Esitere 4:1-17

4  Moredekai+ anadziwa zonse zimene zinachitika.+ Choncho anang’amba zovala zake ndi kuvala chiguduli*+ ndipo anadzithira phulusa+ ndi kutuluka kupita pakati pa mzinda. Ndiyeno anayamba kulira mofuula ndiponso mopwetekedwa mtima.+  Kenako anafika pafupi ndi chipata cha mfumu,+ pakuti palibe amene anali kuloledwa kufika pachipata cha mfumu atavala chiguduli.  Ndipo m’zigawo zonse,+ kulikonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, Ayuda anali ndi chisoni kwambiri+ ndipo anali kusala kudya,+ kubuma ndi kulira mofuula. Ambiri anayala ziguduli+ ndi kuwazapo phulusa+ kuti agonepo.  Ndiyeno atsikana otumikira Esitere ndi amuna ofulidwa+ amene anali kumuyang’anira anayamba kubwera kudzamuuza zimenezi. Ndipo mfumukaziyo inamva chisoni kwambiri, choncho inatumiza zovala kuti Moredekai akavule zigudulizo ndi kuvala zovalazo, koma Moredekai sanalole.+  Pamenepo Esitere anaitana Hataki,+ mmodzi mwa amuna ofulidwa a mfumu amene mfumuyo inamuika kuti azitumikira Esitere. Ndiyeno anamutumiza kwa Moredekai kuti akafufuze zimene zachitika.  Choncho Hataki anapita kwa Moredekai kubwalo la mzinda limene linali pafupi ndi chipata cha mfumu.  Kenako Moredekai anauza Hataki zonse zimene zamuchitikira.+ Anamuuzanso zonse zokhudza ndalama zimene Hamani ananena kuti apereka mosungiramo chuma cha mfumu,+ n’cholinga chofuna kuwononga Ayuda.+  Ndiyeno anapatsa Hataki kalata+ imene munali lamulo lochokera ku Susani+ lakuti Ayuda afafanizidwe. Anamupatsa kalata imeneyi kuti akaonetse Esitere ndi kumuuza+ kuti akaonekere kwa mfumu ndi kuipempha kuti iwakomere mtima,+ ndiponso kuti Esitere akachonderere mfumu mwachindunji m’malo mwa anthu a mtundu wake.+  Ndiyeno Hataki+ anapita kukauza Esitere mawu a Moredekai. 10  Kenako Esitere anauza Hataki kuti akauze Moredekai+ mawu akuti: 11  “Atumiki onse a mfumu ndi anthu a m’zigawo za mfumu akudziwa kuti mfumu ili ndi lamulo limodzi lokhudza mwamuna kapena mkazi aliyense wokaonekera kwa iye m’bwalo lamkati+ asanaitanidwe. Lamuloli+ ndi lakuti aphedwe. Koma ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yachifumu ya golide, pamenepo adzakhala ndi moyo.+ Ndiye ine sindinaitanidwe kukaonekera kwa mfumu kwa masiku 30 tsopano.” 12  Ndiyeno Moredekai anauzidwa mawu a Esitere. 13  Kenako Moredekai anayankha Esitere kuti: “Usaganize kuti iwe wekha udzapulumuka mwa Ayuda onse chifukwa chakuti uli m’nyumba ya mfumu.+ 14  Pakuti ngati iwe ukhala chete pa nthawi ino, thandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina.+ Koma anthu inu, iwe ndi nyumba ya bambo ako, nonse mudzatheratu. Ndipo ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.”+ 15  Poyankha, Esitere anatumiza uthenga kwa Moredekai kuti: 16  “Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse amene angapezeke ku Susani+ ndipo musale kudya+ m’malo mwa ine. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu,+ usana ndi usiku. Inenso pamodzi ndi atsikana anga onditumikira+ tisala kudya. Pamenepo, ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu, ndipo ngati n’kufa,+ ndife.” 17  Zitatero Moredekai anapita kukachita zonse zimene Esitere anamuuza.

Mawu a M'munsi

Ena amati “saka.”