Esitere 5:1-14

5  Ndiyeno pa tsiku lachitatu,+ Esitere anavala zovala zachifumu.+ Kenako anakaima m’bwalo lamkati+ la nyumba ya mfumu moyang’anana ndi nyumba ya mfumuyo. Pa nthawiyi mfumu inali itakhala pampando wake wachifumu m’nyumba yakeyo moyang’anana ndi khomo lolowera m’nyumbayo.  Mfumu itangoona Mfumukazi Esitere itaima m’bwalo la nyumba ya mfumu, inamukomera mtima+ moti inamuloza ndi ndodo yachifumu ya golide+ imene inali m’manja mwake. Pamenepo Esitere anayandikira ndi kugwira pamwamba pa ndodoyo.  Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Chavuta n’chiyani Mfumukazi Esitere, ndipo ukufuna kupempha chiyani?+ Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu,+ ipatsidwa kwa iwe.”  Pamenepo Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, lero inu ndi Hamani+ mubwere kuphwando+ limene ine ndakukonzerani.”  Ndiyeno mfumu inati: “Amuna inu, itanani Hamani mofulumira+ mogwirizana ndi mawu a Esitere.” Kenako mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Esitere anakonza.  Pa nthawi ina mkati mwa phwando la vinyo, mfumu inafunsa Esitere kuti: “Ukufuna kupempha chiyani?+ Chimene ukufunacho ndikupatsa. Ukufuna chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu, ipatsidwa kwa iwe.”  Poyankha Esitere anati: “Pempho langa ndi ili,  Ngati mungandikomere mtima mfumu+ ndipo ngati zingakukomereni kuchita zimene ndapempha n’kundipatsa zimene ndikufuna, inu mfumu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndidzakukonzerani mawa. Ndipo mawa ndidzanena pempho langa monga mmene inu mfumu mwanenera.”+  Pamapeto pake, Hamani anatuluka tsiku limenelo ali wokondwa+ komanso akusangalala kwambiri mumtima mwake. Koma atangoona Moredekai pachipata cha mfumu+ komanso kuti sanaimirire+ ndi kunthunthumira chifukwa cha iye,+ nthawi yomweyo Hamani anamukwiyira kwambiri+ Moredekai. 10  Koma Hamani anaugwira mtima ndipo analowa m’nyumba yake. Kenako anatumiza uthenga kuti anzake ndi mkazi wake Zeresi+ abwere. 11  Ndiyeno Hamani anayamba kudzitamandira pamaso pawo chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chake+ ndi kuchuluka kwa ana ake aamuna.+ Anadzitamandiranso chifukwa cha zonse zimene mfumu inamulemekeza nazo komanso chifukwa chakuti inamukweza kuposa akalonga ndi atumiki a mfumu.+ 12  Pamenepo Hamani anapitiriza kunena kuti: “Kuwonjezera apo, Mfumukazi Esitere sanaitane wina aliyense kuphwando limene anakonza, koma anaitana ine ndi mfumu,+ ndipo mawa+ wandiitananso pamodzi ndi mfumu. 13  Koma zonsezi sizikundikwanira ndikamaona Moredekai, Myuda, atakhala pachipata cha mfumu.” 14  Pamenepo mkazi wake Zeresi ndi anzake onsewo anamuuza kuti: “Mukonzetse mtengo+ wotalika mikono* 50. Ndiyeno m’mawa+ mukauze mfumu kuti apachike Moredekai pamtengowo.+ Mukatero mupite kuphwando ndi mfumu muli wosangalala.” Zimenezi zinaoneka zosangalatsa+ kwa Hamani, choncho anakonzetsa mtengowo.+

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.