Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAGWIRIZANA NDI ZOTI ANTHU AZIMENYA NKHONDO?

Kodi Mulungu Ankagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo M’nthawi ya Aisiraeli?

Kodi Mulungu Ankagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo M’nthawi ya Aisiraeli?

Pa nthawi ina, mfumu yamphamvu ya ku Iguputo inkalamulira Aisiraeli mwankhanza kwambiri. (Ekisodo 1:13, 14) Aisiraeliwa ankapempha Mulungu kuti awathandize, ndipo patadutsa zaka zambiri, Mulungu anawathandizadi. (Ekisodo 3:7-10) Baibulo limanena kuti Mulungu anawamenyera nkhondo. Anakhaulitsa Aiguputo powagwetsera miliri yoopsa komanso anapha mfumu ya Iguputo limodzi ndi asilikali ake m’Nyanja Yofiira. (Salimo 136:15) Apatu, Yehova anasonyeza kuti ndi Mulungu “wankhondo.”—Ekisodo 15:3, 4.

Zimene Mulungu anachitazi zikusonyeza kuti sadana ndi nkhondo zonse. Mwachitsanzo, pa nthawi ina analamula Aisiraeli kuti amenyane ndi Akanani omwe anali oipa kwambiri. (Deuteronomo 9:5; 20:17, 18) Komanso anauza Mfumu Davide kuti amenyane ndi Afilisiti omwe ankapondereza Aisiraeli. Anachitanso kuuza Davideyo njira yabwino yomenyera nkhondoyo, yomwe inathandiza kuti awagonjetse.—2 Samueli 5:17-25.

Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zina Mulungu ankavomereza kuti anthu ake amenye nkhondo akaona kuti akuponderezedwa komanso khalidwe la anthu a mtundu winawake likafika poipa kwambiri. Ankachita zimenezi pofuna kuteteza anthu akewo kuti asayambe kutengera makhalidwe oipa a anthuwo. Koma tsopano tiyeni tione zinthu zitatu zochititsa chidwi zokhudza nkhondo zimenezi.

  1. MULUNGU NDI YEMWE ANKASANKHA WOTI AMENYE NKHONDO. Nthawi ina Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo.” N’chifukwa chiyani anawauza zimenezi? Anawauza zimenezi chifukwa iyeyo ndi amene ankafuna kuwamenyera nkhondoyo. (2 Mbiri 20:17; 32:7, 8) Mulungu anachita zimenezi kambirimbiri kuphatikizapo nthawi imene Aisiraeli anali ku Iguputo ija. Koma nthawi zina ankachita kuuza Aisiraeliwo kuti amenye nkhondo pakakhala zifukwa zomveka. Mwachitsanzo, anawauza kuti amenye nkhondo n’cholinga choti alande Dziko Lolonjezedwa. Komanso atafika m’dzikolo, anawauzanso kuti azimenya nkhondo, mitundu ina ikafuna kulanda malo awo.—Deuteronomo 7:1, 2; Yoswa 10:40.

  2.   MULUNGU NDI AMENE ANKANENA NTHAWI YOYENERA KUMENYA NKHONDO. Aisiraeli ankafunika kudikira mpaka Mulungu atawauza nthawi yoyenera kumenya nkhondo. Akachita zosemphana ndi zimenezi, Mulungu sankawathandiza. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti Aisiraeli akamenya nkhondo imene Mulungu sanawauze, ankakumana ndi zokhoma. *

  3. Ngakhale kuti Mulungu anawononga Akanani, anapulumutsa Rahabi ndi anthu a m’banja lake

    MULUNGU SASANGALALA ANTHU AKAMAFA, NGAKHALE ATAKHALA OIPA. Yehova Mulungu ndi amene analenga anthu. (Salimo 36:9) Choncho sasangalala anthu akamafa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti padzikoli pali anthu ena oipa kwambiri amene amakonda kupondereza komanso kupha anzawo. (Salimo 37:12, 14) Pofuna kuthana ndi anthu ngati amenewa, nthawi zina Mulungu ankalamula Aisiraeli kuti amenye nkhondo. Koma pa nthawi yonse imene Aisiraeli ankamenya nkhondo ngati zimenezi, Yehova ankasonyeza kuti ‘sakwiya msanga’ komanso ankawachitira ‘chifundo’ anthu oipawo. (Salimo 86:15) Mwachitsanzo, anauza Aisiraeli kuti asanayambe kumenya nkhondo, ‘azilengeza mfundo za mtendere’ n’cholinga choti anthuwo asinthe makhalidwe awo oipa. Akasintha, Aisiraeli sankafunikanso kumenyana nawo. * (Deuteronomo 20:10-13) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ‘sasangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma amafuna kuti munthu woipa abwerere kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.’—Ezekieli 33:11, 14-16.

Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti m’nthawi ya Aisiraeli, Mulungu ankalola kuti anthu ake amenye nkhondo pofuna kuchotsa anthu oipa komanso kupulumutsa anthu ake akamaponderezedwa. Taonanso kuti Mulungu ndi yemwe ankasankha woti amenye nkhondo ndiponso nthawi yoyenera kumenya nkhondoyo. Koma kodi Mulungu ankalola kuti anthu azimenya nkhondo monga njira yongofuna kuphera anthu? Ayi, chifukwa Baibulo limanena kuti Mulungu amadana kwambiri ndi chiwawa. (Salimo 11:5) Koma popeza Yesu atabwera padziko lapansili ankalimbikitsa anthu kuti azikonda adani awo, kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu anasintha maganizo?

^ ndime 7 Mwachitsanzo nthawi ina Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Aamaleki komanso Akanani, chifukwa anakamenyana nawo Mulungu asanawalamule. (Numeri 14:41-45) Kenako patadutsa zaka zambiri, Yosiya yemwe anali Mfumu, anachitanso zomwezi. Zimene anachitazi zinachititsa kuti ataye moyo wake.—2 Mbiri 35:20-24.

^ ndime 8 Aisiraeli sanalengeze mfundo za mtendere asanakamenyane ndi Akanani chifukwa choti Akananiwo anali okanika. Anali atapatsidwa nthawi yokwanira yoti asinthe makhalidwe awo oipa. Koma ayi ndithu sanasinthe, moti pa nthawi imene Aisiraeli ankabwera kuti amenyane nawo, makhalidwe awo anali ataipiratu. (Genesis 15:13-16) Choncho Aisiraeli ankafunika kuseseratu Akanani onse kupatulapo anthu amene anasintha makhalidwe awo.—Yoswa 6:25; 9:3-27.