Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SATANA ALIPODI?

Kodi Satana Tizimuopa?

Kodi Satana Tizimuopa?

Mpweya umene umatuluka m’makala komanso m’malasha suoneka koma ndi woopsa. Satana ali ngati mpweya umenewu

Makala komanso malasha amatulutsa mpweya winawake wa poizoni. Mpweyawu suoneka ndiponso sukhala ndi fungo. Komatu anthu ambiri amafa chifukwa chopuma mpweyawu. Komabe sikuti palibe chimene munthu angachite kuti azindikire mpweyawu n’kudziteteza. Mwachitsanzo, ambiri amaika maalamu m’nyumba zawo n’cholinga choti mukakhala mpweyawu, maalamuwo azilira. Zimenezi zimathandiza kuti anthuwo adziteteze.

Satana tingamuyerekezere ndi mpweya umenewu. Iye saoneka komanso ndi wovuta kumuzindikira. Komatu ndi woopsa kwambiri. Komabe Mulungu angatithandize kuti tithe kulimbana naye. Pali zinthu zotsatirazi zomwe Mulungu watipatsa zimene zingatithandize kuti Satana asatisocheretse.

Yehova watipatsa zinthu zambiri zimene zingatithandize kuti Satana asatisocheretse

Anatilenga moti tizitha kusankha zochita. Lemba la Yakobo 4:7 limati: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.” Ngakhale kuti Satana ali ndi mphamvu, sangatikakamize kuchita zomwe ifeyo sitikufuna. Timasankha tokha kuchita zoipa kapena ayi. Lemba la 1 Petulo 5:9 limati: “Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye [Mdyerekezi].” Komanso kumbukirani kuti Yesu atakana zofuna za Satana katatu konse, Satanayo anamusiya. (Mateyu 4:11) Choncho ifenso tingathe kukana zofuna za Satana.

Tingathe kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Lemba la Yakobo 4:8 limatiuza kuti: “Yandikirani Mulungu.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti mukhale naye pa ubwenzi. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Choyamba, muyenera kuphunzira za iye kudzera m’Baibulo. (Yohane 17:3) Zimene mungaphunzire zokhudza Yehova, zingakuthandizeni kuti muyambe kumukonda. Chikondi chimenechi chingapangitse kuti muzichita zimene amafuna. (1 Yohane 5:3) Kodi Yehova amachita chiyani akaona kuti mukuyesetsa kuti mukhale naye pa ubwenzi? Lemba la Yakobo 4:8 lija limanena kuti: “Iyenso adzakuyandikirani.”

Anatilonjeza kuti adzatiteteza. Lemba la Miyambo 18:10 limati: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.” Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu ayenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, loti Yehova, ngati chithumwa. Koma zikutanthauza kuti anthu amene amakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo amaona kuti dzina lake ndi lofunika, angathe kupemphera kwa iye nthawi iliyonse kuti awathandize.

Watipatsa zitsanzo. Lemba la Machitidwe 19:19 limanena zimene anthu a ku Efeso anachita atangokhala Akhristu. Limati: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana  50,000.” * Akhristu amenewa anawotcha chilichonse chogwirizana ndi zamizimu, ngakhale kuti zinthuzo zinali za ndalama zambiri. Chitsanzo chawochi chingatithandize kwambiri masiku ano. M’dzikoli anthu ambiri amakhulupirira zamizimu komanso nkhani zokhudza ufiti. Kukhala ndi chilichonse chokhudza zamizimu komanso kuchita zamizimu kungapangitse kuti munthu azivutitsidwa ndi ziwanda. Choncho ndi bwino kupewa chilichonse chokhudzana ndi mizimu.—Deuteronomo 18:10-12.

Rogelio, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, poyamba sankakhulupirira kuti kuli Satana. Koma ali ndi zaka 50 anayamba kukhulupirira kuti Satana alipo. Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti ayambe kukhulupirira zimenezi? Iye anati: “Ndinapeza Baibulo ndipo nditawerenga ndinazindikira kuti Satana alipo. Zimenezi zandithandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti Satana asamandisocheretse.”

“Zimene ndinawerenga m’Baibulo zinandithandiza kuzindikira kuti Satana alipo, ndipo zimenezi zandithandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti Satana asamandisocheretse”

Komatu sikuti Satana azingosocheretsa anthu mpaka kalekale. Baibulo linaneneratu kuti iye “adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule.” (Chivumbulutso 20:10) Popeza Satana ali ndi thupi lauzimu, ataponyedwa pamoto komanso sulufule sangapse. Choncho lembali likungotanthauza kuti iye adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso. Apatu anthu onse amene amakonda Mulungu adzasangalala kwabasi.

Kodi mungakonde kudzakhalapo pa nthawi imene Satana adzakhale atawonongedwa? Dziwani kuti zimenezi n’zotheka. Panopa mungachite bwino kupitiriza kuphunzira za Yehova kuti mumudziwe bwino. * Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi moyo pa nthawi imene Satana sadzakhalapo. Pa nthawiyi zidzakhala zoona tikamadzanena kuti “kulibe Satana.”

^ ndime 8 Ngati ndalama zasiliva zomwe zatchulidwa palembali zinali madinari achiroma, ndiye kuti zinali ndalama zochuluka kwambiri chifukwa zinali zofanana ndi ndalama zimene anthu 50,000 ankalandira akagwira ntchito tsiku lonse.

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Satana komanso kukhulupirira mizimu, werengani mutu 10 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mungapemphe wa Mboni aliyense kuti akupatseni bukuli.