Esitere 1:1-22

1  M’masiku a Ahasiwero,*+ amene anali kulamulira zigawo 127 monga mfumu, kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya,+  m’masiku amenewo mfumuyo inali kulamulira ili m’nyumba yachifumu+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri+ ya ku Susani.+  M’chaka chachitatu cha ulamuliro wake, Ahasiwero anakonzera phwando+ akalonga ndi atumiki ake onse, akuluakulu a asilikali a Perisiya+ ndi Mediya,+ anthu olemekezeka+ ndi akalonga a m’zigawo za ufumu wake.+  Masiku amenewo, iye anaonetsa anthuwo chuma+ chimene chinali kuchititsa anthu kumupatsa ulemu+ ndi ulemerero mu ufumu wake, komanso anawaonetsa kukongola kwa ufumu wakewo. Anawaonetsa zimenezi kwa masiku ambiri, masiku okwana 180.  Masiku amenewa atatha, mfumu inakonza phwando la masiku 7 m’munda wamaluwa, pabwalo la nyumba yake. Phwandoli inakonzera anthu onse okhala kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani, anthu olemekezeka ndi anthu wamba omwe.  Anapachika makatani a nsalu, makatani opangidwa ndi thonje labwino kwambiri ndi makatani abuluu.+ Makataniwo anawamanga ndi zingwe zopangidwa ndi nsalu zabwino kwambiri ndi zingwe zaubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira.+ Zingwezi anazikulunga pamikombero yasiliva ndi pazipilala za miyala ya mabo. Anazikulunganso pamipando+ yagolide ndi siliva yokhala ngati mabedi. Mipandoyi inali pakhonde la miyala ya pofeli,* miyala yoyera ya mabo, ngale ndi miyala yakuda ya mabo.  Anthu anali kulandira vinyo m’ziwiya zagolide.+ Chiwiya chilichonse chinali chosiyana ndi chinzake, ndipo vinyo amene mfumu inapereka+ anali wochuluka kwambiri, moti ndi mfumu yokha imene ikanatha kupereka vinyo wochuluka choncho.  Pa nthawiyo, palibe amene anali kuwakakamiza kutsatira malamulo a kamwedwe, pakuti umu ndi mmene mfumu inakonzera kuti aliyense wogwira ntchito kunyumba ya mfumu amwe mmene akufunira.  Nayonso Mfumukazi Vasiti+ inakonzera phwando akazi kunyumba ya Mfumu Ahasiwero. 10  Pa tsiku la 7, pamene mtima wa mfumu unali kukondwera ndi vinyo,+ mfumu inauza Mehumani, Bizita, Haribona,+ Bigita, Abagata, Zetara ndi Karikasi, nduna 7 za panyumba ya mfumu zimene zinali kutumikira+ Mfumu Ahasiwero, 11  kuti abweretse Mfumukazi Vasiti itavala duku lachifumu pamaso pa mfumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kuoneka bwino kwake, pakuti inalidi yokongola kwambiri.+ 12  Koma Mfumukazi Vasiti inakana+ kubwera itaitanidwa ndi mfumu kudzera mwa nduna za panyumba ya mfumu. Pamenepo mfumu inakwiya kwambiri ndipo mumtima mwake munali ukali waukulu.+ 13  Ndiyeno mfumu inalankhula ndi amuna anzeru,+ odziwa miyambo ya masiku amenewo.+ (Pakuti pa nkhani iliyonse, mfumu inali kufunsira kwa onse odziwa malamulo ndi nkhani zokhudzana ndi milandu. 14  Alangizi amene anali pafupi kwambiri ndi mfumu anali Karisena, Setara, Adimata, Tarisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, akalonga 7+ a Perisiya ndi Mediya, amene nthawi zonse anali kufika pamaso pa mfumu+ komanso anali ndi maudindo akuluakulu mu ufumuwo.) 15  Choncho mfumu inawafunsa kuti: “Popeza Mfumukazi Vasiti siinachite zimene Mfumu Ahasiwero yanena kudzera mwa nduna zake, kodi tichite nayo chiyani malinga ndi malamulo?” 16  Pamenepo Memukani+ anayankha pamaso pa mfumu ndi akalonga kuti: “Mfumukazi Vasiti siinalakwire mfumu yokha,+ koma yalakwiranso akalonga onse ndi anthu a mitundu yonse a m’zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero. 17  Pakuti zimene mfumukazi yachita zidziwika kwa akazi onse okwatiwa ndipo iwo ayamba kunyoza+ amuna awo+ ponena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero inalamula kuti Mfumukazi Vasiti ibwere pamaso pake koma Vasiti sanapite.’ 18  Lero akazi a akalonga a Perisiya ndi Mediya amene amva zimene mfumukazi yachita alankhula chimodzimodzi ndi akalonga onse a mfumu ndipo pakhala kunyozana ndi kukwiyitsana.+ 19  Ngati zingakukomereni mfumu,+ lamulani monga mfumu ndipo lamuloli alilembe m’malamulo+ a Perisiya ndi Mediya kuti zimene mwalamula zisasinthe.+ Mulamule kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso panu, inu Mfumu Ahasiwero, ndipo mupereke ulemu wake wachifumu kwa mkazi wina, mkazi wabwino kuposa iyeyu. 20  Lamulo limene inu mfumu mupereke limveke mu ufumu wanu wonse (chifukwa ndi waukulu), ndipo akazi onse okwatiwa adzalemekeza+ amuna awo,+ kaya amunawo ndi olemekezeka kapena anthu wamba.” 21  Mawu amenewa anali osangalatsa kwa mfumu+ ndi akalonga, ndipo mfumu inachita mogwirizana ndi mawu a Memukani. 22  Choncho mfumu inalemba makalata ndi kuwatumiza+ m’zigawo zonse za ufumu wake. Chigawo chilichonse+ anachilembera kalata malinga ndi mmene anthu a kumeneko amalembera ndiponso malinga ndi chinenero chawo. Anachita izi kuti mwamuna aliyense apitirize kutsogolera banja lake monga mutu,+ ndiponso kuti banjalo lizilankhula chinenero cha anthu a mtundu wa mwamunayo.

Mawu a M'munsi

“Ahaswero” amatchedwa Aritasasita m’Baibulo la Septuagint. Anthu amati iyeyu anali Sasita Woyamba, mwana wamwamuna wa Dariyo Wamkulu (Dariyo Hisitasipi).
“Pofeli” ndi mtundu wa mwala wolimba kwambiri. Kawirikawiri mwala umenewu umaoneka wakuda mofiirira, wokhala ndi mawanga oyera ndipo ndi wamtengo wapatali kwambiri.