Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Ndalama?

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Ndalama?

Estelle * ankakonda kupita kutchalitchi ndi ana ake okwana 7. Iye ananena kuti: “Ndinauza abusa kuti ndikufuna kuphunzira Baibulo.” Koma abusawo sanamuthandize. Kenako Estelle anasiya kupita kutchalitchi. Iye anapitiriza kunena kuti: “Akuluakulu a kutchalitchiko anandilembera kalata yondiuza kuti ngati sindikufuna kupita kutchalitchiko ndizingotumiza ndalama basi. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amenewa akufuna kundithandiza kapena akungofuna ndalama zanga?’”

Angelina, yemwe ankakonda kwambiri kupita kutchalitchi, ananena kuti: “Kutchalitchi kwathu ankayendetsa basiketi ya zopereka katatu pa nthawi yonse ya mapempheroyo. Ndipo ankafuna kuti aliyense aziponyamo nthawi iliyonse basiketiyo ikamayendetsedwa. Nthawi zonse ankangofuna tizipereka ndalama. Mumtima ndinadziuza kuti, ‘Anthu amenewa alibe mzimu wa Mulungu ndithu.’”

Kodi zipembedzo za m’dera lanu zimakakamiza anthu mochita kuonetsera kapena mwakabisira kuti azipereka ndalama? Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa?

KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI PA NKHANI YA NDALAMA?

Yesu, yemwe anayambitsa Chikhristu, ananena kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Zimenezi zikutanthauza kuti uthenga wa m’Baibulo si wogulitsa ndipo aliyense ayenera kuupeza kwaulere.

Kodi Akhristu akale ankapeza bwanji ndalama zoyendetsera mpingo?

Aliyense ankapereka “mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” (2 Akorinto 9:7) Mtumwi Paulo anati: “Mwa kugwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza, tinalalikira uthenga wabwino.” (1 Atesalonika 2:9) Paulo ankasoka mahema kuti azipeza ndalama zomuthandiza pa utumiki wake.—Machitidwe 18:2, 3.

KODI A MBONI ZA YEHOVA AMATANI PA NKHANI IMENEYI?

A Mboni za Yehova amachitira misonkhano yawo m’nyumba za Ufumu. Kodi ndalama zomangira nyumba zimenezi amazitenga kuti? Samayendetsa mbale ya zopereka kapena kuyenda ulendo wa ndawala n’cholinga chofuna kupeza ndalama. M’malo mwake, aliyense amene amayamikira mapulogalamu auzimu amene amachitika kumeneko, amaponya ndalama m’kabokosi kamene kamakhala m’nyumba za Ufumu. Amachita zimenezi mosadzionetsera.

Kodi chipembedzo chiyenera kupeza bwanji ndalama zoyendetsera mpingo?

Pamafunika ndalama zambiri kuti magazini mukuwerengayi isindikizidwe komanso kuti itumizidwe malo osiyanasiyana. Koma simudzaona tikuitsatsa kapena kuchonderera anthu kuti atipatse ndalama. Cholinga chathu chachikulu ndi kuphunzitsa anthu zoona zimene Baibulo limaphunzitsa.

Kodi mukuganiza kuti njira imeneyi yopezera ndalama ikugwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa komanso zimene Akhristu oyambirira ankachita?

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa m’nkhaniyi ndi m’nkhani zotsatirazi.