Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli”

“Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli”
  • CHAKA CHOBADWA: 1966

  • DZIKO: FINLAND

  • POYAMBA: NDINKAMENYERA UFULU WA ANTHU NDI ZINYAMA

KALE LANGA:

Kuyambira ndili mwana ndinkakonda kwambiri zinthu zachilengedwe. Banja lathu linkakonda kupita kukaona zachilengedwe ku nkhalango komanso kunyanja zomwe zinali m’tauni yathu ya Jyväskylä, m’chigawo chapakati cha dziko la Finland. Ineyo ndimakonda kwambiri zinyama moti ndili mwana ndinkati ndikaona mphaka kapena galu ndinkangofuna kumukumbatira. Koma nditakula ndinakhumudwa kwambiri kuona mmene anthu amazunzira zinyama. Kenako ndinalowa m’gulu lina loona za ufulu wa zinyama.

Tinkachita zinthu zosiyanasiyana pomenyera ufulu wa zinyama. Mwachitsanzo tinkagawira mapepala komanso kuchita zionetsero zosonyeza kukwiya ndi anthu amene ankapha zinyama n’kumagulitsa ubweya wake komanso anthu amene ankagwira zinyama kuti aziyesera mankhwala osiyanasiyana. Tinakhazikitsanso bungwe loteteza zinyama. Chifukwa choti nthawi zina tinkachita zachiwawa pochita zionetsero ndipo apolisi ankatigwira. Ndinamangidwapo komanso kutengeredwa kukhoti maulendo angapo.

Kuwonjezera pa kumenyera ufulu wa zinyama, ndinkakhumudwanso kwambiri ndi mavuto amene ankachitika padzikoli. Choncho ndinalowanso m’mabungwe osiyanasiyana omenyera ufulu wa anthu monga la Amnesty International ndi la Greenpeace. Ndinkagwira ntchitoyi modzipereka kwambiri ndipo ndinkamenyera ufulu wa anthu osauka, osowa chakudya komanso anthu ena ovutika.

Koma pamapeto pake ndinazindikira kuti sindingakwanitse kusintha zinthu padzikoli. Ngakhale kuti mabungwe amenewa anakwanitsa kuthetsako mavuto ena, ndinkaona kuti mavuto akuluakulu ankawonjezerekabe. Zinkangooneka ngati chimzimu choipa chameza dziko lonse moti palibe amene angasinthe zinthu. Zimenezi zinandifooketsa kwambiri.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Chifukwa chokhumudwa kuti sindingathe kusintha zinthu, ndinayamba kuganizira za Mulungu komanso Baibulo. Ndinali nditaphunzirapo Baibulo ndi Mboni  za Yehova m’mbuyomu. Ngakhale kuti ndinkaona kuti a Mboni za Yehova ndi anthu achifundo komanso kuti ankachita zinthu mondiganizira, sindinkafuna kusintha khalidwe langa. Koma pa nthawiyi zinthu zinali zitasintha.

Ndinatenga Baibulo langa n’kuyamba kuwerenga. Zimene ndinawerengazo zinandikhazika mtima pansi. Ndinapeza malemba ena omwe amalimbikitsa kuti tizisamalira zinyama. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 12:10 limati: “Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake.” Ndinazindikiranso kuti Mulungu si amene amachititsa mavuto amene ali padzikoli. M’malomwake, mavuto akuchulukirachulukira chifukwa choti anthu ambiri satsatira malangizo a Mulungu. Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi komanso woleza mtima.—Salimo 103:8-14.

Pa nthawi imeneyi ndinapeza kapepala koitanitsira buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndipo ndinakatumiza. Pasanapite nthawi banja lina la Mboni za Yehova linafika panyumba yanga n’kundipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo ndipo ndinavomera. Ndinayambanso kusonkhana nawo ku Nyumba ya Ufumu. Zimenezi zinandithandiza kwambiri kuti ndizikonda zimene ndinkaphunzira.

Zimene ndinkaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kuti ndisinthe kwambiri. Ndinasiya kuledzera ndi kusuta komanso ndinayamba kudzisamalira. Ndinasiyanso kutukwana. Ndinasinthanso mmene ndinkaonera malamulo a boma. (Aroma 13:1) Komanso ndinasiya khalidwe lachiwerewere lomwe ndinalowerera nalo kwambiri.

Koma chimene chinandivuta kwambiri kusintha ndi kusiya kukonda kwambiri mabungwe omenyera ufulu wa anthu ndi zinyama. Zinanditengera nthawi yaitali kuti ndisiyane ndi mabungwe amenewa. Poyamba ndinkaona ngati kusiya mabungwewa kungasonyeze kuti ndine munthu wosakhulupirika. Komabe ndinazindikira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathe kusintha zinthu padzikoli. Choncho ndinayamba kugwira ntchito yolalikira za Ufumu umenewu.—Mateyu 6:33.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Pa nthawi imene ndinkamenyera ufulu wa anthu ndinkaona kuti anthu ali m’magulu awiri, gulu la anthu oipa ndi la anthu abwino ndipo ndinkadana ndi amene ndinkawaona kuti ndi oipa. Koma chifukwa chophunzira Baibulo, sindidana ndi munthu aliyense. Ndimayesetsa kutsanzira Khristu pokonda aliyense. (Mateyu 5:44) Njira imodzi imene ndimachitira zimenezi ndi kuwalalikira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndimasangalala kuona kuti ntchito imeneyi imalimbikitsa mtendere, kuthandiza anthu kuti azisangalala komanso kuwapatsa chiyembekezo.

Ndimakhala ndi mtendere wa mu mtima chifukwa ndimadziwa kuti Yehova ndi amene adzasinthe zinthu. Ndimakhulupirira kuti iye monga Mlengi sadzalekerera kuti anthu azizunza nyama ndi anthu anzawo mpaka kalekale komanso kuti awononge dziko lathu lokongolali. Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kukonza zinthu zonse zimene zawonongedwa padzikoli. (Yesaya 11:1-9) Ndimasangalala kwambiri kudziwa zinthu zimenezi komanso kuthandiza anthu kuti azikhulupirira zoti zimenezi zidzachitika. Panopa ndilibenso maganizo ofuna kusintha zinthu padzikoli.