Esitere 6:1-14

6  Usiku umenewo mfumu inasowa tulo.+ Choncho inaitanitsa buku limene anali kulembamo zochitika+ za m’masiku amenewo. Ndiyeno anawerenga zochitikazo pamaso pa mfumu.  M’bukumo anapeza kuti mwalembedwa zimene Moredekai anaulula+ zokhudza Bigitana ndi Teresi, nduna ziwiri+ za panyumba ya mfumu, alonda apakhomo, amene anafuna kupha Mfumu Ahasiwero.  Pamenepo mfumu inati: “Kodi Moredekai walandira ulemu ndi zinthu zazikulu zotani chifukwa cha zimene anachitazi?” Poyankha atumiki a mfumu, nduna zake, zinati: “Palibe chimene walandira.”+  Kenako mfumu inati: “Kodi m’bwalo muli ndani?” Tsopano Hamani anali atalowa m’bwalo lakunja+ kwa nyumba ya mfumu kudzauza mfumu kuti apachike Moredekai pamtengo+ umene anamukonzera.  Pamenepo atumiki a mfumu anati: “Hamani+ waima m’bwalomo.” Ndiyeno mfumu inati: “Muuzeni alowe.”  Hamani atalowa, mfumu inam’funsa kuti: “Kodi munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu tim’chitire chiyani?”+ Atamva zimenezi, Hamani ananena mumtima mwake kuti: “Kodi winanso ndani amene mfumu ingafune kum’patsa ulemu kuposa ine?”+  Choncho Hamani anauza mfumu kuti: “Munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu,  amubweretsere zovala zachifumu+ zimene mfumu imavala ndi hatchi* imene mfumu imakwera.+ Hatchiyo aiveke duku lachifumu.  Ndiyeno chovalacho ndi hatchiyo azipereke kwa mmodzi wa akalonga olemekezeka a mfumu.+ Akalongawo aveke chovalacho munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemuyo ndipo amukweze pahatchiyo ndi kumuyendetsa m’bwalo+ la mzinda.+ Ndipo azifuula pamaso pake kuti, ‘Umu ndi mmene timachitira ndi munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu.’”+ 10  Nthawi yomweyo mfumu inauza Hamani kuti: “Fulumira, tenga chovala ndi hatchi monga mmene wanenera, ndipo ukachitire zimenezi Moredekai, Myuda, amene ali kuchipata. Uonetsetse kuti zonse zimene wanenazi zakwaniritsidwa.”+ 11  Pamenepo Hamani anatenga chovala+ ndi hatchi, ndipo chovalacho anaveka Moredekai.+ Kenako anam’kwezeka pahatchiyo ndi kumuyendetsa m’bwalo+ la mzinda, akufuula pamaso pake kuti:+ “Umu ndi mmene timachitira ndi munthu amene mfumu yafuna kum’patsa ulemu.”+ 12  Zimenezi zitachitika, Moredekai anabwerera kuchipata cha mfumu.+ Koma Hamani anapita kunyumba kwake mofulumira, akulira ndiponso ataphimba kumutu.+ 13  Ndiyeno Hamani anafotokozera Zeresi+ mkazi wake ndi anzake onse chilichonse chimene chinam’chitikira. Pamenepo amuna anzeru+ amene anali kum’tumikira ndi Zeresi mkazi wake anati: “Ngati n’zoona kuti Moredekai amene iwe wayamba kugonja pamaso pake ndi Myuda, sudzamugonjetsa koma udzagonja ndithu pamaso pake.”+ 14  Pamene anali kukambirana naye zimenezi, nduna za panyumba ya mfumu zinafika, ndipo mofulumira+ zinatenga Hamani ndi kupita naye kuphwando+ limene Esitere anakonza.

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”