Esitere 10:1-3

10  Ndiyeno Mfumu Ahasiwero inayambitsa ntchito ya ukapolo+ m’dzikomo ndi pazilumba+ za m’nyanja.  Koma ntchito zonse zamphamvu zimene anachita ndi mawu ofotokoza mphamvu zimene Moredekai+ anali nazo zimene mfumu inam’patsa,+ zinalembedwa m’Buku la zochitika+ za m’masiku a mafumu a Mediya ndi Perisiya.+  Moredekai Myuda anali wachiwiri+ kwa Mfumu Ahasiwero ndipo anali wotchuka pakati pa Ayuda. Khamu lonse la abale ake linali kukondwera naye. Iye anali kuchitira zabwino anthu a mtundu wake ndi kulankhula zamtendere+ kwa ana awo onse.

Mawu a M'munsi