Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAVIDIYO OTHANDIZA POPHUNZIRA

Mavidiyo Othandiza Kumvetsa Mfundo Zofunika za M’baibulo

Mavidiyowa ali ndi mayankho a mafunso ofunika kwambiri a m’Baibulo ndipo ndi ogwirizana ndi mitu ya m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.

 

Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu

Kodi uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu n’chiyani? Kodi tingaukhulupirire? Kabuku kano kali ndi mayankho a mafunso ambiri a m’Baibulo.

Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?

Mulungu ali ndi maina ambiri audindo monga akuti Atate, Mlengi ndi Ambuye. Koma Dzina lake lenileni limapezeka m’Baibulo malo oposa 7000.

Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?

Ngati Baibulo linalembedwa ndi anthu, kodi n’zomveka kunena kuti ndi Mawu a Mulungu? Kodi m’Baibulo muli mawu a ndani?

Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

Ngati Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndiye kuti liyenera kukhala losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse.

N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

Baibulo limasonyeza kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Kodi imfa ya Yesu ili ndi phindu lililonse?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

Padziko lapansili pali zinthu zambiri zokongola. Mulungu anaika dzikoli pamalo abwino kwambiri kuchokera pamene pali dzuwa ndipo limazungulira pa liwiro labwino. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansili mwanjira imeneyi?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Ali padziko lapansi, Yesu anafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kwa zaka zambiri otsatira ake akhala akupempherera Ufumu umenewu kuti ubwere.