Esitere 7:1-10

7  Kenako mfumu ndi Hamani+ anafika kudzachita phwando ndi Mfumukazi Esitere.  Tsopano mfumu inafunsanso Esitere pa tsiku lachiwiri la phwando la vinyo kuti:+ “Ukufuna kupempha chiyani+ Mfumukazi Esitere? Chimene ukufunacho ndikupatsa.+ Ukufuna chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu,+ ipatsidwa kwa iwe.”  Pamenepo Mfumukazi Esitere inayankha kuti: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndipo ngati zingakukomereni, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga+ komanso kuti musawononge anthu a mtundu wanga.+  Pakuti ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa+ kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa.+ Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna+ ndi akapolo aakazi ndikanakhala chete. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike chifukwa liwonongetsa zinthu zambiri za mfumu.”  Tsopano Mfumu Ahasiwero inalankhula ndipo inafunsa Mfumukazi Esitere kuti: “Ndani wachita zimenezi,+ ndipo ali kuti munthu amene wadzikuza+ ndi kuchita zinthu zoterezi?”  Poyankha Esitere anati: “Munthu wake ndi uyu, Hamani, mdani ndiponso munthu woipa.”+ Pamenepo Hamani anachita mantha+ chifukwa cha mfumu ndi mfumukazi.  Ndiyeno mfumu inanyamuka mokwiya+ kuchoka paphwando la vinyo ndi kupita kumunda wamaluwa wa panyumba ya mfumu. Pamenepo Hamani ananyamuka kuti apemphe Mfumukazi Esitere kuti ipulumutse moyo wake,+ chifukwa anaona kuti mfumu yatsimikiza zomupatsa chilango.+  Kenako mfumu inabwera kuchokera kumunda wamaluwa wa panyumba ya mfumu ndi kulowanso m’nyumba imene munali phwando la vinyo.+ Pamenepo inaona Hamani atadzigwetsa pampando wokhala ngati bedi+ pamene panali Esitere. Choncho mfumu inati: “Kodi ukufunanso kugwirira mfumukazi ine ndili m’nyumba mom’muno?” Mfumu italankhula,+ Hamani anamuphimba nkhope.  Haribona,+ mmodzi mwa nduna za panyumba ya mfumu+ amene anali pamaso pa mfumu anati: “Palinso mtengo+ umene Hamani anapangira Moredekai, amene analankhula zabwino za mfumu.+ Mtengowu uli m’nyumba ya Hamani ndipo ndi wotalika mikono 50.” Pamenepo mfumu inati: “Amuna inu, kam’pachikeni pamtengo umenewo.”+ 10  Choncho anapachika Hamani pamtengo+ umene anakonzera Moredekai,+ ndipo mkwiyo wa mfumu unatha.

Mawu a M'munsi