Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 2)

Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 2)

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza zimene a Mboni za Yehova amachita akamakambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti munthu wina wa Mboni, dzina lake Cameron, wafikanso pakhomo pa Bambo Jon, omwe anakambiranapo nawo zokhudza Ufumu wa Mulungu.

KUBWEREZA MWACHIDULE ZOKHUDZA MALOTO A NEBUKADINEZARA

Cameron: Ndasangalala kuti takumananso a Jon. Ndimasangalala kwambiri kuphunzira nanu Baibulo. * Kaya muli bwanji?

Jon: Ndili bwino, kaya inu.

Cameron: Inenso ndili bwino. Ulendo wapita uja tinakambirana chifukwa chake a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914. * Tinaona kuti umboni wa zimenezi ndi ulosi umene umapezeka m’buku la Danieli chaputala 4. Kodi mukukumbukira zomwe tinakambirana?

Jon: Ee. Tinakambirana za maloto amene Mfumu Nebukadinezara inalota okhudza mtengo waukulu.

Cameron: Zoona. Mfumu Nebukadinezara inalota mtengo wautali kufika kumwamba. Kenako inamva mngelo wa Mulungu akulamula kuti mtengowo udulidwe, koma chitsa chake achisiye. Anati pakatha “nthawi zokwanira 7” mtengowo udzaphukanso. * Tinakambirananso chifukwa chake tingati ulosiwu unakwaniritsidwa m’njira ziwiri. Kodi mukukumbukira njira yoyamba?

Jon: Ee. Unakwaniritsidwa pa Nebukadinezara yemweyo, pa nthawi yomwe anachita misala, si choncho?

Cameron: Ndi chonchodi. Nebukadinezara anachita misala kwa zaka 7, ndipo pa nthawiyi sankalamuliranso monga mfumu. Pa kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosiwu, ulamuliro wa Mulungu unasokonekera kwa nthawi zokwanira 7. Ndiye paja tinaona kuti nthawi 7 zimenezi zinayamba mu 607 B.C.E. pamene mzinda wa Yerusalemu unawonongedwa. Kuyambira m’chakachi, padziko lapansi panalibe mfumu yomwe inkalamulira anthu a Mulungu poimira Mulunguyo. Komabe pamapeto a nthawi zokwanira 7 zimenezi, Mulungu ankayenera kusankha Mfumu yatsopano kuchokera kumwamba yoti izilamulira anthu ake. Choncho m’mawu ena tingati nthawi zokwanira 7 zitatha, Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira. Paja taona kale kuti nthawi zokwanira 7 zimenezi zinayamba mu 607 B.C.E. Ndiyetu tikadziwa chaka chimene nthawi zokwanira 7 zimenezi zinatha, tingadziwenso chaka chimene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira. Tili limodzi?

Jon: Inde. Ndipotu zimenezi zandithandiza kukumbukira zomwe tinakambirana.

Cameron: Chabwino. Tsopano tiyeni tione kutalika kwa nthawi zokwanira 7 zimenezi. Ndinawerenganso nkhaniyi kuti ndikumbukire mfundo zofunika. Ndiyesetsa kuzifotokoza momveka bwino.

Jon: Oho.

 NTHAWI ZOKWANIRA 7 ZITATHA MASIKU OTSIRIZA ANAYAMBA

Cameron: Pakukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwu, komwe kunakhudza Nebukadinezara, nthawi zokwanira 7 zinali zaka 7 zenizeni. Koma pakukwaniritsidwa kwakukulu, komwe kukukhudza Ufumu wa Mulungu, nyengo ya nthawi zokwanira 7 iyenera kukhala yaitali osati zaka 7 zenizeni.

Jon: N’chifukwa chiyani mukutero?

Cameron: Choyamba, kumbukirani kuti nthawi zokwanira 7 zinayamba pamene mzinda wa Yerusalemu unawonongedwa mu 607 B.C.E. Pa nthawiyi powerengera zaka ankachotsera osati kuphatikiza. Choncho tikawerenga zaka 7 kuchokera mu 607 B.C.E., zimatifikitsa mu 600 B.C.E. Koma palibe chinthu chapadera chokhudza Ufumu wa Mulungu chomwe chinachitika m’chaka chimenechi. Komanso monga tinaonera nthawi yapita ija, pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi anasonyeza kuti nthawi zokwanira 7 zinali zisanathe.

Jon: Ndakumbukiradi kuti tinakambirana zimenezi.

Cameron: Choncho nthawi zokwanira 7 zimenezi si zaka zenizeni, koma zikuimira nthawi yaitali.

Jon: Ndiye nthawi yake ndi yaitali bwanji?

Cameron: Buku la Chivumbulutso, lomwe lili ndi maulosi ogwirizana ndi omwe ali m’buku la Danieli, lingatithandize kudziwa kutalika kwa nthawi zokwanira 7 zimenezi. Limati nthawi zitatu ndi hafu n’chimodzimodzi ndi masiku 1,260. * Choncho popeza nthawi zitatu ndi hafu, zomwe ndi hafu ya nthawi 7 zikupanga masiku 1,260, ndiye kuti nthawi 7 n’chimodzimodzi ndi masiku 1,260 kuphatikiza masiku 1,260 omwe ndi masiku 2,520. Tili limodzi pamenepa?

Jon: Ee, tili limodzi. Koma zimenezi zikugwirizana bwanji ndi mfundo yoti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914?

Cameron: Okhe. Tiyeni tione kugwirizana kwake. M’maulosi ena a m’Baibulo, tsiku limodzi limaimira chaka. * Tikawerengetsera motsatira mfundo imeneyi, ndiye kuti nthawi zokwanira 7 zimenezi ndi zaka 2,520. Choncho tikawerenga zaka 2,520 kuchokera mu 607 B.C.E., zakazi zimatifikitsa m’chaka cha 1914. * N’chifukwa chaketu timanena kuti nthawi zokwanira 7 zija zinatha mu 1914, ndipo chaka chimenechi ndi chimene Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipotu n’zochititsa chidwi kuti kuyambira mu 1914, padzikoli pakhala pakuchitika zinthu zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika m’masiku otsiriza.

Jon: Zinthu ngati chiyani?

Cameron: Taonani zimene Yesu ananena zomwe zalembedwa pa Mateyu 24:7. Palembali Yesu ananena zimene zidzachitike padzikoli, iye akadzayamba kulamulira kumwamba. Ananena kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” Onani kuti Yesu ananena kuti pa nthawiyi kudzakhala njala komanso zivomezi. Kuyambira mu 1914, padzikoli pakhala pakuchitika zinthu zoipa ngati zimenezi. Si choncho?

Jon: Zoonadi.

Cameron: Palembali Yesu ananenanso kuti akadzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba, padzikoli pazidzachitika nkhondo. Ndipotu buku la Chivumbulutso linaneneratu kuti m’masiku otsiriza nkhondo zizidzachitika padziko lonse osati m’mayiko ochepa okha. * Kodi mukukumbukira chaka chimene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba?

Jon: Inde. Inayamba mu 1914, chaka chomwe  mukuti Yesu anayamba kulamulira. Ndinali ndisanaganizirepo zimenezi.

Cameron: Tikagwirizanitsa ulosi wonena za nthawi zokwanira 7 ndi maulosi ena okhudza masiku otsiriza, tingaone kuti Ufumu wa Mulungu unayambadi kulamulira mu 1914. A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Yesu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anayamba kulamulira mu 1914 komanso kuti masiku otsiriza anayamba chaka chomwechi. *

Jon: Ndiganiziranso mfundo zimenezi kuti ndizimvetse bwino.

Cameron: Zimenezo ndi zomveka. Musaiwale kuti paja nanenso zinanditengera nthawi kuti ndimvetse nkhaniyi. Komabe ndikukhulupirira kuti pa zimene takambirana pa nkhaniyi, mwaona kuti ngakhale m’Baibulo mulibe chaka cha 1914, zimene a Mboni amakhulupirira pa nkhaniyi n’zochokera m’Malemba.

Jon: N’zoona. A Mboni mumandichititsa chidwi kwambiri. Mfundo iliyonse imene munganene mumawerenga lemba losonyeza kuti mfundoyo ndi yochokeradi m’Baibulo. Komabe ndikudabwa kuti n’chifukwa chiyani nkhaniyi ili yovuta kumvetsa chonchi? N’chifukwa chiyani Mulungu sanangolemba m’Baibulo kuti Yesu adzayamba kulamulira kumwamba mu 1914?

Cameron: Mwafunsa funso labwino kwambiri. Pali zinthu zambiri zimene Baibulo silinena mwatchutchutchu. Koma kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Mulungu analemba Baibulo mwanjira yakuti anthu azichita khama kuti alimvetse? Bwanji tidzakambirane nkhani imeneyi ndikadzabweranso?

Jon: Zingakhaledi bwino kuti tidzakambirane.

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibulo imene simuimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzasangalala kukambirana nanu.

^ ndime 5 Pali njira imene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu. Iwo amapita kunyumba za anthu n’kumaphunzira nawo nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo kwaulere.

^ ndime 7 Onani nkhani yakuti, “Kucheza ndi Munthu Wina—Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira?—Gawo 1” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2014.

^ ndime 22 Onani Chivumbulutso 12:6, 14. Pa vesi 14 atchula nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi, zomwe tikaziphatikiza zikupanga nthawi zitatu ndi hafu.

^ ndime 24 Onani tchati chakuti, “Kugwirizana kwa Maloto a Nebukadinezara ndi Ufumu wa Mulungu.”