Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SATANA ALIPODI?

Kodi Satana Ndi Maganizo Oipa Chabe?

Kodi Satana Ndi Maganizo Oipa Chabe?

Anthu ambiri amaganiza kuti Satana amene amatchulidwa m’Baibulo ndi maganizo oipa chabe amene munthu amakhala nawo mumtima mwake. Koma kodi zimenezi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Ngati zimene anthu amaganizazi zili zoona, n’chifukwa chiyani Baibulo limasonyeza kuti Satana analankhulapo ndi Yesu Khristu komanso ndi Mulungu? Tiyeni tione zimene zinachitika.

SATANA ANALANKHULA NDI YESU

Yesu atangoyamba kumene utumiki wake, Satana anamuyesa maulendo atatu. Koyamba, anamuuza kuti agwiritse ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa pofuna kuthetsa njala yake. Kachiwiri, anamuuza kuti aike moyo wake pachiswe n’cholinga choti adzionetsere kuti ndi Mwana wa Mulungu. Ndipo kachitatu, anamuuza kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi ngati atamugwadira kamodzi kokha. Koma Yesu anagwiritsa ntchito Malemba pokana mayesero onsewa.—Mateyu 4:1-11; Luka 4:1-13.

Kodi pamenepa tingati Yesu ankalankhula ndi ndani? Kodi ankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwake? Ayi, chifukwatu Malemba amanena kuti Yesu “anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.” (Aheberi 4:15) Baibulo limanenanso kuti: “Iye sanachite tchimo, ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.” (1 Petulo 2:22) Yesu anakhalabe wokhulupirika ndipo sanachimwe komanso analibe maganizo oipa mumtima mwake. Choncho n’zoonekeratu kuti Yesu sankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwake. Koma ankalankhula ndi mngelo woipa yemwe ndi Satana.

Zimene Satana anauza Yesu zimasonyezanso kuti Satanayo alipodi.

  • Kumbukirani kuti Satana anauza Yesu kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi akamugwadira. (Mateyu 4:8, 9) Zomwe Satana ananenazi sizikanakhala zomveka, zikanakhala kuti Satanayo kulibeko. Komanso Yesu sanatsutse zoti maufumuwa ndi a Satana.

  • Yesu atakana mayeserowa, Satana “anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Zimenezi zikusonyeza kuti Satana si maganizo oipa chabe koma ndi mngelo woipa amene amachititsa anthu kuchita zoipa.

  • Komanso Satana atamusiya Yesu, “kunabwera angelo ndi kuyamba kum’tumikira.” (Mateyu 4:11) Kodi angelowa analidi enieni? Inde. Popeza angelowa ndi enieni, ndiye kuti Satana ndi weniweninso osati maganizo oipa chabe.

SATANA ANALANKHULA NDI MULUNGU

Pa nthawi inanso, Satana analankhula ndi Mulungu  kawiri ndipo anakambirana zokhudza Yobu, yemwe anali wokhulupirika. Pa maulendo onsewa, Mulungu ananena kuti Yobu ndi wokhulupirika. Koma Satana anati Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Ananenanso kuti Mulungu ankamudalitsa Yobu n’cholinga choti azimumvera. Pamenepatu Mdyerekezi analankhula ngati kuti iyeyo ankamudziwa bwino Yobu kuposa Mulungu. Pofuna kusonyeza kuti Yobu sankamutumikira chifukwa cha dyera, Yehova * analola Satana kuti awononge katundu yense wa Yobu, ana ake onse ngakhalenso thanzi lake. Patapita nthawi, zinadziwika kuti Yobu sankatumikira Yehova chifukwa cha dyera ndiponso kuti Satana ndi wabodza. Pamapeto pake Mulungu anadalitsa Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake.—Yobu 1:6-12; 2:1-7.

Kodi pamenepa tingati Yehova ankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwake? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.” (2 Samueli 22:31) Limanenanso kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova Mulungu.” (Chivumbulutso 4:8) Mawu akuti woyera akutanthauza kuti Yehova ndi wosadetsedwa, wopatulika komanso alibe uchimo uliwonse. Choncho iye sangakhale ndi maganizo oipa mumtima mwake.

Satana atanena kuti Yobu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera, Mulungu anamulola kubweretsa mavuto kwa Yobu

Komabe mwina ena anganene kuti Yobu sanali munthu weniweni, choncho zoti Satana analankhula ndi Mulungu ndi zongopeka. Koma kodi zimenezi n’zomveka? Baibulo limasonyeza kuti Yobu anali munthu weniweni. Mwachitsanzo, lemba la Yakobo 5:7-11 limanena kuti Yobu ndi chitsanzo chabwino kwa Akhristu pa nkhani ya kupirira mayesero. Nkhani ya Yobu imatithandizanso kudziwa kuti Yehova amadalitsa anthu amene amapirira mayesero. Kodi Yobu akanakhala bwanji chitsanzo cholimbikitsa zikanakhala kuti sanali munthu weniweni? Komanso zikanatheka bwanji kuti Satana awononge zinthu zonse za Yobu, zikanakhala kuti Yobuyo sanali munthu weniweni? Kuwonjezera pamenepa, palemba la Ezekieli 14:14, 20, Yobu akutchulidwa pamodzi ndi Nowa komanso Danieli, omwe anali anthu okhulupirika. Nowa ndi Danieli anali anthu enieni. Choncho nayenso Yobu anali munthu weniweni, yemwe ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Ngati Yobu anali munthu weniweni, kodi si pomveka kunena kuti Satana, yemwe ankamuyesa komanso kumuzunza, analinso weniweni?

Apatu taona kuti Baibulo limasonyeza kuti Satana alipodi. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Satana ndi woopsa?’

ZIMENE SATANA AKUCHITA MASIKU ANO

Yerekezerani kuti gulu la zigawenga lalowa m’dera lanu. Kodi mukuganiza kuti zotsatira zake zingakhale zotani? N’zoonekeratu kuti chitetezo cha m’deralo chikhoza kusokonekera ndipo anthu ena akhoza kuyamba kuchita makhalidwe oipa. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limanena kuti angelo oipa, omwe amatchedwa ziwanda, anaponyedwa padziko lapansi limodzi ndi Satana. Pa nkhaniyi Baibulo limati: “Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. . . . Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:9, 12) Zimenezi ndi zimene zimachititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri komanso kuti anthu azichita zinthu zoipa. Taganizirani zinthu zotsatirazi, zomwe timamva pa wailesi, kuwerenga m’nyuzipepala komanso kuonera pa TV.

  • Anthu akuchita makhalidwe oipa kwambiri komanso zinthu zachiwawa, ngakhale kuti mayiko ambiri akuyesetsa kuletsa zinthu zimenezi.

  • Zosangalatsa zolimbikitsa kukhulupirira mizimu zikuchuluka ngakhale kuti makolo ambiri sagwirizana nazo.

  • Ngakhale kuti mayiko ndi mabugwe akuyesetsa kuteteza zinthu zachilengedwe, anthu akupitirizabe kuwononga zinthuzi.

Anthu ambiri akaganizira zimene zikuchitikazi amavomereza kuti Satana ndi amene akupangitsa zinthu zoipa zimene zikuchitika padzikoli.

Popeza taona kuti Satana ndi woopsa, mwina mungadzifunse kuti: Kodi ndingatani kuti Satana asamandisocheretse? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri ndipo nkhani yotsatira ifotokoza yankho lake.

^ ndime 12 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.