Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zilango za Mulungu Kodi Zimasonyeza Kuti Ndi Wankhanza?

Zilango za Mulungu Kodi Zimasonyeza Kuti Ndi Wankhanza?

KUTI TIPEZE yankho la funso limeneli, tiyeni tikambirane mwachidule zitsanzo ziwiri za zilango zimene Mulungu anapereka zomwe zinalembedwa m’Baibulo. Tikambirana za Chigumula cha m’nthawi ya Nowa komanso kuwonongedwa kwa mtundu wa Akanani.

CHIGUMULA CHA M’NTHAWI YA NOWA

ZIMENE ANTHU AMANENA: “Mulungu ndi wankhanza chifukwa anabweretsa chigumula chomwe chinawononga anthu onse kupatulapo Nowa ndi banja lake.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Ine [Mulungu] sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.” (Ezekieli 33:11) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu sanasangalale ndi imfa ya anthu amene anawonongedwa pa chigumulacho. Ndiye n’chifukwa chiyani anawawononga?

Baibulo limanena kuti kale Mulungu anawononga anthu osamvera, “kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.” (2 Petulo 2:5, 6) Kodi zimene anachitazi zikutiphunzitsa chiyani?

Choyamba, ngakhale kuti Mulungu sasangalala ndi imfa ya anthu oipa, Iye amalanga anthu oipa omwe amachititsa kuti anthu ena azivutika. M’tsogolomu adzathetsa mavuto onse komanso zinthu zonse zopanda chilungamo.

Chachiwiri, zimene Mulungu anachita powononga anthu oipa zimasonyeza kuti Iye amachenjeza kaye anthu asanapereke chilango. Nowa anali mlaliki wachilungamo koma anthu ambiri ananyalanyaza uthenga wake. Baibulo limanena kuti: “Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.”—Mateyu 24:39.

Mulungu wakhala akuchita zimenezi akafuna kupereka chilango. Mwachitsanzo, anachenjeza Aisiraeli kuti ngati atayamba kuchita zoipa ngati mmene anthu a mitundu ina ankachitira, Iye adzalola kuti adani awo awalande dziko lawo, kuwononga likulu lawo ku Yerusalemu kenako n’kuwatengera ku ukapolo. Aisiraeli anayamba kuchita zoipa moti anafika pomapereka nsembe ana awo. Kodi Yehova anatani? Anatumiza aneneri mobwerezabwereza kuti akawachenjeze kuti asinthe. Baibulo limanenanso kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.”—Amosi 3:7.

KODI NKHANI IMENEYI NDIYOFUNIKA BWANJI KWA INU? Zimene Yehova ankachita akafuna kupereka  chilango zimatipatsa chiyembekezo. Timadziwa kuti Mulungu adzapereka chilango kwa anthu ankhanza omwe amachititsa kuti anzawo azivutika. Baibulo limati: “Pakuti ochita zoipa adzaphedwa. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” (Salimo 37:9-11) Pamenepa n’zoonekeratu kuti Mulungu si wankhanza chifukwa zilango zimene amapereka zimathandiza kuti anthu asamavutike.

KUWONONGEDWA KWA AKANANI

ZIMENE ANTHU AMANENA: “Zimene Mulungu anachita powononga Akanani zinali nkhanza zoopsa kuposa nkhanza zimene anthu amachitirana masiku ano popha anthu onse amtundu wosiyana ndi wawo.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ‘Njira zake zonse [za Mulungu] ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene amachita zinthu mwachilungamo.’ (Deuteronomo 32:4) Mulungu akafuna kulanga anthu, amalanga mwachilungamo ndipo sitingayerekezere ndi zimene anthu amachita akafuna kulanga anthu ena. N’chifukwa chani tikutero? Chifukwa chakuti Mulungu amatha kuona zimene zili mumtima mwa munthu pomwe anthufe sitingathe kuchita zimenezo.

Mwachitsanzo, pamene Mulungu ankafuna kuwononga mizinda ya Sodomu ndi Gomora, Abulahamu ankafunitsitsa kuti Mulungu asawononge anthu abwino. Iye sankaganizira n’komwe kuti Mulungu, yemwe ndi wachilungamo, ‘angawononge olungama pamodzi ndi oipa.’ Koma Mulungu anamutsimikizira kuti ngakhale mu Sodomu mutapezeka anthu 10 olungama, Iye sakanawononga mzindawo. (Genesis 18:20-33) Apa n’zoonekeratu kuti Mulungu anafufuza mitima ya anthuwo ndipo anaona kuti anali oyeneradi kuwonongedwa.—1 Mbiri 28:9.

Mulungu anachitanso zimenezi powononga Akanani. Iye anafufuza mitima yawo ndipo anaona kuti ndi oyenera kuwonongedwa. Akanani ankadziwika kuti anali anthu ankhanza chifukwa ankaotcha ana amoyo pamoto popereka nsembe. * (2 Mafumu 16:3) Akanani ankadziwa kuti Yehova analamula Aisiraeli kuti alande dziko lawo. Akanani amene anasankha kukhalabe m’dzikolo komanso kumenya nkhondo ndi Aisiraeli ankatsutsana ndi Yehova, yemwe anali atasonyeza kuti amatsogolera anthu ake.

Komabe, Yehova anachitira chifundo Akanani amene anasiya njira zawo zoipa n’kuyamba kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, Rahabi yemwe anali hule ndipo ankakhala ku Kanani, anapulumutsidwa limodzi ndi banja lake. Komanso anthu a ku Kanani omwe ankakhala mumzinda wa Gibeoni anapulumutsidwa pamodzi ndi ana awo atapempha kuti Yoswa awachitire chifundo.—Yoswa 6:25; 9:3, 24-26.

KODI NKHANIYI NDIYOFUNIKA BWANJI KWA INU? Tingaphunzirepo mfundo yofunika kwambiri pa zimene Mulungu anachitira Akanani. Panopa tayandikira kwambiri “tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:7) Ngati timakonda Yehova, tidzasangalala kwambiri akamadzawononga anthu onse amene amakana ulamuliro wake komanso amene amachititsa kuti anthu ena azivutika.

Akanani ankadziwika kuti anali anthu ankhanza kwambiri ndipo ankadana ndi Mulungu komanso Aisiraeli

Mwachikondi, Yehova amakumbutsa makolo kuti zimene amachita zimakhudza ana awo. Baibulo limati: “Choncho inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo. Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake ndi kum’mamatira.” (Deuteronomo 30:19, 20) Kodi Mulungu akanakhala wankhanza akananena mawu amenewa? Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu si wankhanza chifukwa amakonda anthu ndipo amafuna kuti azichita zinthu mwanzeru.

^ ndime 15 Akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza kuti anthu a ku Kanani akamalambira ankawotcha ana awo ngati nsembe.