali kuwapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako anali kuwapaka mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ndiye kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera. 13  Zimenezi zikachitika, mtsikana aliyense anali kubwera kwa mfumu. Anali kum’patsa chilichonse chimene wapempha kuti atenge pochokera kunyumba ya akazi kupita kunyumba ya mfumu.+ 14  Madzulo mtsikanayo anali kubwera kwa mfumu, ndipo m’mawa anali kubwerera kunyumba yachiwiri ya akazi, imene Sasigazi anali kuyang’anira. Sasigazi anali munthu wofulidwa wa mfumu,+ mkulu woyang’anira akazi. Mtsikanayo sanalinso kubwera kwa mfumu pokhapokha ngati mfumuyo yakondwera naye ndipo yamuitanitsa mwa kum’tchula dzina.+ 15  Ndiyeno nthawi itakwana yoti Esitere akaonekere kwa mfumu, sanapemphe kalikonse+ kupatulapo zimene Hegai+ anatchula. Iye anali munthu wofulidwa wa mfumu woyang’anira akazi, amenenso anali mkulu woyang’anira nyumba ya akazi. Esitere anali mwana wa Abihaili, m’bale wa bambo ake a Moredekai, amene Moredekai anamutenga ngati mwana wake+ (pa nthawi imeneyi Esitere anali kukondedwa ndi aliyense womuona).+ 16  Pamenepo anatenga Esitere kupita naye kwa Mfumu Ahasiwero, kunyumba yake yachifumu, m’mwezi wa 10 umene ndi mwezi wa Tebeti,* m’chaka cha 7+ cha ulamuliro wa Mfumu Ahasiwero. 17  Ndiyeno mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti mfumu inakondwera naye ndipo inamusonyeza kukoma mtima kosatha kuposa anamwali ena onse.+ Pamenepo mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake ndi kumusandutsa mfumukazi+ m’malo mwa Vasiti. 18  Kenako mfumu inakonzera akalonga ake ndi atumiki ake onse phwando lalikulu, phwando la Esitere. Ndiyeno mfumu inamasula+ anthu m’madera ake onse, ndipo inali kupereka mphatso zimene mfumu yokha ndiyo ikanatha kupereka mphatso zoterozo. 19  Pamene anamwali+ anasonkhanitsidwa pamodzi kachiwiri, Moredekai anali atakhala pansi kuchipata cha mfumu.+ 20  Esitere sanali kunena za abale ake ndi anthu a mtundu wake,+ monga mmene Moredekai+ anamulamulira.+ Esitere anali kuchita zimene Moredekai wanena monga mmene anali kuchitira pa nthawi imene Moredekai anali kumusunga.+ 21  M’masiku amenewo, pamene Moredekai anali kukhala pansi kuchipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, nduna ziwiri za panyumba ya mfumu, amenenso anali alonda a pakhomo, anakwiya ndipo anafuna kupha+ Mfumu Ahasiwero. 22  Ndiyeno zimenezi zinadziwika kwa Moredekai ndipo iye mofulumira anauza+ Mfumukazi Esitere. Kenako Esitere analankhula ndi mfumu m’malo mwa Moredekai.+ 23  Choncho nkhani imeneyi anaifufuza ndipo pamapeto pake zonse zinadziwika, ndipo onse awiri, Bigitana ndi Teresi anapachikidwa+ pamtengo.+ Kenako zimenezi zinalembedwa pamaso pa mfumu m’buku la zochitika+ za m’masiku amenewo.

Mawu a M'munsi

“Mule” ndi madzi onunkhira ochokera kumitengo inayake, ndipo nthawi zina madziwa anali kupangira mafuta odzola.
Onani Zakumapeto 13.