Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SATANA ALIPODI?

Kodi Satana Alipodi?

Kodi Satana Alipodi?

Chipilala chomwe chili ku Madrid, m’dziko la Spain, chosonyeza Satana ngati mngelo woipa amene anagwetsedwa padziko lapansi

“Ndili mwana, ine ndi makolo anga tinkakhala ku El Salvador. Ndikachita mwano, mayi ankakonda kundiuza kuti, ‘Satana abwera kudzakutenga.’ Koma ine ndinkawayankha kuti, ‘Abwere! Ine sindiopa Satana chifukwa ndimakhulupirira Mulungu.’”—ROGELIO.

Kodi nanunso muli ndi maganizo ofanana ndi a Rogelio? Pa mfundo zomwe zili m’munsizi, ndi iti imene mukuona kuti ndi yolondola?

  • Satana ndi maganizo oipa amene munthu amakhala nawo mumtima mwake.

  • Satana alipodi, koma sachita chidwi kwenikweni ndi zochita za anthufe.

  • Satana ndi mngelo woipa yemwe amachititsa kuti anthu azichita zoipa.

Ena amaona kuti mfundo yolondola ndi yoyambayo, ena amati yachiwiriyo ndipo ena amati yolondola ndi yomalizayo. Koma kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi n’kofunika? Ngati Satana kulibe, ndiye kuti amene amakhulupirira kuti alipo amakhulupirira zabodza. Ngati Satana alipodi koma sachita chidwi kwenikweni ndi zochita za anthufe, ndiye kuti anthu amene amamuopa, amangoopa njokaluzi. Komanso ngati Satana ndi mngelo woipa, yemwe amachititsa kuti anthu azichita zoipa, ndiye kuti ndi woopsa kwambiri kuposa mmene ambiri amaganizira.

Tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu amanena pa mafunso otsatirawa: Kodi Satana ndi ndani? Kodi ndi maganizo oipa amene amakhala mumtima mwa munthu kapena ndi mngelo woipa? Ngati alipodi, kodi ndi woopsa? Nanga mungatani kuti mudziteteze?