NSANJA YA OLONDA November 2014 | Kodi Satana Alipodi?

Ngati Satana kulibe, ndiye kuti anthu amene amamuopa, amangoopa chinthu chomwe kulibe. Koma ngati alipodi, ndiye kuti anthu amene amaganiza kuti kulibe akhoza kunyengedwa mosavuta.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Satana Alipodi?

Kodi Satana ndi maganizo oipa amene munthu amakhala nawo mumtima mwake kapena ndi mngelo woipa yemwe amasocheretsa anthu?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Satana Ndi Maganizo Oipa Chabe?

Pali nkhani za m’Baibulo ziwiri zimene zingatithandize kupeza yankho la funso limeneli.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Satana Tizimuopa?

Mulungu watipatsa zinthu 4 zimene zingatithandize kuti Satana asatisocheretse.

KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 2)

Ulosi wa m’Baibulo komanso maloto omwe Mulungu analotetsa mfumu ya ku Babulo zimatithandiza kudziwa chaka chimene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

“Ndingachitirenji Choipa Chachikulu Chonchi N’kuchimwira Mulungu?”

Kodi Yosefe anatha bwanji kukana zofuna za mkazi wa Potifara zoti agone naye?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani zokhudza anthu amene Yesu anawaukitsa, nanga zimenezi zimatithandiza bwanji kukhulupirira malonjezo amene tikuyembekezera?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mulungu Analenga Mdyerekezi Kuti Azitiyesa?

Kodi Satana anachokera kuti? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Yesu ananena kuti Mdyerekezi “sanakhazikike m’choonadi.”