Esitere 8:1-17

8  Tsiku limenelo, Mfumu Ahasiwero inapereka kwa mfumukazi Esitere nyumba ya Hamani,+ amene anali kuchitira nkhanza Ayuda.+ Ndipo Moredekai anabwera pamaso pa mfumu chifukwa Esitere anali atauza mfumu ubale umene unalipo pakati pawo.+  Ndiyeno mfumu inavula mphete yake yodindira+ imene inalanda Hamani ndi kuipereka kwa Moredekai. Pamenepo Esitere anaika Moredekai kuti ayang’anire nyumba ya Hamani.+  Kuwonjezera pamenepo, Esitere analankhulanso ndi mfumu ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamapazi a mfumuyo. Iye analira+ ndi kuchonderera kuti mfumu imukomere mtima. Ndiponso kuti isinthe choipa+ cha Hamani Mwagagi ndi chiwembu+ chimene anakonzera Ayuda.+  Ndiyeno mfumu inaloza Esitere ndi ndodo yachifumu ya golide.+ Zitatero, Esitere anadzuka ndi kuima pamaso pa mfumu.  Tsopano Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima,+ komanso ngati n’zoyenera kwa inu mfumu ndiponso ngati ndine munthu wabwino kwa inu, palembedwe makalata ofafaniza makalata+ achiwembu amene Hamani, mwana wa Hamedata Mwagagi,+ analemba pofuna kuwononga Ayuda+ amene ali m’zigawo zanu zonse mfumu.+  Ndingapirire bwanji pamene ndikuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndipo ndingapirire bwanji pamene ndikuona abale anga akuwonongedwa?”  Choncho Mfumu Ahasiwero inauza mfumukazi Esitere ndi Moredekai Myuda kuti: “Nyumba ya Hamani ndaipereka kwa Esitere,+ ndipo Hamani wapachikidwa pamtengo+ chifukwa chakuti anatambasula dzanja lake ndi kuukira Ayuda.  Ndiye inu lembani makalata m’malo mwa Ayuda. Mulembe zimene mukuona kuti n’zabwino kwa inu m’dzina la mfumu.+ Mudinde makalatawo ndi mphete yodindira ya mfumu, pakuti n’zosatheka kufafaniza makalata amene alembedwa m’dzina la mfumu ndi kudindidwa ndi mphete yake yodindira.”+  Choncho anaitana alembi+ a mfumu pa nthawi imeneyo, m’mwezi wachitatu umene ndi mwezi wa Sivani,* pa tsiku la 23 la mweziwo. Iwo analemba makalatawo mogwirizana ndi zimene Moredekai ananena. Makalatawo anali opita kwa Ayuda, masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi akalonga a m’zigawo zonse kuchokera ku Indiya kukafika ku Itiyopiya, zigawo 127.+ Chigawo chilichonse anachilembera makalata amenewa malinga ndi mmene anthu a m’chigawocho anali kulembera+ ndiponso m’chinenero chawo.+ Nawonso Ayuda anawalembera malinga ndi mmene iwo anali kulembera ndiponso m’chinenero chawo.+ 10  Moredekai analemba makalatawo m’dzina la Mfumu+ Ahasiwero ndi kuwadinda+ ndi mphete yodindira ya mfumu.+ Atatero anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma okwera pamahatchi+ aliwiro amene anali kuwagwiritsa ntchito potumikira mfumu. 11  M’makalatawo mfumu inalola Ayuda amene anali m’mizinda yosiyanasiyana kuti asonkhane+ ndi kuteteza miyoyo yawo. Inawalolanso kuwononga, kupha ndi kufafaniza magulu onse ankhondo a anthu+ ndi zigawo zimene zinali kuwachitira nkhanza, ngakhalenso ana ndi akazi ndiponso kufunkha zinthu zawo.+ 12  Mfumu inawalola kuchita zimenezi m’zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi,+ tsiku la 13+ la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 13  Zimene analemba+ m’makalatawo anazipereka kuti zikhale lamulo m’zigawo zonse. Anazifalitsa kwa anthu a mitundu yonse kuti Ayuda akonzekere kudzabwezera+ adani awo pa tsiku limeneli. 14  Amtokomawo+ anathamanga ndi kupita mofulumira atakwera pamahatchi amene anali kuwagwiritsa ntchito potumikira mfumu. Anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndipo lamulo linachokera m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ 15  Ndiyeno Moredekai anachoka pamaso pa mfumu atavala chovala chachifumu+ cha buluu ndi nsalu yoyera. Analinso atavala chisoti chachikulu chachifumu chagolide, mkanjo wa nsalu yabwino kwambiri yaubweya wa nkhosa+ wonyika mu utoto wofiirira.+ Ndipo mumzinda wa Susani munamveka kufuula kwa chisangalalo ndi kukondwera.+ 16  Pakati pa Ayuda panali chisangalalo, kukondwa+ ndi kunyadira ndipo anthu anali kuwapatsa ulemu. 17  M’zigawo zonse ndi m’mizinda yonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake linafika, Ayuda anali kusangalala ndi kukondwera. Anachita phwando+ ndipo linali tsiku lachisangalalo. Anthu ambiri+ a m’dzikomo anayamba kudzitcha Ayuda+ chifukwa anali kuchita mantha kwambiri+ ndi Ayudawo.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.
Onani Zakumapeto 13.