Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo?

Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo?

Kodi munthu atakufunsani funso limeneli, mungamuyankhe bwanji? Ambiri amaganiza kuti Mulungu amagwirizana ndi zoti anthu azimenya nkhondo. Amanena kuti m’Baibulo muli umboni wambirimbiri wosonyeza kuti Mulungu ankalamula anthu ake kuti azimenya nkhondo. Komabe ena amadabwa akaganizira zoti Yesu, yemwe ndi mwana wa Mulungu, analamula otsatira ake kuti azikonda adani awo. (Mateyu 5:43, 44) Chifukwa cha zimenezi amanena kuti poyamba Mulungu ankavomereza kuti anthu azimenya nkhondo, koma kenako anasintha maganizo.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi Mulungu amagwirizana ndi zoti anthu azimenya nkhondo? Ngati amatero, kodi amakhala mbali ya ndani pa nkhondo zomwe zimachitika masiku ano? Kudziwa mayankho a mafunsowa kungakuthandizeni kwambiri. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwadziwa zoti Mulungu amavomereza kuti anthu azimenya nkhondo ndiponso kuti ali ku mbali ya gulu limene inunso mukufuna kuti lipambane. Kodi mungaone kuti munasankha molakwika? Ayi, ndipo simungakayikire kuti gulu lanulo lipambana. Koma kodi mungamve bwanji ngati mutadziwa kuti Mulungu ali kumbali ya gulu linalo? Mwina pamenepo mungafunike kuganizanso kawiri.

Kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani ya nkhondo n’kofunika kwambiri chifukwa kungakuthandizeni kuti mumudziwe bwino. Ngati inuyo mukukumana ndi mavuto chifukwa cha nkhondo kapena ngati zimakupwetekani mukaona anthu akuvutika chifukwa cha nkhondo, mwina mungaganize kuti Mulungu ndi wankhanza. Kapena mungamaganize kuti sizimamukhudza n’komwe akamaona anthu akuponderezedwa.

Komatu mungadabwe kudziwa kuti zimene Baibulo limanena n’zosiyana kwambiri ndi zimene anthu amaganiza. Komanso si zoona kuti poyamba Mulungu ankagwirizana ndi zoti anthu azimenya nkhondo koma kenako anasintha maganizo. Tsopano tiyeni tione ngati Mulungu ankagwirizana ndi zoti anthu azimenya nkhondo m’nthawi ya Aisiraeli, m’nthawi ya atumwi, komanso ngati amagwirizana nazo masiku ano. Tionanso ngati nkhondo zidzathe kapena ayi.